Phunziro 5
Kodi Chifuno cha Mulungu cha Dziko Lapansi N’chiyani?
Kodi Yehova analengeranji dziko lapansi? (1, 2)
Kodi n’chifukwa ninji dziko lapansi silili paradaiso tsopano? (3)
Kodi n’chiyani chidzachitika kwa anthu oipa? (4)
Kodi n’chiyani chimene Yesu adzachita mtsogolo kwa odwala? okalamba? akufa? (5, 6)
Kuti mukalandire madalitso amtsogolo, kodi muyenera kuchitanji? (7)
1. Yehova analenga dzikoli lapansi kuti anthu asangalale kukhalamo kosatha. Anafuna kuti dziko lapansi nthaŵi zonse likhalidwe ndi anthu olungama ndi achimwemwe. (Salmo 115:16; Yesaya 45:18) Dziko lapansi silidzawonongedwa konse; lidzakhala kosatha.—Salmo 104:5; Mlaliki 1:4.
2. Mulungu asanapange munthu, anasankha kachigawo kena ka dziko lapansi nakapanga paradaiso wokongola. Anakatcha munda wa Edene. Mmenemo ndimo anaika mwamuna ndi mkazi woyamba, Adamu ndi Hava. Chifuno cha Mulungu chinali chakuti iwo akhale ndi ana ndi kudzaza dziko lonse lapansi. M’kupita kwa nthaŵi iwo akanasandutsa dziko lonse lapansi paradaiso.—Genesis 1:28; 2:8, 15.
3. Adamu ndi Hava anachimwa mwa kuswa dala lamulo la Mulungu. Chotero Yehova anawachotsa m’munda wa Edene. Paradaiso anatayika. (Genesis 3:1-6, 23) Koma Yehova sanaiŵale chifuno chake cha dziko lapansili. Akulonjeza kuti adzalisandutsa paradaiso, mmene anthu adzakhala kosatha. Kodi adzachita motani zimenezi?—Salmo 37:29.
4. Dziko lapansili lisanakhale paradaiso, anthu oipa ayenera kuchotsedwapo. (Salmo 37:38) Izi zidzachitika pa Armagedo, imene ili nkhondo ya Mulungu yothetsa kuipa. Ndiyeno, Satana adzaponyedwa m’ndende zaka 1,000. Zimenezi zikutanthauza kuti sipadzakhala oipa owononga dziko lapansi. Anthu a Mulungu ndiwo okha amene adzapulumuka.—Chivumbulutso 16:14, 16; 20:1-3.
5. Ndiyeno Yesu Kristu adzalamulira dziko lapansi monga Mfumu kwa zaka 1,000. (Chivumbulutso 20:6) Iye pang’ono ndi pang’ono adzachotsa uchimo m’maganizo ndi m’matupi athu. Tidzakhala anthu angwiro monga analili Adamu ndi Hava asanachimwe. Ndiyeno sipadzakhalanso matenda, ukalamba, ndi imfa. Anthu odwala adzachiritsidwa, ndipo okalamba adzakhalanso anyamata.—Yobu 33:25; Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:3, 4.
6. Mkati mwa Ulamuliro wa Yesu wa Zaka Chikwi, anthu okhulupirika adzagwira ntchito yosandutsa dziko lapansi paradaiso. (Luka 23:43) Ndiponso, mamiliyoni a akufa adzaukitsidwira ku moyo waumunthu padziko lapansi. (Machitidwe 24:15) Ngati adzachita zimene Mulungu afuna kwa iwo, adzapitiriza kukhala padziko lapansi kosatha. Ngati sadzatero, adzawonongedwa kosatha.—Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 20:11-15.
7. Motero chifuno choyamba cha Mulungu pa dziko lapansi chidzakwaniritsidwa. Kodi mukufuna kulandira madalitso amtsogolo ameneŵa? Ngati mukutero, mufunikira kupitiriza kuphunzira za Yehova ndi kulabadira zofunika zake. Kupezeka pamisonkhano pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yakwanuko kudzakuthandizani kuchita zimenezo.—Yesaya 11:9; Ahebri 10:24, 25.
[Chithunzi patsamba 10]
Paradaiso wotayika
[Zithunzi patsamba 11]
Pambuyo pa Armagedo, dziko lapansi lidzasandutsidwa paradaiso