Tetezani Mwana Wanu Kungozi
YOSIMBIDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU SWEDEN
HANNA, pamene anali ndi zaka pafupifupi zitatu, anali limodzi ndi makolo ake, Karl-Erik ndi Birgitta, pamene ankakonza m’nyumba ya mnansi wawo amene anali atamwalira. Patapita nthaŵi pang’ono, Hanna anatuluka m’chipinda ali ndi botolo la mapilisi m’manja mwake. Anali atadyako ena. Poona botololo, Birgitta anachita kakasi. Linali botolo la mankhwala a mtima a mnansi wawo uja.
Mwamsanga, Hanna anam’tengera kuchipatala, kumene anakakhalako usiku umodzi m’chipinda cha anthu odwala mwakayakaya. Ngakhale kuti anamwa mlingo wa mankhwala amene akanatha kuvulaza thanzi lake, mpaka kalekale iye sanadwale matenda alionse. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kanthaŵi kochepa asanadye mankhwalawo anali atadya phala pang’ono. Phalalo limene linasakanizikana ndi poizoni analisanza.
Si Hanna yekha amene anakumana ndi zoterezi. Tsiku lililonse, ana zikwizikwi padziko lonse amachita ngozi zofunika kupita nawo kwa dokotala kapena kuchipatala. Chaka chilichonse mwana mmodzi mwa ana 8 alionse ku Sweden amalandira chithandizo kuchipatala chifukwa chochita ngozi. Motero ngati muli kholo, n’zotheka kwabasi kuti zimenezi zingachitikire mwana wanu.
Sizodabwitsa kuti nthaŵi zambiri ana amavulala kumalo ozoloŵereka, monga panyumba kapena pabwalo. Kuvulala kwake kumasinthasintha akamakula. Mwana wakhanda angathe kugwa mosavuta patebulo limene amamuvekerapo thewera kapena kutsamwa ndi chakudya kapena kanthu kamene kam’phata pakhosi. Ana nthaŵi zambiri amagwa akamakwera zinthu ngakhalenso kupsa kapena kumwa mankhwala akupha akamagwiragwira kapena kulaŵa zinthu zimene ali nazo pafupi. Ana ausinkhu wopita kusukulu nthaŵi zambiri amavulazidwa pangozi zapamsewu kapena akamaseŵera panja.
Zambiri mwa ngozi zimenezi zingathe kupeŵedwa. Pokhala okonzekereratu komanso kudziŵa bwino za msinkhu wa mwana wanu, mungathandize kupeŵa kuvulala kapenanso ngozi zoopsa kwambiri. Zimenezi zatsimikizidwa ndi ntchito ya kuteteza ana imene yakhala ikuchitika ku Sweden kuyambira 1954. Isanayambe, ana opitirira 450 anali kufa pangozi chaka chilichonse. Lero chiŵerengero cha imfa zotere chatsika n’kufika pa 70.
M’nyumba
“Simungaphunzitse mwana wachaka chimodzi, zaka ziŵiri, kapena zitatu kupeŵa ngozi n’kumaganiza kuti azikumbukira,” anatero katswiri wa zamaganizo a ana Kerstin Bāckstrōm. Motero, udindo wothandiza mwana wanu kupeŵa ngozi uli m’manja mwa inu monga kholo kapena achikulire ena amene mwanayo amakhala nawo kaŵirikaŵiri.
Choyamba, tayang’anani kuzungulira panyumba panupo. Gwiritsani ntchito ndandanda yokukumbutsani imene ili m’bokosilo. Mwina zinthu zina zotetezera sizipezeka m’mayiko onse kapena mwina zimapezeka pamtengo wokwera. Komabe, mwakugwiritsa ntchito luso lanu, ndi kuganizira, mungathe kupeza njira yothandiza malingana ndi mmene zinthu zilili kwa inuyo.
Mwachitsanzo, ngati makabati a m’khichini mwanu ali ndi zitseko zokhala ndi zotsegulira zokoloŵeka mungawatseke poloŵetsa ka mtengo m’zotsegulirazo. Mungachitenso mofanana ndi chitseko cha uvuni. Matumba a pulasitiki saopsa kwenikweni mukawamanga pamodzi musanawasunge.
Mwina mungathe kuganiza njira zina zosavuta zopeŵera ngozi m’nyumba komanso panja ndipo mungathe kuuza anzanu ndi ena owadziŵa amene ali ndi ana ang’onoang’ono.
Panja
Yenderani malo amene mwana wanu amaseŵerako. Ana ambiri a zaka zopitirira zinayi amachita ngozi akamaseŵera panja. Amagwa n’kudzipweteka kapena amagwa panjinga zawo. Ngozi zoopsa kwambiri zapanja zimene zimachitikachitika kwa ana oyambira pa zaka zitatu mpaka zisanu n’ziŵiri ndizo ngozi zapamsewu ndiponso kumira.
Poyendera mabwalo amene amaseŵererako, muone ngati malowo ali abwino kotero kuti mwanayo asavulale akamaseŵerapo. Kodi pansi pa mizende, zokwerapo zina, ndi zinthu zina zoterezi pali zinthu zofeŵa, monga mchenga kotero kuti ngati mwanayo atagwa sangapweteke?
Kodi pafupi ndi nyumba yanu pali zitsime kapena makwawa a madzi? Madzi ochepa chabe angathe kumiza mwana wanu. “Mwana wamng’ono akagwa chafufumimba m’madzi, sadziŵa kuti kumwamba n’kuti ndipo pansi mpati,” anatero Bāckstrōm, katswiri wa zamaganizo a ana. “Mwanayo sangathe n’komwe kudzidzutsanso.”
Choncho, lamulo lofunika kwambiri ndi ili: Osasiya ana oyambira pa chaka chimodzi mpaka zitatu kuti aziseŵera okhaokha panja popanda munthu wamkulu wowayang’anira. Ngati chapafupi pali madzi ochepa, dikirani kaye kuti mwanayo akule ndithu musanayambe kumulola kukaseŵera panja popanda kumuyang’anira.
Pamsewu
Zimenezi n’zothandizanso ngati pali msewu wagalimoto pafupi ndi nyumba yanu. “Mwana wosayamba sukulu angamvetse machenjezo okha amene ali osavuta kumva ndipo amachita chidwi ndi chinthu chimodzi chokha panthaŵi imodzi,” anatero Bāckstrōm. “Koma pamsewu pamakhala zinthu zambirimbiri ndiponso mauthenga ochokera uku ndi uku.” Musalole mwana wanu kudumpha msewu ali yekha pokhapokha ngati wafika msinkhu wopita kusukulu. Akatswiri amati ana sangayende okha panjinga mu msewu wodutsa magalimoto ambiri mpaka atafika zaka 12.
Phunzitsani mwana wanu kugwiritsa ntchito chipewa chodzitetezera akamakwera njinga, kukwera pamsana pa nyama inayake, kuyenda pansapato za matayala, kapena akamaguguzana. Kuvulala m’mutu kumavuta kuchiritsa ndipo kungapundule kapena kupha kumene! Pachipatala china cha ana, 60 peresenti ya amene anali kupatsidwa chithandizo chifukwa cha ngozi za njinga zakapalasa anali n’zilonda m’mutu ndi kumaso, koma amene anali kugwiritsa ntchito zipewa zodzitetezera sanavulale kwambiri m’mutu.
Komanso onetsetsani kuti mwana wanu ndi wotetezedwa mukamayenda ulendo wapagalimoto. Mayiko ambiri ali ndi malamulo amene amati ana aang’ono azimangiridwa m’mipando yotetezera pangozi yopangidwa mwapadera. Zimenezi zachepetsa kwambiri chiŵerengero cha kuvulala ndiponso imfa za ana ochita ngozi zapamsewu. Ngati mipando yotetezera pangozi iliko kumene mukukhala, mungateteze moyo pogulako umodzi. Koma onetsetsani kuti mwagula mtundu wovomerezeka. Dziŵani kuti mipando ya makanda ndi yosiyana ndi ya ana a zaka zoyambira pa zitatu.
Ana athu ali mphatso zamtengo wapatali zochokera kwa Yehova, ndipo tiyenera kuwasamalira m’njira iliyonse. (Salmo 127:3, 4) Monga makolo abwino, Karl-Erik ndi Birgitta nthaŵi zonse akhala ofunitsitsa kuteteza ana awo ngozi ya Hanna ija isanachitike ndipo ngakhale itachitika. “Koma mwachionekere tinali osamala kwambiri kuchokera pamene ngoziyo inachitika,” Karl-Erik akuvomereza motero. “Tsopano tili ndi zidzukulu, ndipo nthaŵi zonse timaonetsetsa kuti mankhwala ali pobisa,” Birgitta akunena choncho.
[Bokosi patsamba 22]
Chitetezo M’nyumba Mwanu
• Mankhwala: Aikeni pamalo amene mwana sangafikirepo m’kabati yokhoma. N’chimodzimodzinso ndi mankhwala osalemberedwa ndi dokotala kapena mankhwala azitsamba. Chinanso, uzani alendo ogona kuti asunge pabwino mankhwala awo.
• Mankhwala ogwiritsidwa ntchito panyumba: Asungeni pamene anawo sangawaone m’kabati yokhoma. Aikeni m’mabotolo ake enieni kuti azidziŵika bwinobwino. Samalani ndi mankhwalawo pamene mukuwagwiritsa ntchito, ndipo nthaŵi zonse abiseni, ngakhale pamene mukungotuluka m’chipinda kwakanthaŵi kochepa chabe. Mmene mumatsukira mbale musasiyemo madzi amankhwala otsukira mbale.
• Chitofu: Nthaŵi zonse zigwiriro za mapoto ziziloza m’kati mwa chitofu. Ikani simbi yogwira poto kuti asagwe ngati muli nayo. Ikani chinthu chogwirizira chitofucho kuti chisagwe kotero kuti muteteze mwanayo ngati angakwere pachitseko cha chitofucho pamene chili chotsegula. Chitseko cha chitofucho chiyenera kukhala ndi pokhomera. Kodi mwanayo akhoza kupsa atagwira chitseko cha chitofucho? Ndiyetu ikanipo thabwa lotsekapo kuti iye asathe kugwira chitseko chotenthacho.
• Zinthu zoopsa zogwiritsidwa ntchito panyumba: Mipeni, masizesi, ndi zipangizo zina zoopsa ziyenera kuikidwa m’makabati okhala ndi maloko kapena akabale kapena zibiseni pamene ana sangafikirepo. Ngati mukugwiritsa ntchito zinthu zimenezi ndiye mwangoziika kaye pambali, ziikeni patali ndi m’mphepete mwa tebulo, pamene mwanayo sangafikire. Machesi ndi matumba a pulasitiki nawonso n’ngoopsa kwa ana aang’ono.
• Masitepe: Ikani zitsulo zazitali kuyambira masentimita 70 mpaka 75 mbali zonse zamasitepewo.
• Mazenera ndi zitseko: Khomani pamwamba pake akabale, matcheni, kapena zinthu zina zotetezera zoletsa mwana kutsegula kapena kudzipapatiza pamene zili zotsegula kuti mpweya uloŵe m’chipinda.
• Makabati a mabuku: Ngati mwanayo amakonda kukwerakwera ndi kukhala pamwamba pa zinthu, ikani makabati a mabuku ndi zipangizo zina zazitali zoterezi kuchipupa kuti zisagwe.
• Masoketi ndiponso mawaya a magetsi: Masoketi amene sakugwiritsidwa ntchito ayenera kukhala ndi loko kapena chinachake chowatseka. Nthambo za nyale zamagetsi zapatebulo ndi zinthu zina zotero ziyenera kumangiriridwa kuchipupa kapena kukabati kuti mwanayo asakoke nyalizo ndipo n’kumugwera. Apo ayi, zibiseni nyalizi. Osasiya simbi yositira yamagetsi pa katebulo kositirapo, ndipo osasiya nthambo ya magetsi ya simbiyo ili lendelende.
• Madzi otentha: Ngati mungathe kusintha mlingo wa kutentha kwa madzi anu sinthani kuti akhale ofunda, kotero kuti mwanayo asapse ngati atatsegula mpopi wa madzi otentha.
• Zoseŵeretsa: Tayani zoseŵeretsa zosongoka. Tayani zoseŵeretsa zing’onozing’ono kapena zimene zingathe kuphwasulidwa n’kukhala tizidutswa ting’onoting’ono, chifukwa zingathe kum’phata mwanayo pakhosi ngati ataziika m’kamwa. Maso komanso mphuno za zidole ziyenera kukhala zosokeredwa bwino. Phunzitsani achimwene komanso alongo ake okulirapo kuti azichotsa zoseŵeretsa zawo zing’onozing’ono mwanayo akakhala ali pansi.
• Masiwiti ndi tizakudya tina: Musasiye masiwiti kapena tizakudya tina, monga mtedza kapena masiwiti olimba, poonekera. Angathe kum’phata mwana pakhosi.
[Mawu a Chithunzi]
Gwero: The Office of the Children’s Ombudsman
[Chithunzi patsamba 22]
Ngati Ngozi Ichitika
• Kumwa mankhwala akupha: Ngati mwana wamwa mankhwala akupha ena ake a madzi, kapena mankhwala alionse oopsa, tsukani mkamwa mwake bwinobwino ndipo m’mwetseni madzi kapena mkaka wozadza kapu imodzi kapena aŵiri. Kenaka, pezani dokotala kapena malo opereka chidziŵitso cha zamankhwala akupha kuti akupatseni malangizo. Ngati mankhwala oipa amuloŵa m’maso mwanayo, nthaŵi yomweyo tsukanimo ndi madzi ambiri kwa mphindi zosachepera khumi.
• Zilonda zamoto: Pazilonda zazing’ono, muikepo madzi ozizira (asakhale ozizira kwambiri) kwa mphindi zosachepera 20. Ngati chilondacho chili chachikulu kuposa chikhatho cha mwanayo kapena ngati chili kumaso, pamfundo, pamimba kapena kumaliseche muyenera kum’pititsa mwanayo kuchipatala kugawo losamalira za ngozi. Zilonda zozama zapakhungu nthaŵi zonse ziyenera kuonedwa ndi dokotala.
• Kutsamwa: Ngati chinachake cham’phata mwana pakhosi muyenera kuchotsa chinthucho mwamsanga. Njira imodzi yothandiza imene mungachite ndiyo njira yotchedwa Heimlich Maneuver. Ngati simukuidziŵa onanani ndi dokotala wanu kuti mudziŵe zambiri za njira imeneyi, kapena pitani kumaphunziro achithandizo choyamba choperekedwa kwa anthu ovulala pa ngozi ndipo kumeneko akakuphunzitsani njira imeneyi.
[Mawu a Chithunzi]
Gwero: The Swedish Red Cross
[Chithunzi patsamba 23]
Kuvala chipewa chotetezera panjinga yakapalasa
[Chithunzi patsamba 23]
Kukhala motetezeka pampando wam’galimoto