Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 9/8 tsamba 31
  • Kodi Kuika Anthu Magazi N’kofunikadi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kuika Anthu Magazi N’kofunikadi?
  • Galamukani!—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Kuthiridwa Mwazi Ndiko Mfungulo Yopulumukira?
    Galamukani!—1990
  • Kodi Kuika Magazi Anthu Odwala Kudzapitirirabe?
    Galamukani!—2006
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Ndimphatso ya Moyo Kapena Mpsopsono wa Imfa?
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 9/8 tsamba 31

Kodi Kuika Anthu Magazi N’kofunikadi?

M’MWEZI wa November chaka chatha funso lili pamwambali linafunsidwa m’nyuzipepala inayake m’nkhani yolembedwa ndi Dr. Ceril Godec, wapampando wa anthu odziŵa za matenda a m’chikhodzodzo pa chipatala cha Long Island College Hospital, ku Brooklyn, New York. Iye analemba kuti: “Lero mwina magazi sangavomerezedwenso kukhala monga mankhwala, chifukwa chakuti sangakwanire pa miyezo ya zinthu zosawononga thupi ya bungwe loona za zakudya komanso mankhwala la Food and Drug Administration. Magazi n’chiŵalo cha thupi ndipo kuika munthu magazi n’chimodzimodzi ndi kumuika chiŵalo cha munthu wina.”

Dr. Godec anati: “Kuika munthu chiŵalo cha munthu wina kumachitidwa pambuyo poti palibenso njira iliyonse yochizira wodwalayo. Chifukwa chakuti kumatha kudwalitsanso munthu, odwala amauzidwa njira zina zonse zochiritsira matendawo asanaikidwe chiŵalo china.” Ponenapo za kuika munthu magazi, iye anati: “Ubwino wake n’ngwokayikitsa kwambiri kotero kuti madokotala a opaleshoni ambiri ayamba kutsatira maganizo akuti ‘peŵeratu kuika munthu magazi’ osati kokha pa zifukwa zokhudza zachipatala komanso zokhudza lamulo.”

Vuto lalikulu kwambiri la kuika munthu magazi ndi lakuti anthu zikwi zambiri apatsidwa matenda oopsa, kuphatikizapo AIDS. Ngakhale kuti njira zoyezera magazi zapita patsogolo m’mayiko ambiri, Dr. Godec analongosola kuti: “Ngozi yaikulu ili pa magazi amene aperekedwa ndi anthu amene ali ndi tizilombo toyambitsa matenda koma amene thupi lawo silinakhazikitse mphamvu yolimbana ndi tizilomboto imene ingazindikiridwe poyezedwa.”

Pomaliza nkhani yake, Dr. Godec anayankha funso limene lili pamwambalo motere “Pamene madokotala wamba ndi madokotala a opaleshoni ayamba kumvetsa bwinopo za kayendedwe ka mpweya wa okosijeni ndi kuzindikira kuti mbali yamagazi yotchedwa hemoglobin siyenera kukhala yochuluka monga mmene anali kuganiziridwa poyamba, angathe kupeza zoloŵa mmalo mwa kuika munthu magazi pafupifupi nthaŵi iliyonseyo. Posachedwapa, tingoti chaka chatha chomwechi, maopaleshoni ovuta kwambiri, a kuika munthu mtima ndi chiwindi china anali kutayitsa anthu magazi ambiri kotero akuti anali ofuna kuti magaziwo aziwabwezeretsa nthaŵi zonse. Lero zonsezi zatha kuchitidwa popanda kuika munthu magazi.

“N’zotheka kwabasi kuti m’tsogolo muno kuika munthu magazi kudzathetsedweratu. . . . Kuika munthu magazi n’kokwera mtengo ndiponso n’koopsa; komanso, sikupereka m’pang’ono pomwe chisamaliro chothandizadi chimene odwala amafunikira.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena