Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 12/8 tsamba 10-12
  • Kusintha Kwabwino Kochititsa Chidwi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusintha Kwabwino Kochititsa Chidwi
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusintha pa Zofunika
  • Tili Pamodzi Koma Tadzipatula
  • 1914, Chaka Chosonyezedwa Kale
  • Posachedwapa Dziko Latsopanodi
  • Mmene Tidziŵira Kuti Tiri mu “Masiku Otsiriza”
    Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Chifuno cha Mulungu Chidzakwaniritsidwa Posachedwapa
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Kodi Tilidi ‘M’masiku Otsiriza’?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Uthenga Wabwino Umene Amafuna Kuti Muumve
    Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 12/8 tsamba 10-12

Kusintha Kwabwino Kochititsa Chidwi

“Mu 1900 dziko lapansi linali kumayambiriro kwa imodzi mwa nyengo za kusintha zochititsa chidwi kwambiri m’mbiri ya anthu. Dongosolo lamakedzana linali kupatsa mpata latsopano.”—Buku la mapu lotchedwa The Times Atlas of the 20th Century.

KUMAYAMBIRIRO kwa zaka zana la 20, “dziko lapansi linaloŵa m’nyengo yachipwirikiti ndiponso chiwawa chadzaoneni,” likutero buku limene mawu ake ali pamwambapo. M’tsogolo mwa zaka zana limeneli munadzakhala nkhondo zambiri kuposa mwa zaka zana lililonse, ndipo anthu oposa 100 miliyoni anaphedwa.

M’nyengo ino, nkhondo zapha anthu wamba ambiri kuposa kale lonse. M’nkhondo yoyamba yapadziko lonse, 15 peresenti ya akufa anali anthu wamba. Koma m’nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse, m’mayiko ena anthu wamba ambiri anafa kuposa asilikali. Kuyambira pamenepo miyandamiyanda ya anthu amene aphedwa pankhondo, ambiri mwa iwo ndi anthu wamba. Chiwawa chonsechi, chakwaniritsa ulosi wa Baibulo wonena za ‘kavalo wofiira,’ amene ‘anapatsidwa mphamvu yakuchotsa mtendere padziko.’—Chivumbulutso 6:3, 4; Mateyu 24:3-7.

Kusintha pa Zofunika

Zaka zana la 20 zakwaniritsa ulosi wa pa 2 Timoteo 3:1-5, umene umati: “Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.”

Anthu poti ndi opanda ungwiro, akhala akusonyeza makhalidwe ameneŵa kumlingo winawake kuyambira kale. Koma m’zaka zana la 20, mtima wofuna zinthu wotere wakula ndiponso n’ngofala. Anthu amene anali ndi makhalidwe amene talongosola pamwambapa kale ankaoneka monga opanda khalidwe, kapena oipiratu kumene. Koma tsopano ngakhale anthu “akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo” akuona makhalidwe ameneŵa monga zabwino.

Panthaŵi ina anthu achipembedzo anali kuona kuti sikwanzeru kuti anthu osakwatirana azikhala pamodzi. Kuchembeza usanakwatiwe kumaonedwa monga chinthu chochititsa manyazi, monga mmene kugonana kwa ofanana ziwalo kunalili. Anthu ambiri sankaganizako n’komwe zochotsa mimba, ngakhalenso kusudzulana. Kusaona mtima pa za malonda kunali kosaloleka. Koma lero, wolemba wina akuti, “chilichonse n’chololeka.” N’chifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa chimodzi n’chakuti, “zimenezi zimakhutiritsa kudzikonda kwa anthu ena amene safuna kuti wina awaletse kuchita zinthu zina.”

M’zaka zana lino, kunyalanyaza makhalidwe abwino apamwamba kwachititsa kuti anthu asinthe zokonda zawo. Buku la The Times Atlas of the 20th Century likulongosola kuti: “Mu 1900 maboma ndi anthu sankaŵerenga ndalama monga chuma ayi . . . Koma pakutha kwa zaka za zana limeneli mayiko akamati zinthu zikuyenda bwino anali kunena ndalama. . . . Nawo anthu anasintha maganizo pankhani ya chuma.” Lero kufala kwa njuga kwadzetsa kukonda ndalama, pamene wailesi, TV, mafilimu, ndi mavidiyo zimalimbikitsa kukhumba zinthu zakuthupi. Ngakhale maseŵera oonerera ndi mipikisano yonenerera malonda imakhala ndi uthenga wakuti ndalama n’zofunika koposa pafupifupi chilichonse.

Tili Pamodzi Koma Tadzipatula

Kumayambiriro kwa zaka zana la 20, anthu ambiri anali kukhala m’madera a kumidzi. Akuti cha kumayambiriro kwa zaka zana la 21, anthu opitirira theka azidzakhala m’mizinda. Buku lotchedwa 5000 Days to Save the Planet (Masiku 5000 Kuti Tipulumutse Pulanetili) linati: “Ntchito yakuti anthu a m’mizinda, ndipo kwenikweni mibadwo yam’tsogolo, idzakhale ndi moyo wabwino, ikuoneka kuti n’njovuta kwambiri.” Magazini ya bungwe la UN yotchedwa World Health inati: “Chiŵerengero cha anthu padziko lonse amene akukhala m’mizinda chikukwera. . . . Anthu mamiliyoni mazana ambiri . . . tsopano ali m’mikhalidwe imene ili yovulaza thanzi lawo ndiponso yoika miyoyo yawo pachiswe.”

Choncho n’zopandadi phindu kuti ngakhale anthu akusamuka n’kukhala pamodzi m’mizinda, iwo akukhala modzipatula! Wailesi yakanema, matelefoni, ndi intaneti, pamodzi ndi kugula zinthu mongoitanitsa, ngakhale kuti n’zofunika, zimachotsa maubwenzi a pamaso m’pamaso. Choncho nyuzipepala ya ku Germany yotchedwa Berliner Zeitung ikuthirira ndemanga yakuti: “Zaka zana la 20 si zaka za kuchuluka kwa chiŵerengero cha anthu kokha komanso ndi zaka za kusukidwa.”

Zimenezi zimabweretsa masoka onga limene linachitika ku Hamburg, ku Germany, kumene mtembo wa munthu unapezeka m’nyumba mwake patatha zaka zisanu! “Palibe munthu amene anali kumusoŵa, ngakhale abale ake, kaya anansi ake kapenanso a boma,” ikutero magazini ya Der Spiegel, ndipo ikuwonjezera kuti: “Kwa nzika zambiri, nkhaniyi ikusonyeza kuti tsiku ndi tsiku anthu ambiri akusoŵana ndiponso kuti m’mizinda yaikulu anthu sayenderana.”

Chimene chikuchititsa mikhalidwe yoipa imeneyi si sayansi ndi tekinoloji yokha ayi. Kwenikweni akuchititsa ndi anthu. Zaka zana lino zakhala ndi anthu ochuluka kuposa kale lonse amene ali “odzikonda okha, okonda ndalama, . . . osayamika, . . . opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, . . . osakonda abwino, . . . okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.”—2 Timoteo 3:1-5.

1914, Chaka Chosonyezedwa Kale

Malingana ndi Winston Churchill, “kuyamba kwa zaka zana la 20 kunkaoneka ngati n’kwabwino ndiponso kwabata.” Anthu ambiri anali kuganiza kuti kubweretsa nyengo ya mtendere ndi kukhazikika kwakukulu. Komabe, mu 1905 magazini ya Watch Tower ya September 1 inachenjeza kuti: “Posachedwa kudzakhala nkhondo,” ndipo inanena kuti “nthaŵi yamavuto” aakulu idzayamba mu 1914.

Ndiponsotu, magazini imeneyi inali itatchulapo kale m’chaka cha 1879, kuti 1914 ndi chaka chapadera. M’zaka zotsatira inasonyeza kuti ulosi wa Baibulo m’buku la Danieli unasonyeza kuti m’chaka chimenechi ndi mmene Ufumu wa Mulungu anaukhazikitsa kumwamba. (Mateyu 6:10) Ngakhale kuti 1914 siinali nthaŵi yakuti Ufumuwu utengeretu ulamuliro wonse wokhudza zochitika za padziko, inali nthaŵi yakuti uyambe ulamuliro wake.

Ulosi wa Baibulo unaneneratu kuti: ‘m’masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu [kumwamba] woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse.’ (Danieli 2:44) Ufumu umenewo, wokhala ndi Yesu Kristu monga Mfumu, unayamba kusonkhanitsa anthu owopa Mulungu pano padziko lapansi amene anali kufuna kuti uwalamulire.—Yesaya 2:2-4; Mateyu 24:14; Chivumbulutso 7:9-15.

Pamodzi ndi zimene zinachitika kumwamba, chaka cha 1914 ndicho chinali chiyambi cha “masiku otsiriza,” kuyamba kwa nyengo imene idzatha ndi chiwonongeko cha dongosolo la zinthu limene lilipoli. Yesu analosera kuti kuyamba kwa nyengo imeneyi kudzadziŵika chifukwa cha nkhondo, njala, milili ya matenda, zivomezi zowononga, ndi kusaweruzika kochuluka ndiponso kuzilala kwa chikondi cha anthu kwa Mulungu ndi munthu mnzawo. Iye anati zinthu zonsezi, zidzadziŵikitsa ‘kuyamba kwa zowawa.’—Mateyu 24:3-12.

Posachedwapa Dziko Latsopanodi

Tsopano takwanitsa zaka 85 tili mu “masiku otsiriza,” ndipo tikuthamangira kumapeto kwa dongosolo la zinthu losasangalatsali. Posachedwapa Ufumu wa Mulungu, pansi pa ulamuliro wa Kristu, “udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44; 2 Petro 3:10-13.

Inde, Mulungu adzachotsa kuipa padziko lapansi ndipo adzaika anthu olungama padziko latsopanodi. “Pakuti owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko.”—Miyambo 2:21, 22.

Uthengawu ndi wosangalatsadi ndipotu n’ngwofunika kuulengeza ponseponse! Posachedwapa Ufumu wa Mulungu uchotsa mavuto amene achuluka m’zaka za zana la 20 zino: nkhondo, umphaŵi, matenda, chisalungamo, udani, kusalolerana, ulova, umbanda, kusasangalala, imfa.—Onani Salmo 37:10, 11; 46:8, 9; 72:12-14, 16; Yesaya 2:4; 11:3-5; 25:6, 8; 33:24; 65:21-23; Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:3, 4.

Kodi lingaliro lokhala kosatha m’dziko lolungama lachimwemwe chosaneneka limakusangalatsani? Funsani a Mboni za Yehova kuti akuuzeni zowonjezereka. Iwo adzakusonyezani kuchokera m’Baibulo lanu lomwelo kuti zaka zana la 20 zimene zakhala ndi kusintha kwakukulu zikutha posachedwapa ndipo patsogolo pake mungadzakhale ndi madalitso osatha!

[Chithunzi patsamba 10]

Dziko latsopanodi likudza posachedwapa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena