Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g01 6/8 tsamba 28-29
  • Kodi Kupulula Anthu Kungadzachitikenso?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kupulula Anthu Kungadzachitikenso?
  • Galamukani!—2001
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Sizikukhudza Ayuda Okha
  • Mboni za Yehova Panthaŵi Yopulula Anthuyi
  • Mmene a Mboni za Yehova Amaonera Nkhani ya Kuphedwa Kwa Ayuda Ambirimbiri mu Ulamuliro wa Chipani Cha Nazi—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nkhani Zina
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Analola Kuti Anthu Ambirimbiri Aphedwe mu Ulamuliro wa Nazi ku Germany?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kuvumbula Zoipa za Nazi
    Galamukani!—1995
  • Okhulupirika Olimba Mtima Anapambana Chizunzo cha Nazi
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—2001
g01 6/8 tsamba 28-29

Kodi Kupulula Anthu Kungadzachitikenso?

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SWEDEN

PA January 26 mpaka 28, m’chaka cha 2000, atsogoleri a mayiko ndi nthumwi zina zaboma 48 zam’mayiko osiyanasiyana zinasonkhana kulikulu la dziko la Sweden pamsonkhano wamayiko onse wotchedwa Stockholm International Forum on the Holocaust. Zimene anthu ena ananena pamsonkhanowu zinavumbula mantha amene atsogoleri amayiko ali nawo akuti khalidwe la chipani cha Nazi lingadzayambirenso. Nduna yaikulu yakale ya dziko la Israyeli, a Ehud Barak anati: “Msonkhano uno ukufuna kudziŵitsa dziko lonse zakuti: Tisadzalekelerenso ulamuliro uliwonse wankhanza, wakupha anthu ndiponso watsankho pa zifukwa za chipembedzo, mtundu kapena khungu.”

Sizikukhudza Ayuda Okha

Anthu ambiri padziko lonse amaganiza kuti chipani cha Nazi chinapulula Ayuda okha. Koma chipanichi chinapululanso anthu ena. Msonkhanowu uli m’kati panachitika mwambo wotchuka wokumbukira kupululidwa kwa Ayuda ndipo unachitikira m’sunagoge yotchedwa Great Synagogue of Stockholm. Nduna yaikulu ya ku Sweden inanenapo kuti pakhale lonjezo lakuti padziko lonse, malo onse osungirako za mbiri yakale awatsegule kuti adziŵitse anthu za mmene chipani cha Nazi chinapululira anthu. Iye anati, “Tiyenera kudziŵa za kupululidwa kwa anthu monga fuko la Roma [Amwenye otchedwa Gypsy], opunduka ndiponso za kuzunzidwa ndi kuphedwa kwa anthu ogona amuna kapena akazi anzawo, anthu otsutsa boma ndiponso a Mboni za Yehova.”

Boma la Sweden lalemba buku lonena za kupululidwa kwa anthu kumeneku lotchedwa Tell Ye Your Children (Uzani Ana Anu), limene aligaŵira kwaulere m’dziko lonselo kumabanja onse okhala ndi ana. Bukuli limati Mboni za Yehova “zinakana kulumbira kuti zikhala zokhulupirika kwa Hitler ndi boma la Germany lolamulidwa ndi chipani cha Nazi. Zimene iwo anakana kuchita n’zosiyana ndi magulu ena onse chifukwa akanangosaina chikalata chosonyeza kuti akhala okhulupirika basi akanasiya kuzunzidwa. Komabe ochepa chabe anachita zimenezi.”

Mboni za Yehova Panthaŵi Yopulula Anthuyi

M’chaka cha 1933, ku Germany kunali Mboni za Yehova pafupifupi 25,000. Mboni zambiri zinali m’gulu la anthu oyamba kuwaika m’makampu ndi ndende za chipani cha Nazi. Iwo ananenetsa kuti monga Akristu sangaloŵerere m’zinthu zilizonse zokhudza ndale kapena nkhondo. Sanam’tame Hitler. Anakana kutsatira tsankhu la chipani cha Nazi ndiponso kukhala m’gulu landale la Hitler lolimbikitsa nkhondo. Pafupifupi anthu 2,000 anafa, ndipo oposa 250 mwa ameneŵa anachita kunyongedwa.

Kuphatikizanso apo, akaidi omwe anali Mboni anathandiza akaidi anzawo kupirira ndipo mwa othandizidwawo panali Ayuda ndi ena. Ankatero powaphunzitsa chiyembekezo cha m’Baibulo ndiponso powagaŵira odwala komanso ofooka zinthu zimene anali nazo. Ndipo nthaŵi zambiri ankapereka ngakhale chakudya chokhacho chomwe anali nacho. Chipani cha Nazi chitangoyamba kuzunza anthu, iwo anali kuulula mwachinsinsi zoti kuli misasa yachibalo ndipo amaululanso zomwe zinali kuchitika kumeneko. Kuyambira nthaŵi imeneyo, Mbonizo zafalitsa nkhani zambirimbiri zosimba nkhanza za a Nazi ndiponso mbiri ya opulumuka, m’magazini awo ofala padziko lonse, a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

Zinaonekeratu kuti nthumwi zimene zinali kumsonkhano wa Stockholm International Forum on the Holocaust zinali ndi mantha akuti khalidwe la chipani cha Nazi lingadzayambirenso. Pulofesa Yehuda Bauer, yemwe ndi mkulu wa bungwe lofufuza za kupululidwa kwa Ayuda lotchedwa International Center for Holocaust Studies ku Institute of Contemporary Jewry, ku Israel analongosola motere: “Chifukwa zinachitikapo, zingadzachitikenso, mwina osati mofanana, osatinso kwa anthu omwewo, mwinanso osati n’kuchitidwa ndi anthu omwewo, koma zingadzachitikire wina aliyense ndipo wina aliyense angadzazichite. Zinali zisanachitikepo koma tsopano zinachitikapo.”

[Chithunzi patsamba 28]

Chizindikiro chamakona atatu n’chimene chinkazindikiritsa Mboni za Yehova m’makampu

[Zithunzi pamasamba 28, 29]

1. Julius Engelhardt, amene anali wa Mboni za Yehova, ananyongedwa ndi a chipani cha Nazi ku Brandenburg pa August 14, 1944

2. A Mboni za Yehova atatu akubwerera kwawo atawamasula ku Sachsenhausen, mu 1945

3. Elsa Abt, wa Mboni amene anam’lekanitsa ndi kamwana kake kakakazi n’kumumanga kwa zaka pafupifupi zitatu

[Mawu a Chithunzi]

Nordrhein-Westfälisches Hauptstaatsarchiv, Düsseldorf

[Zithunzi patsamba 29]

Mboni zimene zinapulumuka zikusimba nkhani zawo m’mavidiyo ameneŵa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena