“Mwana Wanu Ali ndi Matenda a Shuga!”
SINDIDZAIŴALA msanga mmene ndinamvera atandiuza mawu ameneŵa dokotala. Panthaŵiyo Sonya mwana wanga, anali ndi zaka khumi zakubadwa. Iye anali ndi thanzi labwino, wamphamvu ndipo nthaŵi zina ankachita kunyanya. Nthaŵi yokha yomwe anamwa mankhwala chifukwa choti wadwala ndi pamene anali ndi zaka zisanu zakubadwa.
Komabe, masiku angapo tisanakaonane ndi dokotala ameneyu zinthu zinafika povuta. Sonya sanali kupeza bwino. Ankafuna kumwa madzi ambiri, akatero ankafuna kukodza pafupipafupi—nthaŵi zina, mphindi 15 zilizonse. Usiku anali kudzuka kosachepera katatu kukakodza. Poyamba ndinanyalanyaza zizindikiro zimenezi ndikumaganiza kuti ameneŵa ndi matenda wamba a m’chikhodzodzo, ndipo kuti achira posachedwapa. Koma patapita masiku ochepa, ndinaona kuti pafunika mankhwala oti mwina akaphe tizilombo m’chikhodzodzomo.
Nthaŵi imeneyi m’pamene ndinapita naye kwa dokotala. Ndinafotokoza zimene ndinkaganiza kuti ndiwo matenda amene akudwala. Anamuuza kuti akodzere m’chikho kuti ayese mkodzo wake, ndipo atatero ndinaona kuti mkodzowo unali ndi tizidutswa tambirimbiri tokhala ngati timadzi tolimba. Nesi nayenso anationa. Matenda omwe ankam’ganizira anaoneka pamene anamuyesa magazi. Anapeza kuti anali matenda a shuga omwe amatchedwa kuti mtundu woyamba wa matenda a shuga.
Sonya ankawadziŵa bwino zedi matenda ameneŵa. Ngakhale kuti anali ndi zaka khumi zokha zakubadwa, iye anali ataphunzira za matenda a shuga kusukulu. Anagwidwa ndi mantha komanso anathedwa nzeru monganso ineyo. Dokotala anatiuza kuti pafunika kupita naye ku chipatala mwamsanga zinthu zisanafike poipa. Anam’konzera ulendo wopita ku chipatala ku Portland, Oregon, U.S.A. kumene anakam’goneka m’chipinda cha anthu odwala mwakayakaya. Sonya anali wokwiya kwambiri kuti zoterezi zamuchitikira. Iye sankafuna kuti azikhalira kudzibaya majakisoni kuti akhale ndi moyo. Analira kwinaku akufunsa kuti n’chifukwa chiyani zimenezi zachitika. Inenso ndinamva chisoni kwambiri moti sindinathe kuugwira mtima. Ndipo sindinapirire. Chotero, tinangokhala motsamirana m’chipinda choyembekezera kwinaku tikusisima ndi kupempha Yehova kuti atithandize kupirira.
Mavuto Tili m’Chipatala
Dokotala anandilola kupita kunyumba ndi Sonya kukatenga zinthu zina ndi zina, kukaimbira foni Phil mwamuna wanga, ndiponso kuuza munthu wina kukatenga Austin mwana wathu wamwamuna kusukulu. Pasanathe ndi ola limodzi lomwe ine ndi mwamuna wanga tinafika naye Sonya kuchipatala kuja. Nthaŵi yomweyo anamuika botolo la madzi kuti achotse shuga wosafunika ndi zinthu zina zotchedwa kuti ketones m’magazi.a Zimenezi zinali zopweteka kwambiri. Sonya anali atawonda kwambiri moti sikero yake inatsika ndi makilogalamu atatu chifukwa chotaya madzi ambiri. Mitsempha yake inali kuvuta kupeza. Komabe, nesi anayesetsa pantchito yake ndipo zinthu zinayamba kusintha panthaŵiyo. Tinalandira buku lalikulu ndi mapepala ena ambiri kuti tiwaŵerenge ndi kuwamvetsa asanatilole kum’tenga Sonya kupita kunyumba.
Ndiyetu kunali kukumana ndi madokotala, manesi, ndiponso akatswiri a zakadyedwe. Anatiphunzitsa mmene tingagwiritsire ntchito jakisoni kuti tizim’baya Sonya kum’patsa mankhwala a madzi a mu nsoso kaŵiri patsiku kuyambira tsiku lomwelo. Tinaphunziranso mmene tingayesere magazi, zimene Sonya adzafunikira kuchita kanayi patsiku kuti tione mlingo wa shuga m’thupi mwake. Panalidi zambiri zoti tiphunzire! Anatilangizanso za chakudya chimene tiyenera kumam’patsa. Anamuletsa kudya zakudya zomwe zili ndi shuga wambiri, komanso kuti azikadya zakudya zamagulu atatu kuti akule bwino, panthaŵi yachakudya iliyonse pazikhala zakudya zokhala ndi mlingo woyenera wa zakudya zopatsa mphamvu.
Patapita masiku atatu anam’tulutsa m’chipatala. Anavomereza kuti ndizim’baya jakisoni koma magazi azidziyesa yekha. Mwezi umodzi wokha anafuna kuti azidzibaya yekha jakisoni, ndipo n’zimene wakhala akuchita mpaka pano. Zinali zochititsa chidwi kuona kuti analolera zoti ali ndi matendawo ndi kumakhala mosangalala. Anasiya zofuna kufa kuti akangouka m’Paradaiso ndipo tsopano amadziŵa zizindikiro za matenda ake, mmene zimam’khudzira mtima, zolephera zake komanso amatha kufotokoza maganizo ake pamene akufuna thandizo.
Nyengo ya Kusintha
Miyezi ingapo yoyambirira zinthu zinali zovuta kwambiri. Aliyense m’banja lathu anali kuvutika ndi maganizo osiyanasiyana ambirimbiri. Ndinali kuyesetsa kuchita zochuluka kwambiri koma zinafika pena pongoganiza kuti apa ndi bwino ndithaŵe. Ndandanda ya zochita inali yovuta kuikwaniritsa, makamaka pamene kunali kofunikanso kupita ku misonkhano ya mpingo ndi ku ntchito yathu yolalikira osaphatikizapo pologalamu ya tsiku ndi tsiku ya kusukulu ndi zopita ku tchuthi. Koma titapemphera mobwerezabwereza, ine ndi mwamuna wanga tinaphunzira kuchita ndi tsiku lililonse palokha ndipo tinalandira udindo wathu watsopanowo.
Tinapeza dokotala amene ndi katswiri wa ziŵalo zomwe zimapanga mahomoni m’thupi amenenso ali wokonzeka nthaŵi zonse kutithandiza pamavuto athu, ngakhale kum’tumizira uthenga wa pakompyuta zikavuta. Timakam’chezera ku ofesi kwake nthaŵi ndi nthaŵi. Kupita kwathu kwa dokotalayo pa miyezi itatu iliyonse kuti akamupime kumatithandiza kuona mmene Sonya alili ndiponso kumatipatsa chitsimikizo chakuti tikuchita zonse zomwe tingathe kum’samalira.
Monga mmene zimakhalira, mwana wathu wamwamuna zinali kum’vuta poona kuti tikupereka chisamaliro chathu chonse kwa mlongo wakeyo kukhala ngati tamuiŵala iye. Ena mumpingo ndiponso aphunzitsi ake kusukulu anazindikira zimenezi ndipo anam’thandiza kukhala wotanganidwa komanso kuona kuti panafunikira masinthidwe pokhala zinthu zinali zitasintha. Tsopano wakhala akuthandiza kwambiri kusamalira Sonya. Monga makolo, nthaŵi zina tinkakonda kuteteza Sonya mopyola mlingo komanso timaopa mopyola muyezo kuti kaya matenda akewo am’yendera bwanji. Taona kuti njira yabwino yopeŵera nkhaŵa zimenezi ndiyo kufufuza za matenda ameneŵa ndi kudziŵa zomwe angachite pathupi la munthu.
Zinthu Zili Pati Tsopano?
Kaŵirikaŵiri timakonda kulankhula za malonjezo a Yehova ndi nthaŵi yomwe ikuyandikira pamene matenda adzakhala zinthu zakale. (Yesaya 33:24) Kufikira nthaŵiyo, cholinga chathu monga banja ndicho kukhala okangalika pa kutumikira Yehova, tikumachita mbali yaikulu m’ntchito ya kuuza ena za Ufumu wa Mulungu. Komanso timayesetsa kuti tisamaphonye misonkhano ya mpingo.
Zaka zingapo zapitazo, mwamuna wanga anapeza ntchito yakuthupi yakanthaŵi ku Israel. Poganizira za matenda a Sonya, tinaganiza mofatsa za ulendowo ndipo tinaupempherera kwambiri. Tinaona kuti titakonzeka bwinobwino, kuphatikizapo kupeza chakudya chabwino cha Sonya, ulendo umenewu ungadzetse ngakhale madalitso auzimu. Kwa chaka chimodzi ndi theka, tinakhala ndi mwayi wa kumasonkhana mumpingo wachingelezi wa Tel Aviv. Tinasangalala kwambiri kuchita nawo ulaliki m’njira ina, ndipo banja lathu linaphunzira zinthu zambiri.
Mawu ochepa chabe akuti “Mwana wanu ali ndi matenda a shuga” anasintha moyo wathu kotheratu. Koma m’malo motaya mtima, tinagwirizana kusamala mwana wathuyo monga ntchito ya aliyense m’banja lathu, ndipo zimenezi zabweretsa mgwirizano wa banja lonse. Yehova, “Mulungu wa chitonthozo chonse,” watithandiza kuti tipirire. (2 Akorinto 1:3)—Yosimbidwa ndi Cindy Herd.
[Mawu a M’munsi]
a “Matenda a shuga akapanda kuchiritsidwa amayambitsa ketosis. Imeneyi imayamba chifukwa cha kuchulukana kwa ma ketones m’thupi, zotsala mafuta atagaika m’magazi; kenako pamatsatira acidosis (kuchulukana kwa asidi m’magazi) komanso kumva mselu ndi kusanza. Pamene thupi ligaya zakudya zopatsa mphamvu ndi mafuta koma kugayako osayenda bwino, zotsala zapoizoni pakugayapo zimachulukirachulukira m’thupi, ndipo wodwalayo amakomoka.”—Encyclopædia Britannica.
[Bokosi patsamba 25]
Kodi Matenda a Shuga N’chiyani?
Matupi athu amagaya chakudya chomwe timadya kuchisandutsa mphamvu zomwe timagwiritsa ntchito. Zimenezi n’zofunika kwambiri mofanana ndi kupuma. M’chifu ndi m’matumbo, zakudya zimagaidwa ndi kuikidwa m’timagulu malinga ndi mitundu yake, kuphatikizapo mtundu wa shuga wotchedwa glucose. Nsoso ukamva shuga umatulutsa madzi amene amathandiza shugayo kuloŵa m’maselo a thupi. Zikatero shuga uja amatenthedwa ndipo amatulutsa mphamvu.
Ngati munthu akudwala matenda a shuga, ndiko kuti nsoso wake sukutulutsa madzi ake okwanira kapena kuti thupi silikugwiritsa bwino ntchito madziwo. Zotsatira zake zimakhala zakuti shuga amene ali m’magazi sangathe kuloŵa m’maselo kuti akagwire ntchito. Buku lakuti Understanding Insulin Dependent Diabetes limanena kuti: “Shuga amachuluka kwambiri m’magazi ndipo amasefukira kudzera mu impso n’kuloŵa m’mikodzo.” Munthu wodwalayo ngati sakulandira mankhwala amakodza pafupipafupi komanso amaonetsa zizindikiro zina.
[Bokosi patsamba 25]
Mtundu Woyamba wa Matenda a Shuga
Mtundu wa matenda a shuga umenewu kale unkadziŵika ndi dzina lakuti matenda a shuga a ana, chifukwa chakuti mtundu umenewu kaŵirikaŵiri umagwira ana ndi achinyamata. Komabe angagwirenso anthu amisinkhu ina. Ngakhale kuti chimene chimayambitsa matenda a shuga sichikudziŵika, pali zinthu zosiyanasiyana zimene ena amakhulupirira kuti zimayambitsa mtundu woyamba wa matenda a shuga monga:
1. Kuwatenga kwa makolo (m’majini)
2. Kusokonezeka kwa mphamvu yolimbana ndi matenda m’thupi (thupi limakana ziwalo zake zina kapena mitundu ina ya maselo ndipo limayamba kulimbana nazo—mwachitsanzo nsoso)
3. Kuipa kwa malo okhala (tizilombo toyambitsa matenda kapena mankhwala oipa)
N’kutheka kuti matenda omwe amayamba chifukwa cha tizilombo totchedwa vairasi ndi zinthu zina amawononga timaselo ta mu nsoso (timene timapanga madzi ake). Pamene timaselo tochuluka timeneti tiwonongeka, munthuyo amayembekezeka kudzadwala matenda a shuga.
Munthu wodwala matenda a shuga amasonyeza zizindikiro zambiri monga:
1. Kukodza pafupipafupi
2. Kumva ludzu kwambiri
3. Kumva njala pafupipafupi; thupi limamva njala chifukwa chofuna mphamvu zimene silikulandira
4. Wodwalayo amawonda. Ngati thupi silikulandira shuga m’maselo ake, limagwiritsa ntchito mafuta ndi mapuloteni kuti lipeze mphamvu, zikatero munthuyo amawonda
5. Kukwiyakwiya. Ngati wodwalayo amadzuka pafupipafupi usiku kukakodza, sagona tulo tabwino. Zimenezi zingachititse wodwalayo kusintha khalidwe lake.
Ponena za mtundu woyamba wa matenda a shuga, zimene zimachitika n’zakuti nsoso umapanga madzi ake ochepa kapena kuti suwapanga n’komwe. Zikakhala chonchi, munthu ayenera kulandira madzi a mu nsoso tsiku lililonse ochita kugula, pogwiritsa ntchito jakisoni (ngati munthu achita kumwa madziwo, sizithandiza chifukwa amawonongeka m’chifu).
[Bokosi patsamba 25]
Mtundu Wachiŵiri wa Matenda a Shuga
Musasokonezeke ndi mtundu woyamba uja, chifukwa mtundu wachiŵiriwu zimene zimachitika n’zakuti thupi silipanga madzi okwanira a mu nsoso kapena kuti silikugwiritsa bwino ntchito madzi ameneŵa. Mtundu umenewu umakonda kugwira anthu akuluakulu amisinkhu yoposa zaka 40 ndipo umakonda kugwira munthu pang’onopang’ono. Matenda ameneŵa munthu amawatenga kwa makolo, ndipo kaŵirikaŵiri amafika poipa ngati munthu sakudya zakudya zabwino kapena ngati ndi wonenepa kwambiri. Nthaŵi zambiri mapilisi amathandiza, makamaka pachiyambi penipeni, kusonkhezera nsoso kuti uzipanga madzi ake ambiri. Mapilisiwo si amadzi a mu nsoso ayi.
[Bokosi patsamba 00]
Kuopsa kwa Matenda a Shuga
Thupi nthaŵi zonse limafuna mphamvu kuti ligwire ntchito. Ndiyeno ngati silingagwiritse ntchito shuga kupangira mphamvu zimenezi, limagwiritsa ntchito mafuta ndi mapuloteni ake. Komabe, ngati thupi ligwiritsa ntchito mafuta, zotsalira zotchedwa kuti ketones zimapangika. Zikatero zotsalira zimenezi zimachuluka m’magazi ndipo zimaloŵa mu mkodzo. Pokhala kuti ma ketones ameneŵa amakhala ndi asidi wamphamvu kuposa wa m’maselo, kuchuluka kwa ma ketones ameneŵa m’magazi kungayambitse matenda ena oopsa a kuchuluka kwa asidi ndi ma ketones m’thupi.
Kumakhalanso koopsa kwa munthu wodwala matenda a shuga ngati magazi ake alibe shuga wokwanira (hypoglycemia). Wodwalayo angadziŵe zimenezi mwa kuona zizindikiro zina zosasangalatsa. Iye nthaŵi zina angamanthunthumire, kukha thukuta kwambiri, kufooka, kumva njala, kukwiyakwiya, mutu kusayenda bwino, kapenanso kumva mtima kuthamanga, kuona chimbuuzi, mutu kuŵaŵa, dzanzi, komanso kulasalasa kukamwa ndi m’milomo. Wodwalayo angafikire ngakhale pa kuchita khunyu. Kudya zakudya zoyenera komanso pa nthaŵi yake kaŵirikaŵiri zimathandiza kupeŵa mavuto otere.
Ngati zizindikiro zomwe tatchula pamwambazi zioneka, kudya shuga mwinamwake madzi azipatso kapena mapilisi a shuga, zingathandize kubwezeretsa mlingo wa shuga m’thupi kufikira pamene zakudya zina zidzapezeke. Ngati zinthu zafika poipa, wodwalayo ayenera kulandira jakisoni ya mahomoni otchedwa glucagon. Mahomoni ameneŵa amathandiza kuti chiŵindi chithe kutulutsa shuga yemwe chimasunga, zikatero shuga amawonjezeka m’magazi. Makolo amene mwana wawo akudwala matenda a shuga adzayenera kufotokoza vutoli kwa akusukulu ndi woperekeza mwanayo ku sukulu kapenanso akusukulu ya mkaka.
[Bokosi patsamba 26]
Matenda Aakulu
Munthu wodwala matenda a shuga angadwale matenda ena aakulu monga mtima, sitiroko, vuto la maso, matenda a impso, mapazi ndi miyendo kupweteka, ndiponso kudwala pafupipafupi. Matenda ameneŵa amachitika chifukwa cha kuwonongeka kwa mitsempha ya magazi, minyewa ndiponso kuchepa kwa mphamvu yolimbana ndi matenda m’thupi. Komabe, si wodwala matenda a shuga aliyense amene angadwale matenda aakulu ameneŵa.
Kuonetsetsa kuti m’thupi mwa wodwalayo muli shuga wokwanira zidzathandiza kuchepetsa mpata woti n’kudzadwala matenda enawo. Kuwonjezera apo, kuonetsetsa kuti wodwalayo sakunenepa kwambiri, magazi ake akuthamanga bwino lomwe ndipo sakusuta fodya ingakhale njira yabwino yochepetsera matenda enawo. Wodwala matenda a shuga ayenera nthaŵi zambiri kumachita maseŵera olimbitsa thupi, kudya zakudya zoyenera, ndiponso kulandira mankhwala ake.
[Chithunzi patsamba 27]
Banja la a Herd