Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 9/8 tsamba 32
  • “Muli Chidziŵitso Chabwino Bwanji!”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Muli Chidziŵitso Chabwino Bwanji!”
  • Galamukani!—1999
Galamukani!—1999
g99 9/8 tsamba 32

“Muli Chidziŵitso Chabwino Bwanji!”

Kodi achinyamata angadziŵe bwanji chofunika pamoyo, angadzimvetse bwanji, kapena kuphunzira mmene angakhalire bwino ndi makolo awo? Posachedwapa, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Spain inalandira kalata, imene mwa zina inanena kuti:

“Cholembera kalatayi ndi chakuti ndikufuna kukuthokozani kwambiri zedi chifukwa cha ntchito yoyamikirika imene mumachita mwakufalitsa mabuku abwino kwambiri, monga limene limatchedwa Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Muli chidziŵitso chabwino bwanji! Ndikuthokoza amene analilemba ndi amenenso analifalitsa, pokwaniritsa maloto a achiyamata ambiri.

“Ndine mtsikana wa zaka 21 ndipo ndinaganiza zoyamba kuphunzira Baibulo. . . . Ndiye mwamwayi, chifukwa cha mnzanga wina, ndinapeza buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.

“Poyamba ndinali kuganiza kuti silingandithandize n’komwe, koma pang’onopang’ono, ndinayamba kuchita nalo chidwi kwambiri poliŵerenga. Linandichititsa kuganiza za zinthu zambiri, monga zimene ndiyenera kuchita ndi moyo wanga ndipo m’kupita kwa nthaŵi linayankha mafunso anga. Pokhala ndi chuma chimenechi ndinaphunzira kumvetsa makolo anga, kukhululukira ena, ndi mmene ndingakhalire mkazi ndi kuchita zinthu ngati mkazidi.”

Ngati mungakonde kupindula ndi chidziŵitso cha m’buku la Achichepere Akufunsa, mungathe kulandira lanu polemba m’kabokosi kotsatiraka ndi kukatumiza ku adiresi imene yasonyezedwapo kapena ku adiresi yoyenerera imene yasonyezedwa pa tsamba 5 la magazini ano.

□ Nditumizireni buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena