Inshuwalansi Imene Aliyense Amafunikira
KAYA mumakhala kumene inshuwalansi ili yofala kaya kumene kulibe, pali mtundu wina wa inshuwalansi umene aliyense angakhale nawo ndipo ayenera kupeza. Popeza mawu akuti “inshuwalansi” amatanthauzanso “njira yotsimikizira kuti ndinu wotetezeka,” mungathe bwanji kupeza inshuwalansi yamtundu umenewo?
Pochitapo kanthu kuchepetsa tsoka. Baibulo limanena kuti “nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika” zimakhudza aliyense. (Mlaliki 9:11, NW) Komatu posaputira dala tsoka, tingachepetse kuchita ngozi kapena kutaya zinthu.
Ganizirani M’tsogolo
Kukhala ndi nzeru zabwino kumateteza. Zinthu zikamayenda bwino, mungasunge kangachepe kodzakuthandizani m’tsogolo zinthu zikadzavuta. Kale Yosefe, munthu woopa Mulungu, anasonyeza kuti anali “munthu wakuzindikira ndi wanzeru” posunga chakudya cha dziko lonse la Aigupto panthaŵi ya mwanaalirenji. Pamene m’dzikomo munadzakhala njala, ntchito yake imeneyi inathandiza Aigupto ngakhalenso banja lake.—Genesis 41:33-36.
Kusasakaza ndalama ndi njira inanso yodziteteza. Tingasunge ndalama ndiponso kuchepetsa nkhaŵa posafuna nthaŵi zonse kungogula katundu, zovala, ndi zinthu zina zosangalatsa zamakono, zimene sizithandiza kwenikweni kapena kutiteteza. Kwenikweni, monga tanenera kale, munthu akakhala ndi katundu wambiri, amakhalanso ndi tsoka lalikulu lakuti aberedwa kapena atayapo wina.—Luka 12:15.
Samalani
Tingachepetse ngozi zambiri m’moyo pokhala osamala basi. Kodi ndi ngozi zoopsa zingati za galimoto zimene tikanapeŵa ngati aliyense amayendetsa mosamala ndiponso paliŵiro labwino? Ganiziraninso za anthu amene akanapulumuka ngati pakanapanda munthu woyendetsa galimoto atatopa kwambiri kapena ataledzera. Ziliponso zinthu zina zangozi zokhudza kuyendetsa galimoto zimene tingapeŵe.
Mwachitsanzo, m’mayiko ambiri lamulo limaletsa kugwiritsa ntchito matelefoni a serula poyendetsa galimoto. Ofufuza ena anapeza mfundo yakuti kuchita zimenezi kumawonjezera kwambiri mpata wochita ngozi. Motero mpatawu n’ngwaukulu mofanana ndi kuyendetsa galimoto utamwa moŵa, ndipo m’mayiko ambiri lamulo limaletsa munthu woledzera kuyendetsa galimoto.
Kumanga malamba nthaŵi zonse nakonso kumapeŵetsa imfa ya madalaivala ndi mapasinjala. Koma osadzinamiza kuti mukakhala ndi zinthu zoteteza monga malamba ndiponso zimipira za mpweya kapena inshuwalansi ndiye kuti palibe choopsa ngati mutadziika dala pangozi. Ofufuza akuti maganizo otere amawonjezera ngozi.
Kukhala osamala kaya m’pakhomo kaya n’kuntchito ndi inshuwalansi yabwinonso. Kodi malo anu okhala ndi ogwirako ntchito ndi osamalika ndiponso opanda zovulaza? Taunguzaniunguzani. Kodi pali chilichonse chotchinga njira chimene anthu angathe kukodwamo? Kodi zinthu zakuthwa kapena zotentha—monga chitofu, mbaula, aironi—zili pamalo amene anthu angathe kuchekedwa kapena kuwotchedwa nazo? Kodi penapake paunjikika mapepala kapena zinthu zina zoyaka? Khalani atcheru kwambiri kuti pasakhale zinthu zovulaza ana. Mwachitsanzo, kodi moŵa ndiponso mankhwala onse oopsa ochapira zili posafikira ana aang’ono?
Samalani Thanzi Lanu
Poganizira thanzi lanu moyenerera, mungathe kuchepetsa mpata wodwaladwala. Apanso, kudziŵa zinthu kungakhale ngati inshuwalansi. Dziŵani zinthu zowononga thanzi lanu, ndipo chitanipo kanthu mwamsanga pakabuka mavuto athanzi. Chofunika kwambiri n’chakuti muphunzire kusamalira thanzi lanu ndiponso la banja lanu. Kumbukirani mwambi wakuti: “Kupeŵa kumaposa kuchiza.”
Kuyambira kale Galamukani! yakhala ikusimba nkhani zolimbikitsa anthu kuti azitsata mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo ndi kupeŵa zizoloŵezi ndiponso makhalidwe owononga thanzi. Mwachitsanzo, zina mwa nkhani zambiri zimene zapendedwapo mu Galamukani! ndi monga za kufunika kwa udongo, kudya moyenera, kugona mokwanira, ndiponso kuchita maseŵera olimbitsa thupi kaŵirikaŵiri komanso ubwino wa kuchepetsa maganizo ndiponso kupeŵa moyo wotanganidwa kwambiri.
Mtundu Wofunika wa Inshuwalansi
M’dziko lopanda ungwiroli, inshuwalansi ingakhale yothandiza kwambiri, koma palibe inshuwalansi iliyonse imene ingatitetezeretu kapena kutipatsa chipukuta misozi chonse pa katundu yense amene wawonongeka. Komabe, pali anthu ena amene sakayika kuti ngakhale atapanda inshuwalansi, sangasiyidwe paokha. Chifukwa? Chifukwa chakuti pakakhala mavuto, otsatira oona a Yesu Kristu, amene amatumikira Atate wake, Yehova Mulungu, amayesetsa kuthandizapo pa mavuto a anzawo.—Salmo 83:18; Yakobo 2:15-17; 1 Yohane 3:16-18.
Kuphatikizanso apo, Yehova mwini amalonjeza kuti sadzasiya atumiki ake okhulupirika. Wamasalmo a Baibulo analemba kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Salmo 27:10) Monga Gwero la moyo, Yehova angathe kuutsa anthu amene amafa, ndipo malingana ndi Baibulo, wapatsa mphamvu Mwana wake, Yesu Kristu, youtsa akufa. (Salmo 36:9; Yohane 6:40, 44) Komatu, Mawu a Mulungu amasonyeza kuti si aliyense adzaukitsidwe. (Yohane 17:12) Motero, kodi tingatani kuti titsimikizire zakuti Mulungu adzatikumbukira poukitsa akufa?
Pa Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri, Yesu kwenikweni anakambapo za mtundu wa inshuwalansi yodalirika kwambiri. Iye ananena kuti: “Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: koma mudzikundikire nokha chuma m’mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.”—Mateyu 6:19-21.
Nthaŵi zambiri anthu amalingalira zopeza chuma chambiri poganiza kuti chidzawapatsa moyo wabwinopo akamakalamba. Koma Yesu anatchula mtundu wodalirika kwambiri wa inshuwalansi. Mtengo wake n’ngwosaneneka, ndipo mtunduwu n’ngwosati n’kukanika! Iye analongosola kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.”—Yohane 17:3.
Pokhala ndi chidziŵitso cholondola ponena za Mulungu ndi Mwana wake ndiponso pogwiritsa ntchito pamoyo wathu zimene timaphunzira, tidzakhala ndi mbiri yabwino kwa Mulungu. (Ahebri 6:10) Mtumwi Petro ndi Yohane, amene zikhulupiriro zawo zinazikidwa pa ziphunzitso za Mbuye wawo, Yesu Kristu, anagogomeza kuti dongosolo la ulamuliro wa anthu lilipoli lidzatha. Koma, Yohane analongosola kuti: “Iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”—1 Yohane 2:17; Mateyu 24:3, 14; 2 Petro 3:7, 13.
Tingakhale ndi chidaliro chakuti ngati titumikira Mulungu ndipo tifa, angadzatiukitse kapena ngati tikhalabe ndi moyo mpaka pamene adzawononga dongosolo lino la zinthu, adzatisunga n’kutiloŵetsa m’dziko lake lolungama latsopano tili moyo. N’zoonadi, lonjezo la Mulungu n’lakuti ‘adzatipukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pathu’ ndi ‘kuchita zonse zikhale zatsopano.’ (Chivumbulutso 21:4, 5) Kutumikira Mulungu ndi kukhulupirira malonjezo ake ndiyodi inshuwalansi yabwino koposa. Ndipo aliyense angathe kukhala nayo.
[Zithunzi pamasamba 26, 27]
Kusamala kupeŵa ngozi ndiponso thanzi ndi mtundu wina wa inshuwalansi
[Chithunzi patsamba 28]
Kuphunzira za Mulungu ndi kuchita chifuniro chake ndiyo inshuwalansi yabwino kwambiri yam’tsogolo