Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Maseŵero Odziyerekeza Kukhala Munthu Wotchuka Angadzetse Ngozi Iliyonse?
“Ndi malingaliro chabe. Nthaŵi zina umakhala wamatsenga. Ndipo kenaka umadzakhala wankhondo. Mungakhale mtundu uliwonse wa munthu amene mumakhumba kufanana naye. Palibe malire.”—Christophe.
“DZIYEREKEZENI kukhala wina aliyense amene simungakhale.” Magazini ina inagwira mawu ameneŵa pamene inkalongosola za maseŵero ena otchuka odziyerekeza kukhala munthu wina. Achinyamata miyandamiyanda, omwe aloŵetsedwa m’maseŵera odziyerekeza kukhala munthu wotchuka akopeka kwambiri. Kodi maseŵera odziyerekeza kukhala munthu wotchukawa, kwenikweni n’chiyani?
Malinga n’kunena kwa buku lotchedwa Jeux de rôle (Maseŵera Odziyerekeza Kukhala Anthu Otchuka), “woseŵera aliyense amadziyerekeza kukhala wotchuka wina wam’mbiri, akumatsanzira zomwe ankakonda kuchita ndipo amayembekezera kusangalala ndi zotsatira za chochitikacho m’malingaliro chabe.” Cholinga cha maseŵerawo chimakhala chofuna kufanana ndi wotchukayo, mwa kupeza maluso, ndalama, zida, kapena mphamvu za matsenga amene amafunika kuti akwaniritse cholinga chakecho.
Maseŵera odziyerekeza kukhala munthu wina anatchuka kwambiri m’ma 1970 makamaka maseŵera otchedwa Dungeons and Dragons.a Kuchokera m’nthaŵiyo, yakhala njira yopezera madola mamiliyoni ochuluka, kuphatikizapo maseŵera apathabwa, makadi ogulitsa, zolembedwa m’mabuku, maseŵera apakompyuta, ngakhalenso maseŵera enieniwo kumene oseŵerawo amachita zenizeni zimene wotchuka amene akumuyerekezayo ankachita. Pakalipano ku United States kuli oseŵera 6 miliyoni, ndipo ku Europe kuli zikwi mazanamazana. Masukulu ambiri asekondale ku France, ali ndi makalabu a maseŵero odziyerekeza kukhala munthu wina, pamene ku Japan ndiwo maseŵero awo otchuka a pa video.
Ochirikiza maseŵerowo amanena kuti amalimbikitsa kulingalira bwino, amaphunzitsa luso lothetsera mavuto, ndiponso amakulitsa luso lochitira zinthu limodzi ndi khamu la anthu. Komabe otsutsa anena kuti maseŵero ameneŵa akuchititsa achinyamata kudzipha, kuyamba umbanda, kugwirira akazi, kufukula manda, ndi kulambira Satana. Ku Madrid, Spain, achinyamata aŵiri anamangidwa chifukwa choŵaganizira kuti anapha mwamuna wina wa zaka 52, pamene anali kupanga maseŵero odziyerekeza kukhala munthu wotchuka. Ku Japan, mnyamata wina anapha makolo ake ndipo kenako anadzicheka pamkono monga mbali yomaliza ya maseŵero amenewo. Zoona, kupatula ameneŵa—oseŵera ambiri n’nganzeru ndi okonda kuchita zinthu limodzi ndi anthu ena. Komabe, Akristu achinyamata angachite bwino atadzifunsa kuti, ‘kodi ndiyenera kupanga maseŵero odziyerekeza kukhala munthu wotchuka? Kodi ndifunikira kukhala wosamala?’
Chiwawa ndi Zamatsenga
Maseŵero odziyerekeza kukhala munthu wotchuka ali m’mitundu yambiri, yosiyana m’kachitidwe kake ndi zophatikizidwamo. Ngakhale kuti zili choncho, chiwawa chimachitika m’maseŵera ambiri aiwo. Chenicheni n’chakuti, m’dziko loyerekeza limene maseŵero ameneŵa amapangidwa, kaŵirikaŵiri chiwawa n’chimene chimakhala mbali yaikulu pofuna kupambana kapena kupita patsogolo. Tsono m’motani mmene kuchita maseŵero amenewo kungagwirizanire ndi malangizo a m’Baibulo? Miyambo 3:31 amati: “Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse.” Baibulo limatilimbikitsanso ‘kufunafuna ndi kulondola mtendere’ osati chiwawa.—1 Petro 3:11.
Vuto lina limene limakhalapo n’lakuti m’maseŵero ameneŵa mumachitika matsenga ochuluka zedi. Kaŵirikaŵiri, oseŵerawo amadzakhala anyanga kapena amatsenga. Zopinga zina kapena adani amawagonjetsa mwa matsenga. Nkhani ina inati, maseŵero ena otchuka “amafuna kuti oseŵera ena atenge mbali ya Angelo kapena Ziwanda akumatumikira Angelo akuluakulu kapenanso Akalonga a Ziwanda. . . Machitachita onyansa ndiwo amakhala zosangalatsa pamenepo.” Maseŵero ena a pakompyuta amalola woseŵera kukhala wamphamvuyonse mwa kungolemba dzina la “Satana.”
Achinyamata ena achikristu alingalira kuti palibe cholakwika ndi maseŵero odziyerekeza kukhala munthu wotchuka, malinga ngati munthuyo sawonongera nthaŵi yaitali pa maseŵerowo. “Ndi seŵero chabe,” anatero wachinyamata wina. Mwinamwake. Koma Mulungu anachenjeza Aisrayeli kuti asamachite zamatsenga. Chilamulo choperekedwa kwa Mose chinati “wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame kapena wanyanga, kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza. . . Yehova anyansidwa naye.”—Deuteronomo 18:10-12.
Pamenepo, kodi n’kwanzeru kuchita seŵero limene limalimbikitsa zamatsenga? Kupanga maseŵero odzala ndi zamatsenga sindikonso kuloŵerera mu ‘zakuya za Satana kodi’? (Chivumbulutso 2:24) Wachinyamata wina anati: “Ndinkachita seŵero loyerekeza kukhala munthu wotchuka tsiku lonse. Nditamaliza ndinaopa kuchoka panyumba. Ndinkaona ngati wina andichita chiwembu.” Kodi chinthu chochititsa mantha aakulu ngati amenewo chingakhale chabwino?
Zifukwa Zina
“Yafupika nthaŵi,” amatero 1 Akorinto 7:29. Choncho chodetsa nkhaŵa china chachikulu ndicho nthaŵi imene imathera pa maseŵero odziyerekeza kukhala munthu wina ameneŵa. Maseŵero ena amatenga maola, masiku, kapenanso milungu mukamaŵaseŵera. Kuwonjezera apo, maseŵerowo nthaŵi zina amatenga maganizo kwambiri, ngakhalenso kulowerera nawo, mwakuti zina zonse zimakankhidwira m’mbuyo. “Pamene ndatsiriza mbali imodzi ya maseŵerowo,” wachinyamata wina akutero, “ndinkafuna zina zokhwimirapo komanso zenizeni. Chinakhaladi chizoloŵezi changa.” Kodi kulowerera nazo kumeneko kungakhudze motani maphunziro a wachinyamata ndi ntchito zake zauzimu?—Aefeso 5:15-17.
Wachinyamata wina wa ku Japan akukumbukira kuti: “Nthaŵi zonse ndinkaganizira za chimene ndidzachitanso m’maseŵerowo ngakhale pamene sindikuseŵera. Kusukulu ngakhalenso kumisonkhano, ndinkaganiza za maseŵero basi. Ndinafika poti n’kusaganizanso china chilichonse koma maseŵerowo basi. Moyo wanga wauzimu unazilala.” Christophe wotchulidwa poyamba uja, akufotokoza mmene “anamwerekerera m’dziko lamaloto.” N’zoona kuti ‘pali mphindi yakuseka, ndi mphindi yakuvina,’ koma kodi kusangalala kuyenera kusapereka mpata wochita zauzimu?—Mlaliki 3:4.
Ganiziraninso za mzimu umene maseŵerowo amalimbikitsa. Magazini ina ya ku France inati ponena za maseŵero oyerekeza kukhala munthu wotchuka: “Mudzakumana ndi zovunda zosiyanasiyana, zosayenera, ndi zachinyengo, zolinganizidwa mochititsa mantha ndi kusinthiratu kaonedwe kanu ka zinthu.” Kodi mzimu umenewu n’ngwogwirizana ndi malangizo a m’Baibulo akuti “koma m’choipa khalani makanda”? (1 Akorinto 14:20) Potsirizira pake Christophe anaona kuti maseŵero amene ankachitawo “sankagwirizana ndi chikhalidwe cha Chikristu.” Akupitiriza kunena kuti: “N’nasiyiratu kulalikira, kupita ku misonkhano, ngakhale kuphunzira zabwino, monga chikondi cha Akristu, chifukwa panthaŵiyo ndinkachita zinthu zosemphana ndi Chikristu. Kunalidi kupanda nzeru.”
Chinyengo Kapena Zenizeni?
Achinyamata ambiri amakopeka ndi maseŵero ameneŵa pofuna kuthaŵa zenizenizo m’moyo. Koma kodi n’kwabwino kuloŵerera m’dziko la maloto limenelo? Katswiri wa ku France wachikhalidwe cha anthu, Laurent Trémel, akupereka ndemanga kuti: “Chilengedwe chenicheni, chodzala ndi zikayikiro ponena za m’tsogolo, . . . n’chosiyana kotheratu ndi chongoyerekezacho, kumene kumakhala kotheka kutsatira malamulo ndi kumenenso mungatengere chitsanzo cha mikhalidwe ya munthu amene m’mafuna kuti muoneke kapena mukhale monga iyeyo.” Katswiri wodziŵa za thanzi la maganizo Etty Buzyn akufotokozanso kuti: “Pamene achinyamata akuseŵera, amakhala ndi malingaliro akuti akukhala m’moyo woopsa, kusintha chikhalidwe, koma kunena zoona, sakhala pangozi iliyonse. Amathaŵa m’chikhalidwe cha anthu ndi mavuto ake.”
Potsirizira pake, chizoloŵezi chomalingalira zinthu zosatheka zikuchitika, chimangogwiritsa mwala munthu, chifukwa akangomaliza kuchita seŵerolo amabwereranso ku moyo wamasiku onse. Mapeto ake, zenizeni za moyo amadzakumana nazo basi. Ndithudi, palibe chipambano chilichonse kapena chochitika chongoyerekeza zinthu chimene chidzasintha zinthu zimene munalephera kapena kukupatsani luso limene mwachibadwa si lanu. Choyenera kuchita ndicho kuyang’anizana ndi zenizeni m’moyo—kuchita nazo! Kulitsani luso lanu la kuzindikira mwa kuyang’anizana ndi mikhalidwe yeniyeni ya moyo. (Ahebri 5:14, NW) Kulitsani mikhalidwe yauzimu yomwe idzakutheketsani kupirira mavuto anu. (Agalatiya 5:22, 23) Kuchita zimenezo n’kokhutiritsa ndi kofupa kusiyana ndi kuchita seŵero lina lililonse.
Zimenezi sizikutanthauza kuti maseŵero onse odziyerekeza kukhala munthu wotchuka n’ngwoipa ayi. M’nthaŵi ya Baibulo, ana ankachita maseŵero oyerekeza zinthu, ndipo ngakhale Yesu anaona zimenezo. (Luka 7:32) Ndipo Yesu sanaletse kusangalala. Komabe, Akristu achinyamata, limodzi ndi makolo awo ayenera “kuyesera chokondweretsa ambuye n’chiyani.” (Aefeso 5:10) Pamene mukulingalira za maseŵero, dzifunseni kuti, ‘kodi “akusonyeza ntchito za thupi”? Kodi ‘adzasokoneza ubwenzi wanga ndi Mulungu?’ (Agalatiya 5:19-21) Mwa kulingalira mfundo zimenezo mudzasankha mwanzeru ponena za maseŵero odziyerekeza kukhala munthu wotchuka.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Galamukani! yachingelezi ya March 22, 1982, masamba 26-7.
[Zithunzi patsamba 29]
Kodi maseŵero ena odziyerekeza kukhala munthu wotchuka amalimbikitsa mzimu wotani?