Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 10/8 tsamba 7-10
  • Moyo Wotetezereka Kosatha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Moyo Wotetezereka Kosatha
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyambi Chotetezereka Chinawonongedwa
  • Zinthu Zauzimu Zikhale Patsogolo
  • “Pemphera kwa Mulungu Wako, Yehova”
  • Chilungamo, Bata ndi Chitetezo
  • Mtsogolo Mosungika Mmene Mungamupezere
    M’tsogolo Mosungika—M’mene Mungamupezere
  • Chisungiko Chenicheni—Tsopano Ndiponso Kosatha
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kufunafuna Moyo Wotetezereka
    Galamukani!—1998
  • N’chiyani Chingakuthandizeni Kuti Musamakhale Mwamantha?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 10/8 tsamba 7-10

Moyo Wotetezereka Kosatha

NGATI thupi lanu latentha, mwachidziŵikire mumamwa mbulu wamankhwala kuti muchepetse kuŵaŵa kwa mutu ndiponso mwina kuziziritsa thupi lanu ndi ayezi. Koma ngakhale kuti mbulu wamankhwala ndi ayeziyo zimapangitsa zizindikiro za matenda kuchepako, sizithetsa matenda. Ndipo ngati matenda anu ndi akulu, mumafunikira chithandizo cha dokotala.

Mtundu wa anthu ukudwala matenda osatha a kusoŵa chitetezo. Timachita bwino kuchitapo kanthu kuchepetsa zizindikiro za matendaŵa, koma amene angapereke mankhwala enieni ndi yekhayo amene angapime bwino kwambiri vuto lathu. Ndipo palibe angadziŵe mtundu wa anthu bwino kwambiri kuposa Mlengi wathu, Yehova Mulungu. Iye amadziŵa kuti moyo ulibe chitetezo chifukwa cha mavuto amene anabweretsedwa pa ife.

Chiyambi Chotetezereka Chinawonongedwa

Mawu a Mulungu amatiuza kuti Yehova analenga anthu aŵiri oyambawo angwiro ndipo anawaika iwo m’malo otetezereka. Iwo analibe nkhaŵa. Chimene Mulungu ankafuna nchakuti anthu akhale ndi moyo kwamuyaya m’paradaiso, ali otetezereka bwino. Malo awo anthu oyambawo anali ndi “mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya.” Onani kuti zofuna zawo zakuthupi zinasamaliridwa; ndipo zinali chonchonso ndi zofunikira pa malingaliro awo, popeza malo awo anatchedwa kuti a “mitengo yonse yokoma m’maso.” Mosakayikira zimenezi zimasonyeza kuti anthu aŵiri oyambawo anaikidwa m’malo mmene iwo anatsimikizira kuti munalibe zovuta, oti nkukhalamo ndi moyo popanda mavuto.—Genesis 2:9.

Adamu ndi Hava anakana ulamuliro wa Mulungu wachikondi, motero kuyambira pamenepo anayamba kukayikira zinthu, kukhala amantha ndi amanyazi, kudzimva olakwa, ndiponso kupanda chitetezo. Atakana Mulungu, Adamu anavomereza kuti ‘anaopa.’ Anthu oyambawo anabisala kuthaŵa Mlengi wawo wachikondi, amene zisanachitike izi anali naye paubwenzi wokondana kwambiri ndi wopindulitsa.—Genesis 3:1-5, 8-10.

Zofuna za Yehova zapoyambapo sizinasinthe. Baibulo limati Mlengi wathu ndi Mulungu wachikondi, amene adzapangitsa kuti mtundu wa anthu omvera ubwezeretse dziko kukhala paradaiso ndi kukhala motetezereka kosatha. Lonjezo limene linaperekedwa kupyolera mwa mneneri Yesaya lakuti: “Ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; . . . khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse.” (Yesaya 65:17, 18) M’dziko latsopano ndi miyamba yatsopano imeneyi mtumwi Petro anati: “M’menemo mukhalitsa chilungamo.”—2 Petro 3:13.

Kodi zimenezi zidzatheka bwanji? Kupyolera mwa boma limene Yehova adzakhazikitsa. Ilo ndiwo Ufumu umene Yesu Kristu anauza ophunzira ake kuti azipempherera kuti: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.

Ufumu wa Mulungu udzaloŵa m’malo maboma opangidwa ndi anthu ndipo mwachikondi udzachita chifuniro cha Mulungu padziko lonse. (Danieli 2:44) Kukayika, mantha, manyazi, kudzimva wolakwa, ndi kusoŵa chitetezo zimene zagwira mtundu wa anthu kuyambira masiku a Adamu zidzatha. Malinga ndi Baibulo, Ufumu umenewo wayandikira. Ngakhale tsopano, m’dziko lathu lino losadalirika, anthu amene amafuna Ufumu wa Mulungu amatetezerekako.

Zinthu Zauzimu Zikhale Patsogolo

Davide anali mtumiki wa Mulungu amene ankadziŵa mmene kuopsedwa kumakhalira ndi mmenenso nsautso imakhalira. Komabe Davide analemba, monga mmene zilili pa Masalmo 4:8: ‘Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.’ Yehova anapangitsa Davide kumadzimva wotetezereka, ngakhale kuti Davide nthaŵi zina anali ndi mavuto ambiri. Kodi pamenepa tingaphunzireponji? Kodi tingapeze bwanji chitetezo ngakhale m’dziko lino lopanda chitetezo?

Lingalirani za nkhani ya mu Genesis yonena za Adamu ndi Hava. Kodi ndi liti pamene analeka kukhala otetezereka? Pamene anangowononga ubwenzi wawo ndi Mlengi ndi kukana kukhala mogwirizana ndi chifuniro chake kwa mtundu wa anthu. Motero ngati tingasinthe zimenezi mwakudziyandikizitsa ndi kukhala ndi ubwenzi ndi Yehova ndi kuyesayesa kukhala mogwirizana ndi chifuniro chake, ngakhale tsopano tingathe kumakhala moyo wotetezerekapo kuposa mmene zingakhalire pachabe.

Kumdziŵa Yehova kupyolera mwa kuphunzira Baibulo kumatithandiza kuti timvetse tanthauzo la moyo. Ndi mwanjira yokhayo pamene timamvetsa kuti ndife ndani ndiponso chifukwa chake tili pano. Moyo wotetezereka ndi wotheka ngati timakonda Mulungu, kudziŵa chifuniro chake kwa mtundu wa anthu, ndi kumvetsetsa zimene tiyenera kuchita. Munthu wotchedwa Paul anazindikira zimenezo zaka zingapo zapitazo.

Paul anabadwa ndi kukulira pachilumba china pafupi ndi Germany. Chifukwa cha zimene makolo ake anakumana nazo nthaŵi ya Nkhondo Yadziko II, banja lawo linalibe chidwi ndi chipembedzo. Paul ananena zimene iye mwini ankachita ali wachinyamata: “Sindinkakhulupiriranso chilichonse ndipo sindinkalemekeza aliyense. Ndinkathetsa chisoni changa mwa kumwa moŵa, kumwa kwambiri kaŵiri kapena kanayi pamlungu. Moyo wanga unalibe chitetezo chilichonse.”

Ndiye kenaka Paul anakambirana ndi munthu wina wa Mboni za Yehova. Paul ankatsutsa kwambiri, koma panali chinthu chimodzi chimene Mboni inanena chomwe chinampangitsa kulingalira. “Palibe chimene chimachitika pachokha.” M’mawu ena, chilichonse chachilengedwe chimene timaona chili ndi Mlengi wake.

“Ndinalingalira zimenezo mobwerezabwereza, ndiye kenaka ndinavomereza.” Motero Paul anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo anafika pozindikira Yehova. Iye anavomereza kuti: “Kusiyapo makolo anga, Yehova anali munthu wapatsogolo m’moyo wanga amene anandichitira ine chilichonse.” Paul anabatizidwa monga wa Mboni mu 1977 ndipo anati: “Tsopano ndikudziŵa kuti chifuno cha moyo nchiyani. Ndimasangalala kumakhala mogwirizana ndi mmene Yehova amafunira. Ndimadzimva kukhala wotetezereka, popeza palibe chimene chingandichitikire kapena banja langa chimene Yehova sangathe kudzakonza mtsogolo.”

Kodi tingaphunzire chiyani pa zokumana nazo zake? Paul anathetsa kusatetezereka kwake—vuto la malingaliro—mwa kusumika maganizo ake osati pachuma koma pazinthu zauzimu. Anayambitsa ubwenzi ndi Mlengi. Mamiliyoni a Mboni za Yehova ali paubwenzi wotero. Ubwenziwo umawapatsa mphamvu mkati mwawo imene imawathandiza kuti akhale odzipereka kwathunthu pothandiza ena. Polalikira kwa anthu kunyumba zawo, Mboni za Yehova zimagwiritsira ntchito nthaŵi yawo kuthandiza anthu ena kuti apangitse miyoyo yawo kukhala yotetezereka mwa kusumika maganizo pa zinthu zauzimu. Koma Mboni zimachita zambiri kuposa pa kulalikira chabe.

“Pemphera kwa Mulungu Wako, Yehova”

M’July 1997 pamene Mtsinje wa Oder unasefukira m’malo ambiri kumpoto kwa Ulaya, Mboni za Yehova za ku Germany zinamva za vuto la anthu a m’dziko loyandikana nalo la Poland. Kodi nchiyani chimene iwo anachita? Mboni iliyonse yokhala mu mzinda wa Berlin ndi kunja kwake inasonyeza kuwolowa manja mwa kupereka modzifunira ndalama zoposa $116,000 m’masiku oŵerengeka chabe.

Mboni zodziŵa bwino ntchito yomanga zinayenda ulendo wa maola asanu ndi limodzi pagalimoto—pogwiritsira ntchito ndalama zawo—kuchokera ku Berlin kukafika kudera lozungulira Wroclaw, ku Poland. M’katauni kena, nyumba zambiri zinali zitawonongeka kwambiri. Nyumba ya banja la Mboni inali m’madzi akuya kukwana mamita 6. Mwana wawo wamkazi ankakonzekera kukwatiwa ndipo kuti azidzakhala m’nyumbayo ndi mwamuna wake. Kodi nchiyani chimafunika kuchita kukonza nyumbayo ndi kuthandiza banjalo, limene pafupifupi katundu wawo yense anali atawonongeka?

Pamene madziwo anaphwa, munthu woyandikana naye nyumba anafunsa monyodola kuti: “Bwanji osapemphera kwa Mulungu wanu, Yehova, muone ngati angakuthandizeni?” Munthu ameneyo anadabwa chotani nanga pamene tsiku lotsatira magalimoto ambiri ochokera ku Germany anapita kunyumba ya banja la Mbonilo! Gulu la anthu achilendo linatsika m’magalimotowo ndi kuyamba kukonza nyumbayo. Munthuyo anafunsa kuti, “Kodi ameneŵa ndani? Ndani akugula zida zokonzera nyumbayi?” Banja la Mbonilo linanena kuti amenewo anali abale awo auzimu ndi kuti alendowo ndiwo anali kugula zidazo. Anthu a m’tauniyo anaonerera modabwa pamene nyumbayo inali kukonzedwa. Mosayembekezereka, chikwaticho chinachitika tsiku limene anakonzalo.

Banja limeneli linazindikira kuti kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova zimene zili paubale wa m’maiko osiyanasiyana sikupindulitsa mwauzimu chabe komanso kumatetezera m’dziko lopanda chitetezoli. Iwo sindiwo okha amene anaona tsoka lotere. Kuzungulira dera lonse logweredwa tsokalo, nyumba zogona ndi Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova zinakonzedwa. Ndiponso anthu omwe si Mboni nawonso anathandizidwa. Anaŵakonzeranso zinthu zambiri panyumba zawo, chinthu chimene anayamikira kwambiri.

Chilungamo, Bata ndi Chitetezo

Pamene kutentha kwa thupi kuleka ndipo tachira, timayamikira kwambiri chotani nanga dokotala amene anatithandiza! Pamene matenda a kupanda chitetezo amene akuta mtundu wa anthu adzathetsedwa kwamuyaya—kupyolera mwa Ufumu wa Mulungu—tidzayamikira Mlengi wathu chotani nanga! Inde, iye ndiye amene amatilonjeza moyo wa “mtendere, bata ndi chitetezo ku nthaŵi zonse.” Ndi chinthu chabwino chotani nanga!—Yesaya 32:17, NW.

[Mawu Otsindika patsamba 10]

Tikhoza kuchepetsa vuto la m’malingaliro mwathu mwa kusumika maganizo athu osati pachuma koma pazinthu zauzimu

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Mulungu amalonjeza dziko latsopano mmene onse adzakhala motetezereka kosatha

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena