Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 11/8 tsamba 16-19
  • Pamene Anthu Onse Adzakhala Okondana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Anthu Onse Adzakhala Okondana
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Moyo m’Dziko Latsopano Lolungama
  • Kuyenerera Kukhala Moyo Kosatha
  • Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere
    Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere
  • Pambuyo pa Harmagedo, Dziko Lapansi Laparadaiso
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kukhala ndi Moyo Kosatha Siloto Chabe
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • “Monga Kumwamba Chomwecho Pansi Pano”
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 11/8 tsamba 16-19

Pamene Anthu Onse Adzakhala Okondana

PAULALIKI wake wa pa Phiri, Yesu Kristu ananena za nthaŵi imene anthu onse adzakhala okondana. M’mawu ake oyamba, anatenga mawu a Salmo la 37, akumati: “Odala ngofatsa: chifukwa adzalandira dziko lapansi.” Salmo la Baibulo limenelo limafotokozanso mmene chinthu chodabwitsacho chidzachitikira, pomati: “Ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekezera Yehova, iwoŵa adzalandira dziko lapansi.”—Salmo 37:9.

Kumenekotu kudzakhala kusintha kwakukulu—anthu onse oipa atachotsedwa padziko lapansi nkungotsala anthu amene amakondana! Kodi zimenezo zingachitikedi bwanji? Yesu, pa Ulaliki wake wotchukawo, anasonyeza mmene zimenezo zidzachitikira pamene anatiphunzitsa kupemphera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Taonani kumene kufuna kwa Mulungu kudzachitidwira. Osati chabe kumwamba. Nkhani ina m’magazini yotchedwa The Christian Century, inanena monenetsa kuti: “Timapemphera kuti, kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”

Chabwino, nangano Ufumu wa Mulungu umene Yesu anatiphunzitsa kuupempherera nchiyani? Mwachionekere, umenewo uli boma lenileni, lolamulira kumwamba. Nchifukwa chake limatchedwa “Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 10:7) Yemwe wasankhidwa kuti akhale Wolamulira mu Ufumuwo, kapena m’bomalo, ndiye Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu.

Kale kwambiri Yesu asanabadwe ndi Mariya, mneneri wa Yehova Yesaya ananeneratu za chochitika chozizwitsa chimenecho ndi zimenenso zidzachitika potsirizira pake, akumati: “Kwa ife mwana wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo boma lidzakhala papheŵa lake: ndipo dzina lake adzamutcha Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuenjezera boma lake ndi za mtendere sizidzatha.” (Yesaya 9:6, 7, AS) Yesu ataphedwa ndi kuukitsidwanso, anakakhala ndi Atate wake kumwamba, namadikira kuti amlamule kuyamba kulamulira monga Mfumu.—Salmo 110:1, 2; Ahebri 10:12, 13; Chivumbulutso 11:15.

Ndiyeno potsirizira nchiyani chidzachitika padziko lodzala udanili? Onani mmene Baibulo likuyankhira funsolo. Mneneri wa Mulungu, Danieli, ananeneratu kuti: “Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.

Mwachionekere, ulosi wa Baibulo umenewu ukunena za mtsogolo kuti zochita za anthu zidzasintha kwambiri. Dongosolo lazinthu lonseli, limene likuphatikizapo anthu a dzikoli amene amakana mouma khosi kugonjera ulamuliro wa Mulungu, adzachotsedwa padzikoli! Taganizani zimene zidzaloŵa m’malo mwake.

Moyo m’Dziko Latsopano Lolungama

Dziko lino litatha, padzakhala opulumuka. Baibulo limafotokoza kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.” (1 Yohane 2:17) Inde, amene akuchita chifuniro cha Mulungu adzapulumuka nkuloŵa m’dziko latsopano, monga mmene Nowa ndi banja lake anapulumukira pamene dziko lawo linawonongedwa. Mtumwi Petro analemba kuti: ‘Monga mwa lonjezano la [Mulungu] tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.’—2 Petro 3:5-7, 11-13.

Ponena za nthaŵi imene boma lokha lolamulira lidzakhala Ufumu wa Mulungu, Baibulo likulonjeza kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Anthu olungama adzakondwera ndi moyo padziko lapansi loyeretsedwa. Imeneyotu ndiye idzakhala nthaŵi yaulemerero zedi! Ngati simunaonebe madalitso amene Baibulo likufotokoza pamasamba am’mbuyo aja, tawaoneni.

Kodi sizikusangalatsa mtima wanu kudziŵa kuti Mlengi wathu akulonjeza zinthu zodabwitsa ngati zimenezi kuchitira anthu amene amamlambira? Ndithudi, zimenezo nzimene Mulungu anali kufuna pamene analenga anthu aŵiri oyamba nkuwaika m’paradaiso wa padziko lapansi! Tamvani zimene Mulungu anawauza: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.”—Genesis 1:27, 28.

Adamu ndi Hava anayenera kubala ana, ndipo pamene anawo azidzakula, anayenera kugwira nawo ntchito yosangalatsa yosamalira Paradaiso wa padziko lapansi. Taganizani mmene kukanakhalira kosangalatsa kufutukula malire a munda wa Edene pamene anthu anamka akumachuluka! Nzachionekere kuti nzimenedi Mulungu anafuna kuti dziko lonseli likhale paradaiso. Kodi chifuno chimenecho adzachikwaniritsa? Tingadalire kuti adzachikwaniritsadi, chifukwa Mawu a Mulungu mwiniyo amatero! Analonjeza kuti: “Ndanena, . . . ndidzachichitanso.”—Yesaya 46:11; 55:11.

Kodi mungakondwere kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso wa padziko lapansi amene malemba afotokoza mwa zithunzi zili pamasamba am’mbuyowo? Aliyense angadziŵe kuti si anthu onse amene adzaloledwa kukhala mmenemo. Pali zofunika zake. Nanga zimenezo nziti?

Kuyenerera Kukhala Moyo Kosatha

Choyamba, amene akufuna kukhala m’dziko latsopano la Mulungu ayenera kuphunzira kukondana, monga mmene Mulungu amatiphunzitsira. Baibulo limati: “Wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake.” (1 Atesalonika 4:9) Kodi Mulungu amatiphunzitsa bwanji?

Makamaka mwa Mawu ake olembedwa, Baibulo. Zimenezo zikutanthauza kuti, kuti tikhale moyo kosatha, tiyenera kumvera zimene Mulungu amatiphunzitsa m’Baibulo. Wophunzira Baibulo wina wa ku Mmaŵa anati: “Ndikudikira nthaŵi imene anthu onse adzakhala ataphunzira kukondana, monga momwe Baibulo limalonjezera.”

Yesu, popemphera kwa Atate wake, anatchula chinthu chofunika kuchita. Anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Brosha la masamba 32 lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? lingakuthandizeni kupeza chidziŵitso chimenechi. Mungapeze kope lake mwa kulemba pakabokosi kali patsamba 32 ndi kukatumiza ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, kapena ku adiresi ina yoyenera patsamba 5.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 16-18]

Zimene Mulungu Akulonjeza

Ubale Wachikondi Padziko Lonse

“Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”—Machitidwe 10:34, 35.

Palibenso Upandu Kapena Nkhondo

“Koma oipa adzalikhidwa m’dziko.”—Miyambo 2:22.

“[Mulungu] aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.”—Salmo 46:9.

Zinthu Zochuluka Zabwino Zakudya

“M’dzikomo mudzakhala dzinthu zochuluka pamwamba pa mapiri.”—Salmo 72:16.

Mtendere Pakati pa Anthu ndi Nyama

“Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; . . . ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera.”—Yesaya 11:6.

Matenda, Ukalamba, ndi Imfa Zidzachotsedwa

“[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.

Akufa Okondedwa Adzaukitsidwa Padziko Lapansi

‘Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu [a Yesu], nadzatuluka.’—Yohane 5:28, 29.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena