Lingaliro la Baibulo
Kodi Mzimu Woyera wa Mulungu n’Chiyani?
“Ndipo panali pamene anthu onse anabatizidwa, ndipo yesu anabatizidwa, nalikupemphera, kuti panatseguka pathambo, ndipo mzimu woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lake ngati nkhunda, nadza pa iye; ndipo munatuluka mawu m’thambo, kuti, iwe ndiwe mwana wanga wokondedwa, mwa iwe ndikondwera.”—Luka 3:21, 22.
POLANKHULA ndi gulu la mafilosofa a ku Greece kale, mtumwi Paulo anatcha Mulungu kuti “ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi.” Paulo anati ndi Mulungu ameneyu amene “analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo” ndi amene “apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:24-28) Kodi Mulungu amazichita bwanji zonsezi? Ndi mwamzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito.
Baibulo limalongosolanso kuti Mulungu ‘mphamvu zake n’zazikulu, ndipo ndi wolimba mphamvu.’ (Yesaya 40:26) Inde, Mulungu analenga dziko lonse ndipo zimenezi zimasonyeza mphamvu yake yaikulu.
Mphamvu Zoonekera m’Ntchito
Sizingakhale zoona kwenikweni kunena kuti mzimu woyera ndi mphamvu ya Mulungu. N’chifukwa chakuti mphamvu zikhoza kumangokhala m’thupi la munthu kapena m’chinthu china monga mphamvu zokhala m’batire lomwe latchajidwa lomwe silikugwiritsidwa ntchito. Koma Malemba amasonyeza kuti mzimu wa Mulungu umakhala ukuyenda, mosasiyana kwenikweni ndi mphamvu yamagetsi imene imayenda kuchokera m’batire limene likugwiritsidwa ntchito. (Genesis 1:2) Choncho, mzimu woyera wa Mulungu ndi mphamvu yomwe amagwiritsira ntchito, mphamvu yogwira ntchito.
Nthaŵi zina Baibulo limanena za mzimu woyera kukhala utachita ntchito inayake kapena kuti unali malo ena kosiyana ndi kumene Mulungu anali. (Mateyu 28:19, 20; Luka 3:21, 22; Machitidwe 8:39; 13:4; 15:28, 29) Ena mwa amene aŵerenga nkhani zimenezi amalingalira kuti mzimu woyera ndi chinthu chapachokha chosiyana ndi Mulungu. Kodi n’chifukwa chiyani Malemba amanena motero? Kodi mzimu woyera ndi chinthu chapadera chosiyana ndi Mulungu?
Mulungu ndi wamtundu wina wosiyana kwambiri ndi chilengedwe chake chomwe timachiona ndi masochi. Iye ndi mzimu, amene sitingathe kumuona ndi maso. (Yohane 4:24) Baibulo limati Yehova Mulungu amakhala kumwamba ndipo kuti ali kumeneko amaona mtundu wa anthu. (Salmo 33:13, 14) Izi n’zomveka. Mlengi ayenera kukhala wamkulu kuposa zinthu zimene iye amazigwiritsa ntchito. Iye amazilamulira, kuzigwiritsa ntchito, kuzipanga.—Genesis 1:1.
Mulungu angapangitse kuti zinthu zichitike nthaŵi iliyonse ndipo kwina kulikonse ali kumalo ake omwe amakhalawo. Motero sayenera kuchita kukhala pamalo pamene mphamvu yake yogwira ntchito ikugwirira ntchito. Iye angathe kutumiza mzimu wake kuti ukachite ntchito ina yake. (Salmo 104:30) Masiku ano izi n’zosavuta kuzimvetsa makamaka kwa anthu amene amagwiritsa ntchito zipangizo za m’nyumba mwakungokanikiza batani pa chipangizo china chokhala pachokha chotchedwa remote control. Makono timadziŵa mphamvu za zinthu zina zosaoneka monga magetsi kapena infrared waves. Momwemonso, ndi mphamvu yake yosaoneka, kapena mzimu, Mulungu angathe kuchita chifuno chake chilichonse, popanda iye mwini kuyenda.—Yesaya 55:11.
M’nthawi za Baibulo nkhani imeneyi iyenera kuti inali yovuta kwambiri kuimvetsetsa. Kumautchula mzimu woyera monga mphamvu yapadera ndithudi kuyenera kuti kunkathandiza woŵerenga kumvetsa mmene Mulungu amagwiritsira ntchito mphamvu zake ngakhale kuti iye mwini sakhalapo pamene ntchitoyo ikuchita. Pamene Baibulo limati mzimu unachita chakuti, kwenikweni limakhala likunena kuti Mulungu iyemwiniyo wachita kapena kuti wagwiritsa ntchito mphamvu zake pa munthu kapena zinthu zina kuti achite zimene akufuna.
Ntchito Zosiyanasiyana za Mzimu Woyera
Yehova anagwiritsa ntchito mzimu woyera kupanga nyama zonse ndiponso zinthu zina zomwe sizili m’gulu la nyama. (Salmo 33:6) Mulungu anaugwiritsiranso ntchito kuwononga mbadwo wa anthu osalapa mwa kupangitsa chigumula. (Genesis 6:1-22) Ndi mphamvu yogwira ntchito yomweyi imene Mulungu anagwiritsa ntchito kusamutsira moyo wa Mwana wake m’mimba mwa namwali wachiyuda, Maliya.—Luka 1:35.
Nthaŵi zina mzimuwu umapatsa mphamvu anthu kuti alankhule choonadi mwamphamvu ndi molimba mtima pamaso pa adani, nthaŵi zambiri amatero moika miyoyo yawo pangozi. (Mika 3:8) Ndipo pali zitsanzo zambiri m’Baibulo, makamaka zokhudzana ndi maulosi, pamene amuna ndi akazi amadziŵiratu kapena kumvetsetsa zinthu zakutsogolo mwanjira ya mphamvu imeneyi. Popeza palibe munthu amene anganeneretu mosaphonyetsako zimene zidzachitika m’tsogolo, iyi ndi ntchito imodzi yooneka bwino ya mzimu.—2 Petro 1:20, 21.
Mzimu ungathenso kupangitsa munthu wina kukhala ndi mphamvu zozizwitsa. Mwachitsanzo, pogwiritsa ntchito mphamvu imeneyi, Yesu ankatha kulamulira zinthu zachilengedwe, kuchiritsa matenda, ndipo ngakhale kuutsa akufa. (Luka 4:18-21; 8:22-26, 49-56; 9:11) Mzimu ndiwo unagwiritsidwa ntchito kulinganiza zinthu ndi kupatsa mphamvu Akristu oyambirira kuti atumikire monga mboni za Mulungu padziko lonse.—Machitidwe 1:8; 2:1-47; Aroma 15:18, 19; 1 Akorinto 12:4-11.
Mphamvu za Mulungu Zimagwira Ntchito m’Malo Mwathu
Kodi n’zotheka kuti anthu omwe amatumikira Mulungu lerolino agwiritseko ntchito mphamvu yopanda malire imeneyi? Inde? Mulungu amapatsako mzimu woyera anthu ake kuwathandiza kuti amvetsetse ndi kukwanitsa kuchita chifuniro chake. Iye amapatsa mzimu amene amapemphera moona mtima, amene ali ndi mitima yabwino, ndi amene amakhala mogwirizana ndi zofuna zake. (1 Akorinto 2:10 -16) Mzimu umenewo ungathe kupatsa anthu opanda ungwiro “ukulu woposa wamphamvu,” umene ungawapangitse kutumikira Mulungu mokhulupirika mosasamala kanthu za zopinga. Ndithudi ndi chinthu chomwe anthu onse oopa Mulungu amasirira, kulandira mzimu wa Mulungu ndi kukhala nawobe.—2 Akorinto 4:7; Luka 11:13; Machitidwe 15:8; Aefeso 4:30.
Posachedwapa Mulungu adzagwiritsa ntchito mphamvu yaikulu imeneyi kuthetsa chisalungamo ndi kuvutika m’dziko loipali, motero akumalemekezetsa dzina lake lalikulu ndi loyera. Mzimu woyera udzakhala ukugwira ntchito padziko lonse lapansi kwamuyaya, ndipo zipatso zake zidzaoneka kwa onse, motero zikumapereka ulemerero kwa Mwini wake.—Agalatiya 5:22, 23; Chivumbulutso 21:3, 4.