Chifukwa Chake Ambiri Akukana Magazi
PACHIWERUZO chimene chinatchedwa kuti kusintha kwa zinthu, khothi la Ontario linapeza bungwe la Canadian Red Cross kukhala lolakwa chifukwa choyika anthu aŵiri magazi okhala nkachilombo ka HIV—onsewo anayikidwa magazi oipawo ochokera kwa munthu mmodzi. “Pamafunikira kuchitapo kanthu msanga ngati pali chinthu choopsa monga ngati miyoyo kukhala pangozi chifukwa cha magazi oipa,” anatero Justice Stephen Borins.
Mkati mwazaka za m’ma 1980, anthu 1,200 a ku Canada anatenga HIV ndipo kuwonjezera apo 12,000 anatenga hepatitis C—onsewo kuchokera m’magazi okhala ndi tizilomboto kapena mankhwala ena opangidwa ndi magazi. Kuti achepetse chiŵerengero cha anthu otenga matenda mwamtundu umenewu, opereka magazi akumawapima ndi kuwafufuza bwino kwambiri. Koma si opereka magazi onse amene amanena mwachilungamo za khalidwe lawo lakale lachiwerewere. Mwachitsanzo, kufufuza kochitidwa mu United States kunasonyeza kuti mmodzi mwa opereka magazi 50 sananene zinthu zina zomwe zikanampangitsa kutenga matenda, monga kugonana kwa amuna okhaokha kapena kugonana ndi hule.
Kuwonjezera apo pali mfundo yakuti si kwapafupi kupima magazi. Malinga ndi magazini ya New Scientist, “ngati munthu apereka magazi pasanathe milungu itatu atatenga kachilombo ka HIV, magaziwo sasonyeza kuti ali nkachilombo malinga nkupima kumene kulipo makono. Kunena za hepatitis C, pafunikira ‘papite kaye’ nthaŵi yoposa miyezi iŵiri.”
M’zaka za posachedwapa, pakhala kutsika kwakukulu kwa chiŵerengero cha anthu a ku Canada ofuna kupereka—kapena kuyikidwa—magazi. Wolemba nkhani Paul Schratz anati: “Popeza chidwi choti nkupereka magazi chikutsika mwa anthu, ndiponso pali kuwonjezereka kwa anthu amene sangapereke magazi nkomwe, tikuthokoza Mulungu chifukwa cha Mboni za Yehova zomwe zakhala patsogolo kutipangitsa kufufuza zinthu zina zomwe tingagwiritsire ntchito m’malo mwa magazi.”
Zodabwitsa nzakuti, The Toronto Star inati m’chaka china posachedwapa, anthu okwana 40 “m’zipatala za ku Canada ananama kuti ndi a Mboni za Yehova chifukwa chakuti sankafuna kuyikidwa magazi.” Kufufuza kumasonyeza kuti pafupifupi 90 peresenti ya anthu a ku Canada angakonde mankhwala ena m’malo mwa magazi. Motero kugwiritsira ntchito magazi masiku ano si nkhani yongokhudza zachipembedzo zokha.