Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g01 3/8 tsamba 22-25
  • Kodi Mukufunikira Inshuwalansi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukufunikira Inshuwalansi?
  • Galamukani!—2001
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mitundu ya Inshuwalansi
  • Kupeza Makampani a Inshuwalansi Odalirika
  • Ntchito ya Alangizi a Inshuwalansi
  • Inshuwalansi ndi Akristu
  • Malonda Akale Kwambiri
    Galamukani!—2001
  • Inshuwalansi Imene Aliyense Amafunikira
    Galamukani!—2001
  • Kodi Kuchita Zimenezi N’kusaonadi Mtima?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kuba Anthu—Malonda Oopsa
    Galamukani!—2000
Onani Zambiri
Galamukani!—2001
g01 3/8 tsamba 22-25

Kodi Mukufunikira Inshuwalansi?

M’MAYIKO ena ndi lamulo kudula mitundu inayake ya inshuwalansi. M’mayiko enanso, mitundu yambiri ya inshuwalansi n’njosadziŵika n’komwe. Kuphatikizanso apo, mtengo wa inshuwalansi ndiponso mtundu wa zinthu zimene ingalipirire zimasiyana kwambiri m’mayiko osiyanasiyana. Koma mfundo yaikulu ya inshuwalansi, yomwe n’kuthandizana patsoka, ndi yomweyo.

Kaŵirikaŵiri, munthu akakhala ndi katundu wambiri, ndiye kutinso tsoka litam’gwera amataya zambiri. Chonchonso ngati munthu ali ndi udindo waukulu wa banja, vuto limakula kwambiri iyeyo akafa kapena kulemala. Kukhala ndi inshuwalansi kungachepetse nkhaŵa imene munthu angakhale nayo yotaya katundu kapena yochita ngozi yolemaza.

Koma kodi n’kwanzeru kuwonongera ndalama polipira inshuwalansi ngakhale kuti mwina simungadzafune chipukutira misozicho? Chabwino, kodi kusunga tayala lapadera m’galimoto, ngakhale litapanda kufunika, n’kungowononga chabe zinthu? Ngati woyendetsa galimotoyo akumva kuti ali m’podalira ndiye kuti n’kwaphindu kutenga tayala lina. Ngakhale kuti chipukutira misozi sichingathe kubwezeretsa zotayika zina, chingathe kuthandiza pa zotayika zina.

Kodi ndi zotayika zotani zimene mapangano a inshuwalansi amakhudza?

Mitundu ya Inshuwalansi

Mainshuwalansi ambiri amene anthu amadula ali m’gulu la inshuwalansi ya katundu, milandu, thanzi, kulemala, ndi moyo.

Inshuwalansi ya katundu: Kudula inshuwalansi yoteteza katundu monga nyumba, bizinesi, galimoto, kapena katundu wina kuli m’gulu la mitundu yofala kwambiri ya kukonzekera masoka. Imeneyi ndiyo inshuwalansi imene John, tam’tchula m’nkhani yoyamba ija, ananyalanyaza kudulira shopu yake yopala matabwa ndiponso zida zake.

Mapangano ena a inshuwalansi ya nyumba amatetezanso katundu wina wa m’nyumba. Mukadula inshuwalansi yotereyi, n’kwanzeru kulemba mndandanda wa katundu yense wa m’nyumba amene mwadulira inshuwalansiyo ndipo ngati n’kotheka musunge zithunzi zake kapena kujambula katunduyo patepi ya vidiyo. Mndandandawo pamodzi ndi makalata alionse osonyeza mtengo wa katunduyo kapena malisiti ake muyenera kuzisunga pamalo otetezeka, osati m’nyumbamo. Kukhala ndi maumboni ameneŵa kungafeŵetse kwambiri ntchito yofunsira ndalama zimene a inshuwalansi ayenera kukupatsani.

Inshuwalansi ya milandu: Munthu aliyense amene amayendetsa galimoto, amene ali ndi nyumba kapena malo, amachita bizinesi, kapena amene ali ndi antchito angapezeke ndi mlandu wa ngozi. Ndipo ngoziyo ingawonongetse katundu kapena kupweteketsa munthu ngakhalenso kumupheratu. Woyendetsa galimoto kapena mwinikatundu kapena bizinesiyo angalipitsidwe kuti akonzetse zowonongekazo kapena chithandizo cha mankhwala ngakhalenso ululu ndiponso kuvutika kumene mnzakeyo wamva. M’mayiko ambiri enintchito ndiponso oyendetsa galimoto, boma limawalamula kukhala ndi inshuwalansi ya milandu kuti athe kulipirira zinthu zoterezi. Ngakhale kumene boma silimafuna inshuwalansi, woyendetsa galimoto, mwinikatundu, kapena mwinintchito angakhale ndi mlandu malinga ndi malamulo kapena chikhalidwe chawo woti athandize ovulala pangozi kapena mabanja awo.

Inshuwalansi ya thanzi: Mayiko ambiri amakhala ndi mitundu ina ya inshuwalansi imene boma limapereka kuthandiza achikulire pa zinthu monga penshoni ndiponso chithandizo chamankhwala. Komabe ngakhale m’mayiko otere, inshuwalansi yotere ingalipirire gawo lochepa chabe la ndalama zolipirira chipatala kapenanso mwina ingalipirire zithandizo zina chabe. Motero anthu ena amadula inshuwalansi yawoyawo yapadera kuti iwathandize kulipirira kotsalako. M’malo ambiri antchito amalandira inshuwalansi ya thanzi. Imeneyi ndi mwayi umene amakhala nawo monga wolembedwa ntchito.

Njira zina zothandizira pa nkhani ya thanzi, kuphatikizapo makonzedwe othandizidwa ndi mabungwe ndiponso magulu oyang’anira zaumoyo otchedwa (HMO), zimapereka chithandizo chokwanira bwino polipira mtengo winawake wa ndalama pa mwezi kapena chaka chilichonse. Mabungwe ameneŵa amayesetsa kutsitsa mitengo popereka chithandizo chotsika ndi polimbikitsa mankhwala oteteza matenda. Komabe, m’magulu a HMO, wodwala sasankha dokotala kapena chithandizo momasuka ngati mmene angachitire ndi inshuwalansi ya thanzi yanthaŵi zonse.

Inshuwalansi ya kulemala ndi inshuwalansi ya moyo: Inshuwalansi ya kulemala imapereka ndalama munthu akavulala moti sangathenso kugwira ntchito. Inshuwalansi ya moyo imapereka chithandizo cha ndalama kwa odalira munthuyo ngati iye atamwalira. Inshuwalansi yotereyi yathandiza mabanja ambiri kulipira ngongole ndi kukhalabe moyo wa masiku onse munthu amene ankadalira atavulala kapena kumwalira.

Kupeza Makampani a Inshuwalansi Odalirika

Cholinga cha inshuwalansi n’chakuti mumapereka ndalama kuti zidzakuthandizeni m’tsogolo, choncho sizodabwitsa kuti malonda a inshuwalansi amakopa akuba ambiri. Zimenezi zimachitika m’mayiko achuma ndi osauka omwe. Motero, munthu ayenera kuchenjera ndi inshuwalansi yotsika mtengo ndiponso kusamala ndi inshuwalansi iliyonse yokayikitsa. Ambiri okhulupirira zimenezi analuza zonse makampani ameneŵa atalephera kuwapatsa chipukutira misozi chimene amalonjeza kapena atangozimiririka!

Motero, n’kwanzeru kuyerekezera kaye ndi kwina monga mumachitira pogula chinthu chilichonse chofunika, ndipo nthaŵi zambiri mukatero mumapulumutsa ndalama. Mwachitsanzo, makampani ena amatsitsa mtengo wa inshuwalansi ya moyo kwa osasuta fodya ndi ya galimoto kwa amene anakhoza udalaivala. Koma kodi munthu amene akufuna kudula inshuwalansi angaipeze bwanji yodalirika?

Choyamba fufuzani zimene ena apezana nazo kumakampani osiyanasiyana a inshuwalansi ndiponso alangizi awo. Anzanu ndiponso anansi angadziŵe mbiri ya mmene kampaniyo imathandizira anthu kapenanso ngati alangiziwo ali ndi mbiri yakuti n’ngokhulupirika ndiponso osamala anthu. Ndi bwinonso kukhala tcheru pomvetsera nkhani zonena za makampani a inshuwalansi amene ali m’mavuto.

Kuphatikizanso apo, mbiri ya kampani ndiponso mmene chuma chake chilili mungathe kuzitsimikizira pofufuza m’mabuku oonetsa mainshuwalansi ochita bwino ku laibulale kapena kusitolo ya mabuku kapenanso pa Intaneti. Zinthu zimenezi zingayankhe mafunso monga akuti: Kodi kampaniyo chuma chake n’chokhazikika? Kodi yakhala ikuchita bwino bizinesi kwa zaka zambiri? Kodi n’njodziŵika kuti imathandiza msanga ndiponso mwamtendere?

Komabe musaganize kuti mabuku oonetsa mainshuwalansi ochita bwino ali osalakwitsa. Boma lina linalanda kampani ina yolemera kwambiri ya inshuwalansi patangotha mlungu umodzi buku lina lodziŵika bwino litati ndi yambambande!

Ntchito ya Alangizi a Inshuwalansi

Mlangizi wa inshuwalansi nthaŵi zambiri amatumikira kampani imodzi ya inshuwalansi. Mlangizi wodziimira payekha, amatha kukambirana ndi makampani osiyanasiyana kuti apeze inshuwalansi yabwino kwambiri pamtengo umene watchulidwa. Onsewa ayenera kugwirizana ndi makasitomala awo kuti apitirire kuchita bizinesiyi. Mlangizi wa inshuwalansi akakhala wokhulupirika ndiponso wosamala anthu, angawathandize kwambiri makasitomala ake.

Choyamba, alangizi abwino oterewa angathandize makasitomala awo kusankha inshuwalansi yoyenerera pa mainshuwalansi ambiri. Ayeneranso kulongosola bwinobwino mfundo zake kwa kasitomala wakeyo. Anthu ambiri akudziŵa kale kuti mfundo za inshuwalansi n’zovuta kwambiri kuzimvetsa. Pulezidenti wina wa kampani ya inshuwalansi anavomereza kuti sanali kumvetsa mbali zina za mfundo za inshuwalansi imene anadulira nyumba yake!

Zimene mlangizi angalongosole zingathandize kasitomala kupeŵa mavuto osayembekezeka. Mwachitsanzo, mainshuwalansi ambiri a katundu ndiponso thanzi amakhala ndi ndalama zochotsera. Zimenezi ndi ndalama zoikika zimene munthu amene wadula inshuwalansi ayenera kupereka—mwachitsanzo, pokonzetsa galimoto kapena kulipirira chipatala—kampani ya inshuwalansiyo isanalipire mbali yake. Mlangiziyo angakhalenso monga nkhoswe ku kampani ya inshuwalansiyo ngati kasitomalayo akuvutika kuti am’lipire.

Inshuwalansi ndi Akristu

Kodi Mkristu wokhulupirira kuti Mulungu amathandiza ndipo akuyembekezera kutha kwa dongosolo lino la zinthu akufunikira inshuwalansi? Kale mu 1910, anthu ena anam’funsa funso limeneli Charles Taze Russell, mkonzi wa magazini imene tsopano imadziŵika kuti Nsanja ya Olonda, inzake ya magazini ya Galamukani! Russell anati Baibulo limaneneratu za kutha kwa dongosolo la zachuma lilipoli, ndipo ananenanso kuti iyeyo payekha analibe inshuwalansi ya moyo.

Russell anatinso “Komabe zinthu zimasiyana kwa munthu aliyense. Bambo amene mkazi ndi ana ake amamudalira, ndipo ngati anawo ali aang’ono ndiponso osatha kudziyang’anira, ali ndi udindo pa iwo.” (1 Timoteo 5:8) Munthu angathe kusunga ndalama zothandizira banja lake, Russell anatero. “Koma ngati sangathe kutero, angathe kukwaniritsa udindo wake kwa iwo podula inshuwalansi ya moyo.”

Munthu wosamala banja lake angadulirenso banjalo inshuwalansi ya thanzi, kulemala, ndiponso ya mitundu ina. Anthu ambiri amene sanaloŵe m’banja amakhala ndi inshuwalansi kuti athe kupeza chithandizo chimene akufuna komanso kuti adziteteze ku ngongole ngati atachita ngozi kapena atadwala.

Kuona mtima n’kofunikanso pankhani za inshuwalansi. Mkristu woona sanganamize kampani ya inshuwalansi, kaya posaina pepala lofunsira inshuwalansi kapena pofunsira chipukutira misozi. (Ahebri 13:18) Iye ayenera kukumbukira kuti cholinga cha inshuwalansi ndicho kupereka chipukutira misozi pa zinthu zikawonongeka. Si tikiti yowinira mpikisano kuti ukhale mpondamatiki.—1 Akorinto 6:10.

Akristu amamvera malamulo onse okhudza zimene ayenera kuchita pa zinthu monga kudula inshuwalansi. Kumene lamulo limati ayenera kukhala ndi inshuwalansi yoyenera kuti azichita bizinesi kapena kuyendetsa galimoto, iwo amamvera. (Aroma 13:5-7) Kuti tikhale oona mtima ndiponso anzeru tiyeneranso kusaiŵala kupereka ndalama mwezi ndi mwezi ku kampani yathu ya inshuwalansi. Ngati sititero, kampaniyo ingathetse panganolo ndi kusatipatsa ndalama zinthu zathu zikawonongeka. N’kwanzeru kutsimikizira nthaŵi ndi nthaŵi ndalama zimene mukupereka pokaona nokha kukampaniyo ndiponso kusunga umboni wolembedwa, monga macheke amene munagwiritsa ntchito polipira.

Kaya kumene mukukhala kuli inshuwalansi kapena ayi, pali zinthu zingapo zimene mungachite zokuthandizani kupewa tsoka ndiponso kusauka mtima inuyo ndi banja lanu kumene inshuwalansi iliyonse singakuthetse. Tsopano tiona zina mwa zinthu zofunika kuchitazo.

[Chithunzi patsamba 25]

Mlangizi wokhulupirika angakuthandizeni kusankha inshuwalansi

[Chithunzi patsamba 25]

Anthu ambiri amakhala ndi inshuwalansi, kaya mochita kulamulidwa ndi boma kapena ayi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena