Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 11/1 tsamba 3-4
  • Kodi Chaka cha 2000 N’chapadera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chaka cha 2000 N’chapadera?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Zaka za Chikwi Chachitatu Zidzayamba Liti?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Chaka cha 2,000 Chidzawakhudza Bwanji Anthu?
    Galamukani!—1998
  • Zaka Chikwi Zachitatu—Kodi Zidzakwaniritsa Ziyembekezo Zanu?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi N’kupupuluma Kapena Kuzengereza?
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 11/1 tsamba 3-4

Kodi Chaka cha 2000 N’chapadera?

KODI pali china chilichonse chapadera ponena za chaka cha 2000? Anthu ambiri okhala m’mayiko a Kumadzulo amaona chakachi ngati chaka choyamba cha m’zaka za chikwi chachitatu. Kukonzekera zodzachita pa chikondwerero cha chakacho kuli mkati. Mawatchi akuluakulu oyendera mphamvu zamagetsi akuikidwa kuti adzaŵerenge masekondi mpakana mbandakucha wa m’zaka chikwi zatsopanozo. Madansi okonzekera kuloŵa chaka chatsopano akukonzedwa. Masikipa olembedwa mawu osonyeza kutha kwa zaka chikwi akugulitsidwa m’sitolo za m’matauni ang’onoang’ono ngakhalenso m’malo a zamalonda m’mizinda ikuluikulu.

Matchalitchi aakulu ndi aang’ono omwe, adzachita nawo mapwando a chaka chonse. Kumayambiriro a chaka chamaŵa, Papa Yohane Paulo wachiŵiri, akuyembekezeka kupita ku Israyeli komwe akatsogolere a Roma Katolika pa mwambo womwe ukutchedwa kuti “chikondwerero chapadera cha Tchalitchi cha Roma Katolika cha m’zaka chikwi.” Akulingalira kuti alendo apakati pa 2,500,000 ndi 6,000,000, akukonzekera kupita ku Israyeli chaka chamaŵa, ena chifukwa cha chikhulupiriro chawo ndipo ena chifukwa chochita chidwi ndi zomwe zikachitika kumeneko.

N’chifukwa chiyani anthu ambiri chonchi akukonzekera kupita ku Israyeli? Polankhula m’malo mwa Papa, Kadinala Roger Etchegaray, wa ku Vatican komweko anati: “Chaka cha 2000, n’choti tikondwerere Kristu ndi moyo wake wam’dziko lino. Choncho n’koyenera kuti Papa abwere kuno.” Kodi chaka cha 2000 chikugwirizana bwanji ndi Kristu? Anthu akulingalira kuti chaka cha 2000 padzakhala kuti patha zaka 2,000 kuchokera pamene Kristu anabadwa. Koma kodi ndi zoona? Tiona kutsogoloku.

Mamembala a magulu ena a zipembedzo, amaona chaka cha 2000 kukhala chofunika zedi. Amakhulupirira kuti mkati mwa chaka chamaŵa kapena patsogolo pake, Yesu adzabwerera ku phiri la Azitona ndipo nkhondo ya Armagedo, yonenedwa m’buku la Chivumbulutso, idzaulika m’chigwa cha Megido. (Chivumbulutso 16:14-16) Poyembekezera zochitika zimenezi, anthu mazanamazana ku United States, akugulitsa nyumba zawo ndi katundu wawo wambiri ndipo akusamukira ku Israyeli. Kuti athandize ena amene sangathe kusiya nyumba zawo, mlaliki wina wotchuka ku United States akuti walonjeza kuti adzaonetsa kubwera kwa Yesu pa wailesi yakanema.

M’mayiko a Kumadzulo, kukonzekera kuloŵa m’zaka za chikwi chachitatu kukuwonjezereka. Komabe, anthu m’mayiko ena akupitirizabe ntchito zawo za masiku onse. Anthu ameneŵa, omwe ndi chiŵerengero chochuluka cha anthu apadziko lapansi, sakhulupirira kuti Yesu wa ku Nazarete anali Mesiya. Ndiponso samavomereza kaŵerengedwe ka madeti ka B.C.-A.D.a Mwachitsanzo, Asilamu ambiri, amagwiritsa ntchito kalendala yawoyawo. Malinga ndi kalendala imeneyi, chaka chamaŵa chidzakhala 1420, osati 2000. Asilamu amaŵerenga zaka kuyambira deti limene mneneri Muḥammad anathaŵa ku Mecca kupita ku Medina. Mwachidule, anthu dziko lonse amagwiritsa ntchito makalendala 40 osiyanasiyana.

Kodi chaka cha 2000 chiyenera kukhala chatanthauzo kwa Akristu? Nanga January 1, 2000, ndi tsiku lofunika kwambiri? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a M’kaŵerengedwe ka madeti ka B.C.-A.D., zinthu zomwe zinachitika Yesu asanabadwe zimalembedwa kuti zinachitika m’zaka za m’ma “B.C.” (Kristu asanadze); zomwe zinachitika pambuyo pake zimalembedwa kuti zinachitika m’zaka za m’ma “A.D.” (Anno Domini​—“m’chaka cha Ambuye wathu.”) Komabe, ophunzira ena amadigiri amakonda kugwiritsa ntchito kalembedwe ka anthu wamba ka “B.C.E.” (Nyengo Yathu isanafike) ndi “C.E.” (za M’nyengo Yathu.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena