Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 12/8 tsamba 28-30
  • Zoona Zake za Angelo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zoona Zake za Angelo
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Angelo Angakuthandizireni
  • Mmene Angelo Angakuthandizireni
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Angelo—Kodi Amayambukira Moyo Wanu?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mmene Angelo Amatikhudzira
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Angelo a Mulungu Amatithandiza
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 12/8 tsamba 28-30

Zoona Zake za Angelo

MONGA taonera kale, zoganiza ndiponso nkhani zotchuka zonena za angelo sizivomerezana nthaŵi zonse ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Kodi pali chovuta ngakhale sizikugwirizana? Kodi pali cholakwa chilichonse ngati titavomereza zikhulupiriro zotchuka zokhudza angelo? Inde, mosakayika konse.

Mwachitsanzo, taganizirani za malingaliro amene amalimbikitsidwa ndi “mkhalidwe wauzimu watsopano.” Mabuku amakono a angelo amalimbikitsa anthu kusaganiza okha chochita, monga ana, mmalo mogwiritsa ntchito mphamvu ya kuganiza. Nthaŵi zambiri oŵerengawo salimbikitsidwa kuti ayese kupeza njira zothetsera mavuto awo kapena kuti ayese kumvetsetsa Baibulo ndi chidziŵitso cha Mulungu. Mabuku a za angelo amatitsimikizira kuti m’moyo wathu timayenda ndi mngelo wabwino ndi wachikondi ndipo kuti palibe chifukwa chochitira mantha, pakuti tikukhala m’chilengedwe chachimwemwe mmene chinthu chilichonse chili mmalo mwake. Pakakhala vuto, tiyenera kungodikira kuti angelo achitepo kanthu. Komabe ngati zimenezi zili zoona, n’chifukwa chiyani Baibulo limatiuza kuti “menyani zolimba nkhondo ya chikhulupiriro.”—Yuda 3, NW.

Mabuku ambiri a angelo amapezerapo mwayi pa kudzikonda ndiponso kupusa kwa anthu. Amagogomezera kwambiri umwini wa munthu. Mabuku otereŵa amati, angelo amasiku ano amafuna kutidziŵitsa kukongola komanso kuwala kwathu. Ngakhale kuti ndibwino kuti tizidziona moyenera, mfundo yaikulu ya “mkhalidwe wauzimu watsopano” ndi yakuti tizidzikonda zivute zitani. Wolemba nkhani wina anati lamulo loyamba ndiponso lalikulu kwambiri ndi lakuti “uzidzikonda wekha monga Mbuye.” Zimenezitu zikutsutsana kotheratu ndi mawu a Yesu! Iye anati: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba.” (Mateyu 22:36-39) Tidzakhala osangalala kwambiri m’moyo tikamafuna kuchita kaye zofuna za Mulungu tisanachite zofuna zathu.

Kuika angelo patsogolo n’kosemphana ndi Chikristu choona. Mtumwi Paulo anatsutsa mchitidwe wolambira angelo. (Akolose 2:18) Kulambira kumatanthauza “kulemekeza kapena kupereka ulemu monga kwa Mulungu kapena mphamvu yauzimu.” Komabe, kulemekeza komanso kupereka ulemu kwa angelo monga kwa Mulungu n’kumene mabuku ambiri a angelo amalimbikitsa aŵerengi kuchita. Komabe, kumbukirani zimene zinachitika pamene Satana anapempha Yesu kuti agwade kusonyeza kum’lambira. Yesu anayankha kuti: “Ambuye Mulungu wako uzim’gwadira, Ndipo Iye yekha yekha uzim’tumikira.” (Luka 4:8) Nthaŵi ina, pamene mtumwi Yohane anagwa pamapazi pa mngelo, mngeloyo ananena kwa iye kuti: “Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzawo wa abale ako akukhala nawo umboni wa Yesu; lambira Mulungu.”—Chivumbulutso 19:10.

Mmene Angelo Angakuthandizireni

Amene tiyenera kumufikira kuti atitsogoze ndi kutithandiza ndiye Mulungu, osati angelo. Iye ali wofunitsitsa ndi wosangalala kupereka moolowa manja chikondi chake kwa onse amene amatsatira miyezo yake yolungama. Mtumwi Yohane analembera Akristu anzake kuti: “Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera; ndipo ngati tidziŵa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziŵa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.”—1 Yohane 5:14, 15.

Pali zambiri zimene sitidziŵa zokhudza angelo okhulupirika a Mulungu. Komabe, tikudziŵa kuti amatumikira Mulungu ndipo amagwira ntchito mogwirizana ndi chifuno ndiponso chitsogozo chake. Ali ofunitsitsa kupititsa patsogolo choonadi chonena za Mulungu. (Chivumbulutso 14:6, 7) Sakhumba kuti tiziwalambira. Chifukwa chakuti sitingathe kuwaona, sitidziŵa kuti Mulungu amawagwiritsa ntchito kumulingo wotani pothandiza anthu ake pa zochitika za tsiku ndi tsiku. Koma tikudziŵa kuti Yehova Mulungu amateteza ndipo amatsogolera anthu ake monga gulu.

Angelo okhulupirika amatipatsa chitsanzo chabwinodi! Amalemekeza ndi kutamanda Mulungu. (Salmo 148:2) Ngakhale kuti ali ndi mphamvu zambiri zamaganizo ndiponso zauzimu; amasonyeza ulemu waukulu ku uchifumu wa Yehova. (Yuda 9) Amaganizira kwambiri za kukwaniritsidwa kwa zofuna za Mulungu. (1 Petro 1:11, 12) Zimenezi timaziphunzira m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Inde, Baibulo ndilo buku limene limatiuza zoona zake za angelo.

[Mawu Otsindika patsamba 30]

Angelo n’ngofunitsitsa kupititsa patsogolo choonadi chonena za Mulungu

[Chithunzi pamasamba 28, 29]

Pamene mtumwi Yohane anayesa kulambira mngelo, mngeloyo anati: “Usatero!”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena