Kodi N’kupupuluma Kapena Kuzengereza?
PALI zonena zambiri zokhudza kuyamba kwa zaka za zana la 21 ndi kwa zaka chikwi zachitatu Yesu Kristu atabadwa. Magazini ya Newsweek inati “zaka za zana la 20, zimene zinayamba monga Zaka za Zana la Nkhondo Yoopsa ndipo zinafika pa Nyengo ya Zida za Atomu, zikuoneka kuti zikutha monga nyengo ya zosangalatsa.” M’kope lake la January 22, 1997, magazini imeneyi inanena kuti: “Zipinda za mahotela padziko lonse lapansi n’zogulidwa kale” kaamba ka chisangalalo cha patsiku lochingamira chaka chatsopano la December 31, 1999.
Komabe, anthu ena akuti chisangalalocho achipupulumira. Iwo amati anthu ambiri amakhulupirira molakwa, chifukwa zaka za zana la 21 ndiponso zaka chikwi zatsopano sizidzayamba pa January 1, 2000, koma pa January 1, 2001. Chifukwa chakuti panalibe chaka cha 0, zaka za zana loyamba zinayambira pa chaka cha 1 n’kuthera pa chaka cha 100, ndipo zaka za zana lachiŵiri zinayambira pa chaka cha 101 n’kuthera pa chaka cha 200, n’kumapita m’tsogolo. Motero amatsutsa ponena kuti zaka za zana la 20, zimene zinayamba pa January 1, 1901, ndipo zaka chikwi zachiŵiri, zimene zinayamba pa January 1 1001, sizidzatha mpaka pa December 31, 2000.
Palinso mfundo yowonjezereka imene tiyenera kupenda. Kalendala yathu imagaŵa nthaŵi mogwirizana ndikuti kaya Kristu anali asanabadwe kapena atabadwa. Tsopano ophunzira azindikira kuti Yesu anabadwa chambuyo mwake kuposa mmene anali kuganizira poyamba, motero pamene kalendalayo imayambira m’polakwa. Pali maganizo osiyana onena za chaka chimene Yesu anabadwa, koma kaŵerengedwe ka nthaŵi ka Baibulo kamasonyeza kuti chinali chaka cha 2 B.C.E. Malingana ndi kuŵerengera kumeneku, zaka chikwi zachitatu Kristu atabadwa kwenikweni zayenera kuyamba chaka chomwe chino! Chidziŵitso chowonjezereka mungachipeze m’makope achingelezi a Galamukani! a May 22, 1997, tsamba 28 ndi December 22, 1975, tsamba 27.a
Mulimonsemo, n’kwanzeru kupeŵa kunena motsindika kuti zaka za zana la 21 ndiponso zaka chikwi zatsopano ziyamba m’milungu ingapo chabe. Komabe, chifukwa chakuti pali malingaliro ambiri ofala, Galamukani! yaona kuti n’koyenera panthaŵi ino kulongosola nkhani imeneyi yakuti “Zaka za Zana la 20—Zaka za Kusintha Kwakukulu.”
[Mawu a M’munsi]
a Onaninso kope la Nsanja ya Olonda ya November 1, 1999.