Kodi Nchifukwa Chiyani Chikondi cha Anansi Chikuzirala?
ANTHU mamiliyoni ambiri amaona kuti alibe chithandizo, ngamantha, ndipo ngopanda chimwemwe, osoŵa chochita. Wina anadandaula kuti: “Ndimadya ndekha, ndimayenda ndekha, ndimagona ndekha ndipo ndimalankhula ndekha.” Ndi anthu ochepa amene amaipeza nthaŵi yosonyeza chikondi anzawo osoŵa chikondi.
Mayi wina wabizinesi wopuma pantchito anati: ‘Madzulo ena mkazi wina wamasiye yemwe ndi mnansi wanga anandigogodera nkundiuza kuti anali kusungulumwa. Ndinamuuza mwaulemu komabe momdula, kuti ndinalibe nthaŵi. Anandipepesa kuti wandivutitsa ndiye anabwerera.’
Ndiye mayiyo anatinso: ‘Ndinadzitama kuti sindinalole munthu wotopetsa ngati ameneyo kundiwonongera nthaŵi. Tsiku linalo bwenzi langa lina linandiimbira foni nkundifunsa ngati ndinkadziŵa mkazi wina wokhala m’nyumba yosanja yomwenso ndinkakhala, yemwe anadzipha usiku wapita. Mwinatu mwadziŵa kale, analidi mayi yemweyo anandigogoderayo.’ Kenaka, mayi wabizinesiyo ananena kuti anaphunzirapo “phunziro loŵaŵa.”
Tonsefe timadziŵa kuti makanda osakondedwa amafa. Achikulirenso angafe chimodzimodzi ngati samakondedwa. Mtsikana wina wokongola wazaka 15 analemba m’kalata yake asanadziphe, kuti: “Chikondi ndicho kusasungulumwanso.”
Tsoka Lamakono
Zaka zingapo zapitazo, magazini ya Newsweek ponena za mmene anthu amadera anzawo a mtundu wina, inati: “Mawu amene sanali kuchoka pakamwa chaka chonse ayenera kuti anali akuti: ‘Uzimuda mnansi wako.’” Pankhondo ya ku Bosnia ndi ku Herzegovina, dziko lomwe kale linali mbali ya Yugoslavia, anthu oposa miliyoni imodzi anathaŵa kwawo, ndipo anthu ena zikwizikwi anaphedwa. Anawapha ndani? Mtsikana wina yemwe anathaŵa pamudzi wake anati: “Ndi anansi athu. Tinkawadziŵa.”
Mayi wina, ponena za Ahutu ndi Atutsi 3,000 okhala m’mudzi wa Ruganda, anati: “Tinkakhala pamodzi mumtendere.” New York Times inati: “Nkhani ya mudzi uwu ndiyo nkhani ya Rwanda: Ahutu ndi Atutsi akumakhalira pamodzi, kukwatirana, popanda kusamala kapenanso kudziŵa kuti ndani amene anali Mhutu ndipo ndani amene anali Mtutsi. Ndiyeno panabuka kanthu kena,” ndipo “kuphanako kunayamba.”
Nchimodzimodzinso Ayuda ndi Aluya ku Israel, amakhala pamodzi, koma ambiri amadana. M’zaka zonse zino za zana la 20, mavuto ngati amenewo abukapo ku Northern Ireland, ku India ndi ku Pakistan, ku Malaysia, ndi ku Indonesia, ndiponso pakati pamafuko osiyanasiyana a ku United States—Inde, zikuchitika padziko lonse lapansi pamene tikukhala.
Mwina wina angasimbebe zitsanzo zambiri za anthu odana ndi anzawo amafuko ena ndi enanso akuda anzawo achipembedzo china. M’mbiri yonse yakale, dziko silinakhalepo lopanda chikondi monga mmene zikuchitikiramu.
Kodi Mlandu Ngwandani?
Anthu amachita kuphunzitsidwa kuda ena, monganso mmene amaphunzitsidwira kukonda ena. Nyimbo ina yotchuka imati ana “amaphunzitsidwa mosamalitsa nthaŵi isanathe, asanakwanitse zaka zisanu ndi chimodzi kapena zaka zisanu ndi ziŵiri kapena zaka zisanu ndi zitatu, kuda anthu onse amene achibale awo amada.” Makamaka lero mpamene anthu akuphunzitsidwa kuda anzawo. Matchalitchi kwenikweni ndiwo amene akulephera kuphunzitsa anthu awo kukondana.
Nyuzipepala yotchedwa Le Monde ya ku France, inati: “Kodi ndi motani mmene munthu angapeŵere kuganiza kuti Atutsi ndi Ahutu amene akumenyana ku Burundi ndi ku Rwanda anaphunzitsidwa ndi amishonale achikristu amodzimodziwo ndi kupita kumatchalitchi amodzimodzi?” Ndithudi, malinga ndi kunena kwa National Catholic Reporter, Mwa ‘anthu onse a ku Rwanda, 70% ndi Akatolika.’
Cha kuchiyambi kwa zaka za zana lino, maiko a ku Eastern Europe anasanduka maiko a chikomyunizimu cha anthu osakhulupirira Mulungu. Chifukwa? Mu 1960, mkulu woona za chipembedzo pa yunivesite ku Prague, Czechoslovakia, anati: “Ifeyo, Akristu tokhafe, ndife amene tinayambitsa Chikomyunizimu. . . . Kumbukirani kuti kale Akomyunisti anali Akristu. Ngati iwo samakhulupirira Mulungu wachilungamo, ndi mlandu wandani umenewo?”
Taganizani zimene matchalitchi anachita m’Nkhondo Yadziko I. Mkulu wankhondo wa ku Britain, Frank Crozier, ponena za nkhondoyo anati: “Matchalitchi achikristu ndiwo osonkhezera kukhetsa mwazi koposa omwe tili nawo, ndipo tinawagwiritsira ntchito monga momwe tinafunira.” Kenaka, Nkhondo Yadziko II itatha, magazini ya The New York Times inati: “Kumbuyoku akuluakulu achikatolika akumaloko nthaŵi zonse anali kuchirikiza nkhondo za maiko awo, akumadalitsa magulu ankhondo ndi kupereka mapemphero kaamba ka chipambano, pamene kuli kwakuti gulu lina lamabishopu la mbali ina linapemphera poyera kuti agonjetsedwe.”
Komabe, Yesu Kristu anasonyeza chikondi m’zochita zake zonse, ndipo mtumwi Paulo analemba kuti: “Wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake.” (1 Atesalonika 4:9) Wolemba nkhani za m’nyuzipepala yotchedwa Vancouver Sun, anati: “Akristu oona ali abale ndi alongo mwa Yesu Kristu. Iwo sakayesa konse, ngakhale mpang’ono pomwe kuvulazana mwadala.”
Nzachionekere kuti matchalitchi ndiwo ali ndi mlandu waukulu wakudanitsa anthu. Nkhani ina yofalitsidwa m’magazini yotchedwa India Today, inati: “Upandu woipitsitsa wakhala ukuchitidwa m’dzina la chipembedzo.” Komabe, pali chifukwa chachikulu chimene mbadwo wathu uno ulili wopanda chifundo ndi wosasamala ena.
Chifukwa Chake Chikondi Chazirala
Mlengi wathu amayankha. Mawu ake, Baibulo, limati nthaŵi imene tikukhalamoyi ndiyo “masiku otsiriza.” Ulosi wa Baibulo umati nthaŵi ino ndiyo imene anthu adzakhala “opanda chikondi chachibadwidwe.” Ponena za “nthaŵi zoŵaŵitsa,” zimene zikutchedwanso m’Malemba kuti “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano,” Yesu Kristu ananeneratu kuti chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala.”—2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:3, 12.
Chotero, kupanda chikondi kwa anthu kumene kulipoku ndiwo umboni wakuti tikukhala m’masiku otsiriza a dzikoli. Komanso chosangalatsa nchakuti zimatanthauzanso kuti dziko la anthu osapembedzali posachedwapa lidzaloŵedwa m’malo ndi dziko latsopano lolungama limene lidzalamulidwa mwa chikondi.—Mateyu 24:3-14; 2 Petro 3:7, 13.
Koma kodi tingakhulupiriredi kuti zinthu zingasinthe mpaka pamenepo—kuti tidzakhoza kukhala padziko ndipo anthu onse namakondana namakhala pamodzi mumtendere?