Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pr gawo 5 tsamba 20-22
  • Moyo Uli ndi Chifuno Chachikulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Moyo Uli ndi Chifuno Chachikulu
  • Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Mulungu Analenga Anthu
  • Chidakali Chifuno cha Mulungu
  • Kodi Chifuno cha Mulungu cha Dziko Lapansi N’chiyani?
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Chifuno Chenicheni cha Moyo
    Galamukani!—1992
  • Kodi Paradaiso Amene Baibulo Limatchula ali Kuti?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Dzikoli Lidzakhala Paradaiso?
    Galamukani!—2008
Onani Zambiri
Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
pr gawo 5 tsamba 20-22

Mbali 5

Moyo Uli ndi Chifuno Chachikulu

1 Njira imene dziko lapansi ndi zinthu zake zamoyo zinapangidwira imasonyeza kuti Mlengi wawo ali Mulungu wachikondi amene amasamaliradi. Ndipo Mawu ake, Baibulo, amasonyeza kuti iye amasamalira; amatipatsa mayankho abwino koposa a mafunso onga akuti: Kodi nchifukwa ninji tili padziko lapansi pano? ndi, Kodi tikumka kuti?

2 Tifunikira kupenda Baibulo kuti tipeze mayankho amenewo. Mawu a Mulungu amati: “Mukamfuna iye, mudzampeza; koma mukamsiya adzakusiyani.” (2 Mbiri 15:⁠2) Pamenepo, kodi kupenda Mawu a Mulungu kumavumbula chiyani ponena za chifuno chake kwa ife?

Chifukwa Chake Mulungu Analenga Anthu

3 Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anakonza dziko lapansi ndi anthu m’maganizo. Lemba la Yesaya 45:18 limanena za dziko lapansi kuti Mulungu “sanalilenga mwachabe [koma] analiumba akhalemo anthu.” Ndipo anaika padziko lapansi zonse zimene anthu akafunikira, osati kuti angokhalako, koma kuti asangalale ndi moyo mokwanira.​—⁠Genesis, machaputala 1 ndi 2.

4 M’Mawu ake, Mulungu amanena za kulengedwa kwa anthu oyamba, Adamu ndi Hava, ndipo amavumbula zimene anali nazo m’maganizo ponena za banja la anthu. Iye anati: “Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa ng’ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.” (Genesis 1:26) Anthu anafunikira kuyang’anira “dziko lonse lapansi” ndi nyama zake zolengedwa.

5 Mulungu anapanga munda waukulu wonga paki, m’mbali imene anaitcha Edene, yokhala ku Middle East. Ndiyeno iye “anatenga munthuyo, namuika iye m’munda wa Edene kuti aulime nauyang’anire.” Anali paradaiso wokhala ndi zakudya zonse zimene anthu oyambawo anafunikira. Ndipo munalinso “mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya,” limodzinso ndi zomera zina ndi mitundu yambiri yokondweretsa ya nyama.​—⁠Genesis 2:​7-9, 15.

6 Matupi a anthu oyambawo analengedwa angwiro, chotero sakanakhoza kudwala, kukalamba, kapena kufa. Iwo anapatsidwanso mikhalidwe ina yabwino, monga ngati ufulu wakusankha. Njira imene anapangidwira yalongosoledwa pa Genesis 1:27 kuti: “Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.” Popeza kuti tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu, sitinapatsidwe mikhalidwe yakuthupi ndi maganizo yokha komanso mbali zamakhalidwe ndi zauzimu, ndipo zimenezi ziyenera kukhutiritsidwa kuti tikhale achimwemwe kwenikweni. Mulungu akapereka njira yokhutiritsira zosoŵa zimenezo limodzinso ndi chakudya, madzi, ndi mpweya. Monga momwe Yesu Kristu ananenera, “munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.”​—⁠Mateyu 4:⁠4.

7 Ndiponso, Mulungu anapereka lamulo labwino koposa kwa anthu aŵiri oyamba pamene anali m’Edene lakuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Motero akakhala okhoza kubala ndi kulera ana angwiro. Ndipo pamene chiŵerengero cha anthu chikawonjezereka, iwo akakhala ndi ntchito yokondweretsa yakufutukula malire a paradaiso woyamba wonga paki, a Edene. Pomalizira pake, dziko lonse lapansi likasandulizidwa kukhala paradaiso, wokhalidwa ndi anthu angwiro ndi achimwemwe amene akakhala ndi moyo kosatha. Baibulo limatiuza kuti atatha kuyambitsa zonsezi, “Anaziwona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, tawonani, zinali zabwino ndithu.”​—⁠Genesis 1:⁠31; onaninso Salmo 118:17.

8 Nkowonekeratu kuti anthu anafunikira kugwiritsira ntchito dziko lapansi logonjetsedwalo kuti apindule. Koma zimenezi zinayenera kuchitidwa mosamala. Anthu anafunikira kukhala adindo achisamaliro a dziko lapansi, osati olisakaza. Kuwonongedwa kwa dziko lapansi kumene tikuwona lerolino nkotsutsana ndi chifuniro cha Mulungu, ndipo amene akukhala ndi phande m’zimenezo akuchita mosemphana ndi chifuno cha moyo padziko lapansi. Adzayenera kulandira chilango, popeza Baibulo limanena kuti Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’​—⁠Chivumbulutso 11:⁠18.

Chidakali Chifuno cha Mulungu

9 Chotero, kuyambira pachiyambi Mulungu anafuna kuti banja la anthu angwiro likhale padziko lapansi kosatha m’paradaiso. Ndipo chidakali chifuno chake! Chifuno chimenecho chidzakwaniritsidwa mosalephera konse. Baibulo limati: “Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, chotero chidzakhala.” “Ndanena, ndidzachiwonetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso.”​—⁠Yesaya 14:24; 46:⁠11.

10 Yesu Kristu analankhula za chifuno cha Mulungu chakubwezeretsa paradaiso padziko lapansi pamene anauza munthu wina amene anafuna chiyembekezo cha mtsogolo kuti: “Udzakhala ndine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Mtumwi Petro nayenso analankhula za dziko latsopano likudzalo pamene ananeneratu kuti: “Koma monga mwa lonjezano [la Mulungu] tiyembekezera miyamba yatsopano [kakonzedwe ka boma latsopano lolamulira kumwamba], ndi dziko latsopano [chitaganya cha dziko lapansi chatsopano] m’menemo mukhalitsa chilungamo.”​—⁠2 Petro 3:⁠13.

11 Wamasalmo Davide analembanso za dziko latsopano likudzalo ndi utali umene lidzakhala. Iye ananeneratu kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Nchifukwa chake Yesu analonjeza kuti: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.”​—⁠Mateyu 5:⁠5.

12 Ha, chimenecho nchifuno chachikulu chotani nanga, kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi laparadaiso popanda kuipa konse, upandu, matenda, chisoni, ndi chowawitsa! M’buku lomalizira la Baibulo, Mawu aulosi a Mulungu amanena mwachidule chifuno chachikulu chimenechi mwakulengeza kuti: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” Limawonjezera kuti: “Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Tawonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi owona.”​—⁠Chivumbulutso 21:​4, 5.

13 Inde, Mulungu ali ndi chifuno chachikulu m’maganizo. Lidzakhala dziko latsopano lachilungamo, paradaiso wamuyaya, amene ananenedweratu ndi Uyo amene angakhoze ndipo adzachita zimene walonjeza, popeza kuti “mawu [ake] ali okhulupirika ndi owona.”

[Study Questions]

1, 2. Kodi tingadziŵe bwanji kuti Mulungu amatisamalira, ndipo nkuti kumene tingatembenukire kuti tipeze mayankho a mafunso onena za moyo?

3. Kodi nchifukwa ninji Mulungu analenga dziko lapansi?

4. Kodi nchifukwa ninji Mulungu analenga anthu oyamba?

5. Kodi anthu oyambawo anaikidwa kuti?

6. Kodi anthu analengedwa ndi mikhalidwe yakuthupi ndi yauzimu yotani?

7. Kodi aŵiri oyambirirawo anapatsidwa lamulo lotani?

8. Kodi anthu anayenera kusamalira motani dziko lapansi?

9. Kodi nchifukwa ninji tili ndichidaliro kuti chifuno cha Mulungu chidzakwaniritsidwa?

10, 11. Kodi Yesu, Petro, ndi wamasalmo Davide analankhula motani za Paradaiso?

12, 13. Tanenani mwachidule za chifuno chachikulu cha Mulungu kwa anthu.

[Pictures on page 20, 21]

Mulungu anafuna kuti anthu akhale ndi moyo kosatha padziko lapansi laparadaiso. Chimenecho chidakali chifuno chake

[Picture on page 22]

Mwini wake angaŵerengere mlandu okhalamo amene akuwononga nyumba yake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena