Kuchititsa Dziko Kugwiritsa Ntchito Mankhwala Osokoneza Bongo
YOSIMBIDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU SPAIN
KHANDA lobadwa kumene likulira mofuula m’chipatala cha ku Madrid, ku Spain. Namwino akuyesa kuligwira apa ndi apa kuti alitonthoze koma akulephera. Khandalo likuvutika chifukwa cha mankhwala osokoneza bongo otchedwa heroin. Kuphatikizanso apo lili ndi kachilombo ka HIV. Amayi ake anali chidakwa cha mankhwala a heroin.
Mosadziŵa, mayi wina wa mumzinda wa Los Angeles akuyendetsa galimoto mumsewu wodzaza ndi anthu ogulitsa mankhwala osokoneza bongo. Iye akuwomberedwa ndi zipolopolo, zimene zapha mwana wake wakhanda wamkazi.
Ku Afghanistan, makilomita zikwi zambiri kuchokera kumeneku, mlimi wosauka akulima munda wambewu yokhala ngati fodya yotchedwa poppy. M’chaka chimenechi zinthu zayenda bwino; ndipo wakolola dzinthu zochuluka ndi 25 peresenti. Mankhwala otchedwa opium amene amapangidwa kuchokera ku ma Poppy ndi opindulitsa kwambiri, ndipo m’banja la mlimiyo zikuvuta kupeza zinthu zofunika m’moyo. Koma posachedwa ma poppy okongola ameneŵa awasandutsa mankhwala a heroin, ndipo mankhwalawa amawononga miyoyo.
Mtsikana wosinkhuka wamanyazi wa ku Sydney, Australia, Loŵeruka lililonse usiku amapita ku dansi. Poyamba zinali kumuvuta kwambiri kukhala m’chigulu, koma posachedwapa mapilisi otchedwa ecstasy amulimbitsa mtima. Mapilisi amene iye amamwa anafika mwakatangale ku Australia kuchokera ku Netherlands, ngakhale kuti nyumba zopangirako mankhwala za komweko nazonso zayamba kuwagulitsa. Ecstasy amachititsa kuti nyimbo zizimveka bwino, ndipo iye amatha mantha. Ndiponso amadziona kuti akuoneka wokongola kwambiri.
Manuel, mlimi wosauka ndiponso wakhama, amagwira ntchito yolima pamunda wake waung’ono ku Andes, ndipo zinthu zinayamba kumuyendera bwino pamene anayamba kulima mbewu yotchedwa coca. Manuel akufuna kusiya kulima mbewuyi , koma akuopa kuti akatero akwiyitsa anthu ankhanza amene amayang’anira ulimi wambewu ya coca m’dera lake.
Aŵa ndi ena chabe mwa anthu amene akuchititsa vuto la mankhwala osokoneza bongo limene likuwonga dziko lathu.a Kaya anthu ameneŵa ndi ogula, opanga, kapena ongoonerera, mankhwalawa akulamulira miyoyo yawo.
Kodi Vuto la Mankhwala Osokoneza Bongo N’lalikulu Motani?
Mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations, a Kofi Annan ananena ndemanga yakuti: “Mankhwala osokoneza bongo akuwononga anthu, akulimbikitsa uchigaŵenga, akufalitsa matenda monga a AIDS, ndipo akupha ana athu ndiponso tsogolo lathu.” Kodi ndi anthu angati amene amakodwa ndi khalidweli? Iye anawonjezera kuti: “Lero pali anthu pafupifupi mamiliyoni 190 amene akugwiritsa ntchito mankhwalawa padziko lonse. Palibe dziko lotetezeka. Ndipo palibe dziko limene lingayembekeze kuthetsa malondawa palokha. M’pofunika kuti mayiko onse achitepo kanthu kuti athetse malonda a mankhwalawa padziko lonse.”
Powonongerawonongera zinthu, m’zaka zingapo zapitazi apanga mankhwala osokoneza bongo okhala ngati mankhwala wamba.b Mankhwala ameneŵa amapangidwa n’cholinga chochititsa munthu wakumwayo kumva ngati akusangalala, kapena kumva bwino. Chifukwa chakuti mankhwala opangawa angapangidwe motsika mtengo pafupifupi kulikonse, apolisi sangathe kuwaletsa ngakhale pang’ono. Mu 1997 Bungwe la United Nations Loona za Mankhwala Osokoneza Bongo Padziko Lonse linachenjeza kuti m’mayiko ambiri mankhwala opangidwa mwatsopano asanduka mbali ya “chikhalidwe cha anthu ogula” ndipo kuti ayenera kuonedwa monga “chinthu choopsa m’mayiko onse m’zaka zana lotsatirali.”
Mankhwala atsopanowa ndi amphamvu zofanana ndi za akale aja. Mankhwala a Crack cocaine atsopanoŵa ndi amphamvu koposa cocaine woyamba. Mankhwala atsopano opangidwa kuchokera ku chambac ali ndi mphamvu zosokoneza bongo zambiri, ndipo mankhwala opangidwa mwatsopano otchedwa ice ali m’gulu la mankhwala oipa kwambiri.
Ndalama Ndiponso Mphamvu za Mankhwala Osokoneza Bongo
Ngakhale kuti anthu ogwiritsa ntchito mankhwalawa alipo ochepa poyerekezera ndi osatero, iwo ali okwanira kupereka mphamvu zochuluka kwa anthu oyendetsa malonda a mankhwalawa, anthu amene amakonza za kupanga komanso kugulitsa mankhwalawa. Anthu opulukirawa amachita katangale amene akupanga naye phindu lalikulu kwambiri ndipo tinganene kuti ndiwo malonda opindulitsa kwambiri padziko lonse. Malonda a katangale wa mankhwala osokoneza bongo amakwana 8 peresenti ya malonda onse a padziko, kapena pafupifupi $400,000,000,000 pachaka. Ndalama za mankhwala osokoneza bongo zikamazungulira padziko lonse, zimalemeretsa zigandanga, kupereka ziphuphu kwa apolisi, kwa andale ndipo zingachirikize uchigaŵenga.
Kodi pangachitike chilichonse kuti vuto la malonda a mankhwala osokoneza bongo lithetsedwe? Kodi malonda a mankhwala osokoneza bongo amakhudza bwanji ndalama zanu, chitetezo chanu, ndi moyo wa ana anu?
[Mawu a M’munsi]
a M’nkhani zino, tikunena za mankhwala amene amagulitsidwa mophwanya lamulo ndipo amagwiritsidwa ntchito osati pochiritsa matenda.
b Mankhwala osinthidwa pang’ono kapangidwe, nthaŵi zambiri amawapanga kuti athe kuzemba malamulo oletsa mankhwala osokoneza bongo.
c Chamba amachipanga poyanika nsonga za mtengo wa chamba. Mtengo womwewu amapangiranso mankhwala ena osokoneza bongo. Anthu ogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo amasutanso zonsezi.
[Mapu patsamba 4, 5]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Kupanga ndi Kuzembetsa Mankhwala Osokoneza Bongo Padziko Lonse
MADERA AKULUAKULU AMENE AMAPANGIRAKO MANKHWALAWA:
Chamba—chamasamba ndi chamaliroliro
Heroin
Cocaine
Mivi ikusonyeza njira zikuluzikulu zozembetseramo mankhwalawa.
[Mawu a Chithunzi]
Gwero: United Nations World Drug Report
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
U.S. Navy photo