Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 11/8 tsamba 8-9
  • Aids—Kodi Tingayembekezerenji m’Tsogolo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Aids—Kodi Tingayembekezerenji m’Tsogolo?
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Padzakhala Njira Yothetsera
  • Zinthu Zolimbikitsa Zimene Zachitika pa Ntchito Yolimbana ndi Edzi
    Galamukani!—2004
  • Aids—Mmene Tingalimbanirane Nayo
    Galamukani!—1998
  • Mankhwala a Edzi Akufunika Kwambiri!
    Galamukani!—2004
  • Edzi Yafala mu Africa
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 11/8 tsamba 8-9

Aids—Kodi Tingayembekezerenji m’Tsogolo?

KUSIYAPO vuto lakuti palibe mankhwala ochilitsira kapena kuteteza munthu kuti asatenge HIV, palinso mavuto ena amene amalepheretsa kuti nthendayi ibwerere m’mbuyo. Limodzi mwa iwo nlakuti anthu safuna kusintha makhalidwe awo ndipo amalolera kutenga kachilomboka. Mwachitsanzo, ku United States chiŵerengero cha anthu ogwidwa nkachilomboka sichikusintha, ngakhale kuti chiŵerengero cha omwe akugwidwa ndi matenda a AIDS chachepa. Associated Press inapereka ganizo lakuti mwina nchifukwa chakuti, “anthu ambiri samvera malangizo a mmene angadzitetezere.”

M’maiko otukuka, komwe kumanenedwa kuti kuli 93 peresenti ya omwe ali ndi HIV, kuli mavuto enanso okhudza nkhani yolimbana ndi nthendayi. Ambiri mwa maiko ameneŵa ndi osauka kwambiri mwakuti sangathe kupatsa anthu awo zinthu zoyenera pamoyo waukhondo. Ngakhale ngati mankhwala atsopanowa atakhalapo m’maikowo—kaŵirikaŵiri sakhala nawo—mtengo wakuti munthu amwe mankhwalaŵa chaka chonse ukhoza kuposa malipiro omwe anthu ambiri angalandire pamoyo wawo wonse!

Koma tingoyerekezera kuti patapezeka mankhwala atsopano otsika mtengo amene angathedi kuchiritsa nthendayi. Kodi anthu onse amene akuwafuna angawapeze? Mwina sizingatheke. Malinga ndi United Nations Children’s Fund, ana okwanira mamiliyoni asanu amamwalira ndi matenda ena asanu amene angathe kutetezedwa ndi mankhwala otsika mtengo omwe alipo.

Nanga bwanji za anthu amene amakhala m’maiko momwe sangathe kupeza mankhwalaŵa? Ruth Mota, wa International Health Programs ku Santa Cruz, California, anathandizapo mwakukonza maprogramu a mmene tingatetezere ndi kusamalira okhala ndi HIV m’maiko ambiri. Iye anati: “Malinga ndi zimene ndaona, kuwasamalira bwino anthu odwala nkofunika mongofanana ndi kuwapatsa mankhwala. Ndimadziŵa anthu omwe akhala nkachilombo ka HIV kwa zaka 10 mpaka 15 koma sanamwepo mankhwala. Mankhwala ndi ofunikadi, koma kuchiritsa anthu kumafuna zambiri koposa kumwa mankhwala chabe. Kumaphatikizapo mmene akukhalira, kuthandizidwa pachikhalidwe, zauzimu, ndi chakudya.”

Padzakhala Njira Yothetsera

Kodi pali chifukwa chilichonse chokhulupilira kuti tsiku lina AIDS idzatha? Inde, chilipo. Chifukwa chenicheni chokhulupilira chikupezeka m’mawu a mu lomwe ambiri amalitcha kuti Pemphero la Ambuye kapena la Atate Wathu (Paternoster). M’pemphero limenelo, lolembedwa m’Baibulo m’buku la Mateyu, timapempha kuti Mulungu achite kufuna kwake padziko monga momwe amachitira kumwamba. (Mateyu 6:9, 10) Mulungu safuna kuti anthu azivutika ndi matenda kosatha. Mulungu adzayankha pemphero limene lija. Motero, adzathetsa osati AIDS yokha komanso matenda onse amene amavutitsa anthu. Panthaŵiyo, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.

Padakali pano chomwe tingachite nkudziteteza basi. Matenda ambiri ali ndi njira ziŵiri: Mukhoza kudziteteza kapena kuchilitsidwa. Koma HIV, pali njira imodzi yokha basi. Mukhoza kudziteteza, koma simungathe kuchilitsidwa padakali pano. Nkuchitiranji zinthu zimene zingaike moyo wanu pachiswe? Ndithudi kudziteteza nkwabwino koposa kusachira.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

“Mankhwala ndi ofunikadi, koma kuchiritsa anthu kumafuna zambiri koposa kumwa mankhwala chabe. Kumaphatikizapo mmene akukhalira, kuthandizidwa pachikhalidwe, zauzimu, ndi chakudya.”—Ruth Mota

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

“Mpingo Unachita Zodabwitsa”

Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Amayi ake a Karen, yemwe tinamtchula m’nkhani yoyamba ija, analongosola mmene mpingo wa Mboni za Yehova wa kumeneko unachitira utamva zakuti Karen ndi Bill ali nkachilombo ka HIV. Iye anati: “Mpingo unachita zodabwitsa. Pamene Bill anadwala chibayo, nayenso Karen anali atadwala ndipo ankavutika kusamalira mwamuna wake pamodzi ndi ana. Abale ankawasesera m’nyumba, kuwakonzera galimoto, ndi kuwachapira zovala. Anawathandiza kusamalira nkhani zokhudza malamulo ndiponso kusamukira kunyumba ina. Anagula ndi kuwaphikira zakudya. Ankabwera kudzawalimbitsa mtima, kuwalimbikitsa mwauzimu, ndi kuwathandiza pazinthu zofunika pamoyo.”

[Chithunzi patsamba 8]

Kukhulupirika m’banja kukhoza kuteteza kuti musatenge kachilombo ka HIV

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena