N’zotheka Kukhala Ndi Tsogolo Labwino
KODI MUKUGANIZA KUTI N’CHIYANI CHINGAKUTHANDIZENI KUTI MUKHALE NDI TSOGOLO LABWINO? KODI NDI:
Maphunziro akuyunivesite?
Chuma?
Kungokhala munthu wabwino?
Kapena zinthu zina?
Malemba Opatulika amati:
“Dziwa nzeru kuti upindule. Ukazipeza, udzakhala ndi tsogolo labwino.”—MIYAMBO 24:14.
M’Malemba Opatulika mungapezemo mawu anzeru omwe angakuthandizeni kukhala ndi tsogolo labwino.