Zaka Chikwi Zachitatu—Kodi Zidzakwaniritsa Ziyembekezo Zanu?
KUŴERENGA nthaŵi yotsala kwayambika. Koloko ya dijito yokhala kutsogolo kwa bwalo lamaseŵera lamwambo ya Beaubourg mu Paris, Falansa, ikusonyeza timphindi timene tatsala. Iyo idzapitirizabe kupyola m’mphindi zotsalazo popanda kuima kufikira pakati pausiku pa December 31, 1999. Panthŵiyo, chinthu chomwe chinachitikapo kamodzi kokha m’Nyengo Yathu Ino chidzachitika: kufika kwa zaka chikwi zatsopano, zaka chikwi zachitatu.
“2000, m’njira inayake, iri ‘chochitika chachikulu choyembekezeredwa’ chikhalire m’mbiri ya anthu,” akulingalira tero Bernward Joerges wofufuza zamayanjano a anthu wa ku Berlin, Jeremani. Kodi pakhaliranji chiyembekezo choterocho? Ndiiko komwe, chaka cha 2000 chiri chabe deti lina m’nyengo ya nthaŵi. Ndiponso, detilo likuzindikiridwa ndi otsatira kalenda ya Kumadzulo okha. Mogwirizana ndi kalenda ya Chisilamu, 2000 C.E ikufika mkati mwa chaka Chachisilamu cha 1420; mogwirizana ndi kalenda Yachiyuda, 5760 A.M.
Koma pofunsidwa m’nyuzipepala ya ku Sweden ya Dagens Nyheter, Profesa Joerges akulongosola izi: “Chifukwa cha utsamunda ndi ulamuliro wotsendereza, kuŵerengera kwathu zaka kotsatira Gregory, koyambira ndi lolingaliridwa kukhala tsiku lakubwadwa kwa Kristu, kwalandiridwa m’mbali zambiri zadziko.” Motero chaka cha 2000 chidzakhala chopanga mbiri kwa anthu ochuluka padziko lonse. Profesa Joerges akuti: “Anthu onse adzagwirizanitsa mbiri zawo zaumwini limodzi ndi china chirichonse ku chochitikachi.”
Komabe, ambiri ali ndi zambiri m’maganizo zoposa kuzindikira nthaŵi kokha. “Maprojekiti aakulu ndi maprogramu ‘odzazindikiritsa’, kulemekeza ndi kukondwerera chochitikachi anayambika kale m’zochitika zonse za moyo ndi pa miyezo yonse ya magulu a anthu,” akutero Joerges. Iye akuwonjezera kuti “padziko lonse, akuluakulu amakampani olinganiza maprojekiti ndi ‘akatswiri a zamaseŵera’ akulingalira ndi kukonza zochitika zazikulu.” Oneneratu zamtsogolo ena akuti “tidzamizidwa ndi kuchuluka kwa mabuku onena za zaka za zana lapita. Ofalitsa nkhani onse adzakhala yakaliyakali kusimba za kufika kwa zaka chikwizo. Nyumba yawailesi ya TV Kumadzulo kwa Jeremani ikukonzekera kufalitsa kutuluka kwa dzuŵa m’maola 24 pa dziko lonse lapansi.”
Ofalitsa nkhani adzatsimikiziranso kuthokoza kwambiri mwana womalizira kubadwa mu 1999 ndi woyamba kubadwa mu 2000. Amtola nkhani adzalakalaka kufunafuna otsala oŵerengeka obadwira m’zaka zana la 19 kuti awafunse mmene akumverera kukhala ndi moyo m’zaka mazana atatu ndi zaka zikwi ziŵiri! Ena akulingalira kuti chiphwete cha m’zaka chikwi chonsechi chidzabweretsa chipwirikiti kwa anthu ambiri. Mogwirizana ndi kulosera kwina kodetsa nkhaŵa, pofika pakati pausiku pa Tsiku Lotsatira Chaka Chatsopanolo, ambiri adzadzipha.
Mosasamala kanthu za kupambanitsa kotsimikizirika koteroko, nzomveka kuti chochitikacho chikudzutsa chidwi. Kwa ambiri m’dziko lathu lodzala ndi mavuto iri, zaka chikwi zatsopanozo zikulingaliridwa kukhala zodzetsa chiyembekezo, poyambira mtsogolo mwabwinopo. Ena amayembekezera sayansi ndi luso la zopangapanga kudzetsa mtsogolo mmene tidzadya bwinopo ndi kukhala kwa nthaŵi yaitali, kugwira ntchito kwa nthaŵi yochepa ndi kukhala panyumba nthaŵi zambiri; kumene maroboti adzatimasula ku ntchito zogwetsa ulesi; kumene kusungunula kolamuliridwa kudzasintha madzi kukhala mafuta oyendetsera magalimoto. Akuwona mtsogolo mokhala TV yokopa yokha, Mafoni osonyeza chithunzithunzi cha wolankhula naye, makina a fax a zinthunzi zamitundumitundu, ndi matelefoni otembenuza chinenero pokambirana. Iwo amalota za kukazonda Mwezi, Mars, kapena zinthu zina zakuthambo, kukakumba chuma chawo.
Koma sionse omwe ali achidaliro motero. Ofufuza ena akulingalira zaka chikwi zatsopanozo kukhala zikubweretsa nyengo ya kukula kosalamulirika kwa chiŵerengero cha anthu ndi kunyonyotsoka kwa malo okhalamo. Kuipitsa mpweya kudzasintha dziko lapansi kukhala ng’anjo yowotcha. Madzi owundana adzasungunuka ndipo nyanja zidzadzala, kusefukira m’malo achonde, okhalidwa ndi anthu koma kusintha mamiliyoni a maekala a dziko kukhala zipululu. Iwo akuwoneratu kugwa kwa chuma chadziko, kutekeseka kwa ndale zadziko kumene kudzagwedeza maboma ndi zitaganya, upandu wauchigaŵenga, ndipo choipitsitsa pa zonse, chipiyoyo cha nyukliya chimene chidzapululutsa moyo wonse wa anthu.
Ponena za zaka chikwi zikudzazo oneneratu za kutsogolowo afulumira ndi nthabwala zawo koma samatsimikizira za kuyandikira kwake. Pali zosawonedweratu zambirimbiri zoloŵetsedwamo m’kuneneratu mtsogolo m’njira yolongosoka. Katswiri wa zamtsogolo akufananiza kuchita tero ndi kuseŵera nsolo: “Ndisanayendetse mwana wansolo, ndimaganizira njira zomwe ndingathe kuyenda. Koma mnzanga atangoyendetsa mwana wake, ndimayambanso kuganiza konseku.”
Nthaŵi yokha ndiyo idzanena zimene chaka cha 2000 chiri nazo. Komabe, ichi sichikutanthauza kuti mtsogolo mwanu muli mosatsimikizirika. Baibulo limapereka umboni wokwanira wakuti tayandikira kufika kwa zaka chikwi zofunika kwambiri koposa zimene zidzayamba pambuyo pa zaka zosakwanira khumi zikudzazo. Zaka Chikwi zomwe zikuyandikirazi zidzapambana kutalitali ziyembekezo zirizonse za anthu! Kodi ichi kwenikweni chikutanthauzanji? Kodi zidzaphatikizaponji? Tikukupemphani kulingalira nkhani yathu yotsatira ndi kuphunzira zimene Baibulo limanena.