Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pe mutu 1 tsamba 7-15
  • Kukhala ndi Moyo Kosatha Siloto Chabe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhala ndi Moyo Kosatha Siloto Chabe
  • Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Tingakhulupirire
  • Chikhumbo cha Kukhala ndi Moyo—Kuti?
  • Mtundu wa Moyo Umene Mukufuna
  • Madalitso Abwino Kwambiri Ayandikira
  • Ungathe Kukhala M’dziko Latsopano la Mulungu Lamtendere
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Tingakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kodi Chifuno cha Mulungu cha Dziko Lapansi N’chiyani?
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere
    Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
pe mutu 1 tsamba 7-15

Mutu 1

Kukhala ndi Moyo Kosatha Siloto Chabe

1, 2. Kodi nchifukwa ninji kuli kovuta kukhulupirira kuti anthu angathe kukhala ndi moyo kosatha m’chimwemwe padziko lapansi?

CHIMWEMWE padziko lapansi—sichimawonekera kukhala chothekera kukhala nacho ngakhale kwakanthawi. Kudwala, kukalamba, njala ndi upandu—kutchula mavuto owerengeka chabe—kawirikawiri zimapangitsa moyo kukhala wosakondweretsa. Motero, munganene kuti, kulankhula za kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso padziko lapansi ndiko kusafuna kuwona chowonadi. Mungalingalire kuti ndikutaya nthawi kukulankhula, kuti kukhala ndi moyo kosatha ndiko loto chabe.

2 Mosakayikira anthu ochuluka angavomerezane nanu. Motero, pamenepa, kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikiza kwambiri kuti inu mungathe kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso padziko lapansi? Kodi nchifukwa ninji tingakhulupirire kuti moyo wosatha suli loto chabe?

Chifukwa Chake Tingakhulupirire

3. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Mulungu amafuna kuti anthu akhale okondwa padziko lapansi?

3 Tingakhulupirire chifukwa chakuti Wolamulira Wamkulu, Mulungu Wamphanvuyonse, anakonza dziko lapansi lokhala ndi chirichonse chofunika kukhutiritsa zimene tikufuna. Iye anapanga dziko lapansi lotiyenereradi! Ndipo iye analenga mwamuna ndi mkazi m’njira yabwino koposa yakuti iwo asangalale ndi moyo mokwanira m’malo awo okhala apadziko lapansi ano—kosatha. —Salmo 115:16

4. Kodi nchiyani chimene asayansi adziwa ponena za thupi lamunthu chimene chimasonyeza kuti linapangidwa kuti likhale ndi moyo kosatha?

4 Asayansi kwa nthawi yaitali adziwa za mphamvu ya thupi lamunthu yodzibwezeretsa. Mwa njira yodabwitsa maselo athupi mwina amabwezeretsedwa kapena kukonzedwa, monga momwe kufunikako kungakhalire. Ndipo kumawonekera kuti njira yodzibwezeretsa imeneyi iyenera kupitirizabe kosatha. Koma siikutero, ndipo kameneka ndikanthu kena kamene asayansi sangakafotokoze. Iwo sakuzindikirabe mokwanira chifukwa chake anthu amakalamba. Iwo amati, m’mikhalidwe yabwino, anthu ayenera kukhala okhoza kukhala ndi moyo kosatha.—Salmo 139:14

5. Kodi Baibulo limanenanji ponena za chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi?

5 Komabe Kodi nchifunodi cha Mulungu kuti anthu akhale ndi moyo mosangalala padziko lapansi kosatha? Ngati chiridi, pamenepo moyo wosatha suli cholakalaka kapena loto chabe—ngwotsimikizirika kudza! Kodi Baibulo, bukhu limene limasimba zifuno za Mulungu, limanenanji za nkhaniyo? Limatcha Mulungu “amene anaumba dziko lapansi, nalipanga;” ndipo limatinso: “Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu.”—Yesaya 45:18.

6. (a) Kodi mikhalidwe padziko lapansi lerolino njotani? (b) Kodi umu ndimo mmene Mulungu akufunira?

6 Kodi kukuwonekera kwa inu kuti dziko lapansi tsopano lakhalidwa m’njira imene Mulungu anafunira? Zowona, anthu alinkukhala pafupifupi m’mbali zonse za dziko lapansi. Koma kodi iwo akukhala limodzi mosangalala monga banja logwirizana, m’njira yabwino imene Mlengi wawo anawafunira? Lerolino dziko nlogawanika. Pali udani. Pali upandu. Pali nkhondo. Mamiliyoni ambiri a anthu nganjala ndi odwala. Ena ali ndi nkhawa zatsiku ndi tsiku ponena za nyumba, ntchito ndi kukwera mitengo. Ndipo palibe zirizonse za zinthu zimenezi zimapereka ulemu kwa Mulungu. Pamenepa, mwachiwonekere, dziko lapansi silirinkukhalidwa m’njira imene Mulungu Wamphamvuyonse anafunira poyambirira.

7. Kodi chifuno cha Mulungu chinali chotani kaamba ka dziko lapansi pamene analenga anthu awiri oyamba?

7 Atalenga mwamuna ndi mkazi oyambawo, Mulungu anawaika m’paradaiso wapadziko lapansi. Iye anafuna kuti iwo asangalale ndi moyo padziko lapansi kosatha. Chifuno chake kwa iwo chinali kufutukulira paradaiso wawo padziko lonse lapansi. Chimenechi chikusonyezedwa ndi zilangizo zake kwa iwo: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” (Genesis 1:28) Inde, chifuno cha Mulungu chinali, m’kupita kwa nthawi, kuchititsa dziko lonse lapansi kulamuliridwa ndi banja laanthu lolungama lonse lokhala pamodzi mu mtendere ndi chimwemwe.

8. Ngakhale kuli kwakuti anthu awiriwo sanamvere Mulungu, kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira kuti chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi sichinasinthe?

8 Ngakhale kuli kwakuti mwamuna ndi mkazi oyambawo sanamvere Mulungu, motero akumadzisonyeza kukhala osayenerera kukhala ndi moyo kosatha, chifuno choyambirira cha Mulungu sichinasinthe. Chiyenera kukwaniritsidwa! (Yesaya 55:11) Baibulo limalonjeza kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha. (Salmo 37:29) Kawirikawiri Baibulo limasimba makonzedwe a Mulungu a kupatsa anthu amene akumtumikira moyo wosatha. —Yohane 3:14-16, 36; Yesaya 25:8; Chivumbulutso 21:3,4.

Chikhumbo cha Kukhala ndi Moyo—Kuti?

9. (a) Kodi anthu amakhala ndi chikhumbo chotani mwachibadwa? (b) Kodi Baibulo limatanthauzanji pamene limati ‘Mulungu waika umuyaya m’maganizo mwawo’?

9 Tingakhaledi okondwa kuti nchifuno cha Mulungu kuti tikhale ndi moyo kosatha. Pakuti taganizani: Ngati munafunikira kusankha, kodi ndi pa deti liti limene mungasankhe kufa? Simungasankhe lirilonse, kodi mungatero? Inu simukufuna kufa, ndipo chimodzimodzinso munthu wina aliyense wabwino amene ali ndi thanzi pang’ono. Mulungu anatipanga ndi chikhumbo cha kukhala ndi moyo, osati chikhumbo cha kufa. Ponena za mmene Mulungu anapangira anthu, Baibulo limati: “Iye waikadi umuyaya m’maganizo mwawo.” (Mlaliki 3:11, Byington) Kodi zimenezi zikutanthauzanji? Zikutanthauza kuti anthu mwachibadwa amafuna kukhalabe ndi moyo, osafa. Chifukwa cha chikhumbo cha mtsongolo mosatha chimenechi, anthu afunafuna kwanthawi yaitali njira yokhalira osakalamba kosatha.

10. (a) Kodi nkuti kumene munthu mwachibadwa amakhumba kukhala ndi moyo kosatha? (b) Kodi nchifukwa ninji tingakhale ndi chidaliro chakuti Mulungu adzatheketsa kuti tikhale ndi moyo kosatha padziko lapansi?

10 Kodi nkuti kumene anthu mwachibadwa amafuna kukhala ndi moyo kosatha? Ndiko kumene iwo azolowera kukhala ndi moyo, padziko lapansi pano. Munthu anapangidwira dziko lapansi, ndi dziko lapansi munthu. (Genesis 2:8, 9, 15) Baibulo limati: “[Mulungu] anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthawi zonse.” (Salmo 104:5) Popeza kuti dziko lapansi linapangidwira kuti likhale kosatha, pamenepo munthu ayeneranso kukhala ndi moyo kosatha. Ndithudi Mulungu wachikondi sakanalenga anthu okhala ndi chikhumbo cha kukhala ndi moyo kosatha ndiyeno nkusapanga kukhala kothekera kwa iwo kukwaniritsa chikhumbo chimenecho! —1 Yohane 4:8; Salmo 133:3.

Mtundu wa Moyo Umene Mukufuna

11. Kodi nchiyani chimene Baibulo limanena kosonyeza kuti anthu angathe kukhala ndi moyo kosatha m’nthanzi langwiro?

11 Yang’anani patsamba lotsatirapoli. Kodi anthu amenewa ali ndi moyo wamtundu wanji? Kodi mungafune kukhala mmodzi wa iwo? Aha, inde, mukutero! Wonani mmene iwo akuwonekerera athanzi ndi achinyamata! Ngati mukanauzidwa kuti anthu amenewa anakhala kale ndi moyo zaka zikwi zambiri, kodi mukanakhulupirira? Baibulo limatiuza kuti nkhalamba zidzasanduka anyamata kachiwiri, odwala adzachiritsidwa ndipo opunduka, akhungu, ogontha ndi mbewewe matenda awo onse adzachiritsidwa. Pamene anali padziko lapansi Yesu Kristu anachita zozizwitsa zambiri mwa kuchiza anthu odwala. Mwa kuchita zimenezi iye anali kusonyeza mmene, m’nthawi yosangalatsa yoyandikira imeneyi, onse amene akukhala ndi moyo adzabwezeretsedwera kuthanzi langwiro. —Yobu 33:25; Yesaya 33:24; 35:5,6; Mateyu 15:30,31.

12. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene tikuwona m’zithunzithuzi zino?

12 Wonani mmene malo okhala amunda wamaluwa okongola amenewa aliri! Monga momwe Kristu analonjezera, alidi paradaiso, wolingana ndi uja wotayidwa ndi mwamuna ndi mkazi oyamba osamverawo. (Luka 23:43) Ndipo wonani mtendere ndi chigwirizano zimene ziripo. Anthu a mitundu yonse—akuda, oyera ndi achikasu—akukhala monga banja limodzi. Ngakhale zinyama nzamtendere. Wonani mwana akusewera ndi mkangoyo. Koma palibe chochititsa mantha. Ponena za zimenezi Mlengi amati: “Nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera. . . . Ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe. Ndipo mwana wakuyamwa adzasewera pauna wa mamba.”—Yesaya 11:6-9.

13. Kodi nchiyani chimene chidzakhala palibe padziko lapansi pamene zifuno za Mulungu zikwaniritsidwa?

13 M’paradaiso amene Mulungu akulinganizira anthu, mudzakhala chifukwa chirichonse chokhalira wokondwa. Dziko lapansi lidzatulutsa zinthu zabwino zakudya zochuluka. Palibe munthu adzakhalanso ndi njala. (Salmo 72:16; 67:6) Nkhondo, upandu, chiwawa, ngakhale udani ndi dyera, zidzakhala zinthu za m’nthawi yapita. Inde, izo zidzachoka kosatha! (Salmo 46:8, 9; 37:9-11) Kodi mukukhulupirira kuti zonsezi nzotheka?

14. Kodi nchiyani chimene chikukukhulupiriritsani kuti Mulungu adzachotsa kuvutika?

14 Chabwino, lingalirani: Ngati mukanakhala ndi mphamvu, kodi mukanachotsa zinthu zonse zimene zimachititsa kuvutika kwa anthu? Ndipo kodi mukanachititsa mikhalidwe imene mtima wa anthu umalakalaka? Ndithudi mukanatero. Atate wathu wakumwamba wachikondi adzachita zimenezozo. Iye adzakwaniritsa zosowa ndi zokhumba zathu, pakuti Salmso 145:16 limati ponena za Mulungu: “Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.” Koma kodi zimenezi zidzachitika liti?

Madalitso Abwino Kwambiri Ayandikira

15. (a) Kodi mapeto a dziko adzatanthauzanji kaamba ka dziko lapansi (b) Kodi adzatanthauzanji kwa anthu oipa (c) Kodi adzatanthauzanji kwa awo amene akuchita chifuniro cha Mulungu?

15 Kuti atheketse madalitso abwino kwambiri amenewa padziko lapansi, Mulungu akulonjeza kuchotsa kuipa ndi awo amene amakuchititsa omwe. Pa nthawi imodzimodziyo, iye adzatetezera awo amene akumtumikira, pakuti Baibulo limati: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi yonse.” (1 Yohane 2:17) Ha, kumeneko kudzakhala kusintha kotani nanga! Mapeto a dziko sadzatanthauza mapeto a dziko lathu lapansi. M’malo mwake, monga momwe kunachitikira pa chigumula chapadziko lonse lapansi m’nthawi ya Nowa, adzatanthauza mapeto okha a anthu oipa ndi kakhalidwe kawo. Koma awo amene akutumikira Mulungu adzapulumuka mapetowo. Ndiyeno, padziko lapansi loyeretsedwa, iwo adzakhala omasuka kwa onse amene amafuna kuwavulaza ndi kuwatsendereza. —Mateyu 24:3, 37-39; Miyambo 2:21,22.

16. Kodi ndi zochitika zotani zimene zinanenedweratu kaamba ka “masiku otsiriza”?

16 Koma munthu wina angati: ‘Mikhalidwe ikuwonjezereka kuipa, sikusintha. Kodi tingatsimikizire bwanji kuti kusintha kwabwino kwambiri kumeneku kwayandikira?’ Yesu Kristu ananeneratu zinthu zambiri zimene atsatiri ake amtsogolo anayenera kufunafuna kotero kuti akadziwe kuti inali nthawi ya Mulungu ya kubweretsa mapeto a dziko. Yesu ananena kuti masiku otsiriza a dongosolo lino akasonyezedwa ndi zinthu zonga ngati nkhondo zazikulu, kuperewera kwa zakudya, zivomerezi zazikulu, kusaweruzika kowonjezereka ndi kutayika kowonjezereka kwa chikondi. (Mateyu 24:3-12) Anati kudzakhala “kuvutika maganizo kwa mitundu, yosadziwa njira yotulukira.”(Luka 21:25, NW) Ndiponso, Baibulo limanenanso kuti: “M’masiku otsiriza nthawi zosautsa zovuta kuchita nazo zidzafika.” (2 Timoteo 3:1-5, NW) Kodi imeneyi sindiyo mikhalidwe yeniyeniyo imene tirinkuiwona tsopano?

17. Kodi nchiyani chimene anthu oganiza akhala akunena ponena za mikhalidwe lerolino?

17 Anthu ambiri amene amapenda zochitika zadziko amanena kuti kusintha kwakukulu kulinkupangika. Mwa chitsanzo, mkonzi wa Miami, U.S.A., Herald, analemba kuti: “Munthu aliyense wokhala ndi maganizo anzeru pang’ono angasonkhanitse zochitika zowopsa za m’nzaka zowerengeka zapitazo ndi kuwona kuti dziko liri pakhomo penipeni. . . . Lidzasintha kosatha mmene anthu akukhalira ndi moyo.” M’njira yofananayo, mlembi Wachimereka Lewis Mumford anati: “Kutsungula kukunyonyotsoka. Motsimikizirika kwambiri . . . Kale pamene kutsungula kosiyanasiyana kunanyonyotsoka, kunali chowopsa cha pamalo amodzi kwenikweni . . . Tsopano, dziko lonse pokhala litalukana kwambiri ndi kugwirizana ndi njira zolankhulirana zamakono, pamene kutsungula kukunyonyotsoka, pulaneti lonse likunyonyotsoka.”

18. (a) Kodi nchiyani chimene mikhalidwe yadziko ikusonyeza ponena za mtsogolo? (b) Kodi nchiyani chimene chidzalowa m’malo mwa maboma amakono?

18 Mikhalidwe yeniyeniyo m’dziko lerolino imasonyeza kuti ife tsopano tirinkukhala pa nthawiyo pamene kuchotsedwa kwa dongosolo lonse la zinthuli kuli pafupi kuchitika. Inde, posachedwa kwenikweni tsopano Mulungu adzachotsa padziko lapansi onse amene akaliwononga. (Chivumbulutso 11:18) Iye adzachotsa maboma amakono kuti malo apezekere boma lake lolungama kuti lilamulire dziko lonse lapansi. Ndilo boma Laufumu limeneli limene Kristu anaphunzitsa omtsatira kupempha. —Danieli 2:44; Mateyu 6:9,10.

19. Ngati tikufuna kukhala ndi moyo kosatha, kodi tiyenera kuchitanji?

19 Ngati mukukonda moyo ndi kufuna kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi pansi pa ulamuliro wa Mulungu, pamenepo muyenera kufulumira kulandira chidziwitso cholongosoka cha Mulungu, zifuno zake ndi zofuna zake. Yesu Kristu m’pemphero kwa Mulungu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Ha, ndi chisangalalo chotani nanga kudziwa kuti tingakhale ndi moyo kosatha—kuti siloto chabe! Koma kuti tilandire dalitso labwino kwambiri lochokera kwa Mulungu limeneli tifunikira kudziwa za mdani amene akuyesa kutilepheretsa kupeza dalitso limeneli.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Kodi Mulungu anafuna kuti dziko likhale motero?

[Chithunzi chachikulu patsamba 11]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena