Kufunafuna Moyo Wotetezereka
CHITETEZO kwa anthu osiyanasiyana chimatanthauza zinthu zosiyanasiyana. Kwa wina, chitetezo ndi kukhala pantchito; kwa wina, ndi chuma; ndipo kwa wachitatu, chitetezo ndi pamene kulibe upandu. Kodi kwa inu chimatanthauza chinthu china?
Mulimonse mmene inu mumaganizira, mosakayika mumachitapo kanthu kuyesayesa kupangitsa moyo wanu kukhala wotetezereka monga mmene mumafunira. Talingalirani zimene anthu ku Ulaya akuchita kuti akhale otetezereka paokha.
Maphunziro Apamwamba
Malinga nkunena kwa Jacques Santer, pulezidenti wa European Commission, 20 peresenti ya achinyamata a m’maiko a m’bungwe la European Union ali paulova. Motero kwa achinyamata amenewo malingaliro awo ali pafunso limodzi lakuti, Kodi ndingapeze bwanji ntchito imene ingapangitse moyo wanga kukhala wotetezereka? Ambiri amalingalira kuti zimenezi zikhoza kutheka mwakukhala ndi maphunziro apamwamba, amene, malinga ndi The Sunday Times ya ku London inati, amapangitsa wophunzirayo “kukhala ndi mwayi wopeza ntchito mosavuta.”
Mwachitsanzo, ku Germany, “anthu amakonda maphunziro ndi masatifiketi apamwamba,” inatero Nassauische Neue Presse. Izi zimatero ngakhale kuti kuphunzira pa yunivesite m’dziko limenelo kumafuna ndalama zokwana pafupifupi $55,000 pa avareji.
Achinyamata amene amakonda maphunziro ndipo amene amafuna kudzakhala ndi ntchito yodalirika ayenera kuyamikiridwa. Ndipo amene amadziŵa ntchito inayake ndiponso ali ndi masatifiketi amakhala ndi mwayi wopezadi ntchito. Koma kodi maphunziro apamwamba nthaŵi zonse amapangitsa kupeza ntchito yodalirika? Wophunzira wina anati: “Ndinadziŵa kuyambira pachiyambi pomwe kuti maphunziro anga sadzandipangitsa kupeza ntchito yolongosoka ndipo idzakhala yosadalirika.” Zimene zinamchitikirazi si zachilendo. M’chaka china posachedwapa, chiŵerengero cha omwe anaphunzira pa yunivesite omwe anali paulova chinakwera kwambiri ku Germany.
Malinga ndi nyuzipepala ina, ku France, achinyamata amapita ku yunivesite chifukwa satifiketi imene amapeza ku sekondale sipindula chifukwa chosoŵa ntchito. Komabe, ophunzira ku yunivesite ambiri amadziŵa kuti pomaliza maphunziro awo, sikuti “zinthu zidzawayendera bwino konse ngakhale kuti adzakhala ndi digiri m’thumba.” The Independent inanena kuti ku Britain “maphunziro akupangitsa ophunzira ambiri kukhala opanikizika maganizo.” M’malo mothandiza achinyamata kuthetsa kusowa chitetezo komwe kulipo m’moyo, moyo wa payunivesite nthaŵi zina umapangitsa mavuto monga kupanikizika maganizo, nkhaŵa, ndi kudziona monga opanda pake.
Motero kuphunzira ntchito ina yabwino kungathandize kuti munthu apeze ntchito yodalirika mosavuta kuposa kukhala ndi digiri ya ku yunivesite.
Kodi Kukhala ndi Zinthu 10,000 Nkokwanira?
Ena amakhulupirira kuti chinsinsi cha moyo wotetezereka chagona pa kukhala ndi chuma. Izi zingaoneke ngati zoona, chifukwa ngati muli ndi ndalama zambiri ku banki zingathe kudzakuthandizani panthaŵi yamavuto. Baibulo limati “ndalama zitchinjiriza.” (Mlaliki 7:12) Komabe, kodi kuwonjezera chuma kumapangitsa kuti mukhale wotetezereka kwambiri?
Osati kwenikweni. Lingalirani mmene chuma chawonjezerekera m’zaka 50 zapita. Pamapeto pa Nkhondo Yadziko II, anthu ambiri a ku Germany pafupifupi analibe kalikonse. Lero, malinga ndi nyuzipepala ya ku Germany, munthu wa ku Germany ali ndi zinthu 10,000. Ngati zimene amanena akatswiri odziŵa zachuma nzoona, mbadwo ukubwerawo udzakhala ndi zinthu zambiri. Kodi kuunjika chuma kumeneku kumapangitsa moyo kukhala wotetezereka kwambiri? Ayi. Ku Germany ofufuza anavumbula kuti anthu aŵiri mwa atatu amaona moyo kukhala wosatetezereka kuposa mmene unaliri zaka 20 kapena 30 zapitazo. Choncho kuwonjezereka kwa chuma sikunapangitse anthu kudzimva otetezereka.
Izi nzomveka chifukwa malinga nzimene tanena m’nkhani yoyamba, kudzimva wosatetezereka kuli vuto lokhudza malingaliro. Motero vuto la malingaliro silingathetsedweretu ndi chuma. Nzoona kuti chuma chimatetezera kuumphaŵi ndipo chimathandiza panthaŵi ya mavuto. Koma nthaŵi zina, kukhala ndi ndalama zambiri kumabweretsa mavuto osasiyana nkukhala nazo pang’ono.
Choncho, kuona zinthu mwanzeru pankhani ya chuma kudzatithandiza kukumbukira kuti pamene chuma chingakhale dalitso, sindicho chinthu chofunika kwambiri kuti tikhale ndi moyo wotetezereka. Pamene anali padziko lapansi, Yesu Kristu analimbikitsa ophunzira ake mwakunena kuti: “Chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” (Luka 12:15) Kuti adzimve wotetezereka kwambiri m’moyo, munthu afunikira zambiri kuposa chuma chokha.
Kwa anthu akuluakulu, zomwe ali nazo amazikonda osati kwenikweni chifukwa cha mtengo wake koma chifukwa cha kungodzimva kuti basi ali nazo. Chimene chimadandaulitsa kwambiri achikulire kuposa chuma ndi kuopa kuchitidwa upandu.
Chenjerani!
Kabuku kakuti Practical Ways to Crack Crime, kofalitsidwa ku Britain, kanati: “Upandu . . . wakhala vuto lomapitirapitira patsogolo kuzungulira dziko lonse m’zaka 30 zapitazo.” Apolisi akugwira ntchito kwambiri. Kodi anthu ena amakhala motani pali zotero?
Chitetezo cha munthu chimayambira panyumba. Mwachitsanzo ku Switzerland, katswiri wina wolemba mapulani a nyumba anaphunzira kupanga nyumba zoti akuba sangathyole zokhala ndi maloko amphamvu, zitseko zolimba kwambiri, ndi mawindo otchinga ndi zitsulo. Eni nyumba zimenezi amaona mwambi uwu kukhala woona: “Nyumba yanga ndi ngaka yanga.” Malinga ndi magazini ya Focus, nyumba zimenezi ndi zokwera mtengo, komabe amazifuna ndi anthu ambiri.
Kuti awonjezere chitetezo m’nyumba ndi kunja komwe, anthu ena m’maiko ena apanga magulu olondera. Anthu a m’madera ena amachita zoposa apo, amalipira a kampani yolondera malo kuti aziyendera dera lawo panthaŵi imene agwirizana. Anthu ambiri amaona kuti si bwino kuyenda okha usiku mumsewu wosayenda anthu ambiri. Ndipo makolo, amene amadera nkhaŵa za ana awo, angachitepo zambiri kuti atetezere ana awo. Lingalirani mfundo zopezeka m’bokosi patsamba lino.
Koma si aliyense amene angathe kumangitsa nyumba yoti akuba sangathe kuthyola. Komanso, magulu olondera ndi makampani omayendera malo sangachepetse upandu; iwo akhoza kungopangitsa kuti upanduwo ulekeke m’deralo ndi kuyamba kuchitika kudera limene kulibe chitetezo. Motero upandu udakali chopinga pa kutetezereka kwa munthu. Kuti miyoyo yathu ikhale yotetezereka, pafunika zambiri koposa kuyesayesa kuthetsa upandu.
Thetsani Nthenda—Osati Zizindikiro za Matenda
Tonse mwachibadwa timalakalaka moyo wotetezereka, ndipo timachita bwino kuchitapo kanthu malinga nzomwe tingathe kuchita kuti zimenezo zitheke. Koma upandu, ulova, ndi zina zonse zimene zimapangitsa moyo wathu kukhala wosatetezereka zili zizindikiro chabe za zovuta zimene zimakhudza mtundu wa anthu. Kuti tithetse vutolo, kuli bwino kulimbana ndi chopangitsacho, osati zizindikiro chabe.
Kodi nchiyani kwenikweni chimapangitsa miyoyo yathu kukhala yosatetezereka? Kodi tingachithetse bwanji kuti tithetseretu kwamuyaya kusowa chitetezo? Izi tizilongosola m’nkhani yotsatira.
[Bokosi patsamba 6]
Njira Zotetezera Ana Aang’ono
Chifukwa chakuti kaŵirikaŵiri ana akuvutitsidwa, kubedwa, ndi kuphedwa, makolo ambiri apeza kuti nkothandiza kuphunzitsa ana awo kuchita zotsatirazi:
1. Kunena kuti toto—mwamphamvu—kuuza munthu aliyense amene akufuna kuchita chinthu china chimene iwo akuona kuti nchoipa.
2. Kukana kuti munthu wina awagwire ziŵalo zina pokhapokha—ngati ndi dokotala kapena nesi—kholo likhalepo.
3. Kuthaŵa, kukuwa, kupuluputa, kapena kupempha chithandizo kwa munthu wina wamkulu amene ali pafupi ngati aona kuti ali pangozi.
4. Kuuza makolo zachochitika china chilichonse kapena makambitsirano alionse amene sanasangalatse mwanayo.
5. Kukana zakuti kanthu kena asakanene kwa makolo.
Ndipo mfundo yomaliza: makolo angamachite bwino kusankha mochenjera munthu aliyense amene amusiyire ana.
[Zithunzi patsamba 5]
Kuti miyoyo yathu ikhale yotetezereka, tifunikira zambiri kuposa maphunziro, chuma, kapena kuyesayesa kwakhama kulikonse kuthetsa upandu