Lingaliro Labaibulo
Kodi Mulungu N’ngolekerera Motani?
“MULUNGU, POFUNA IYE KUONETSA MKWIYO WAKE, NDI KUDZIŴITSA MPHAMVU YAKE, ANALEKERERA NDI CHILEKERERO CHAMBIRI ZOTENGERA ZA MKWIYO ZOKONZEKERA CHIWONONGEKO.”—AROMA 9:22.
KUYAMBIRA kale lonse Mulungu walekerera zinthu zambiri zoipa zedi. Zaka zoposa 300 zapitazo, Yobu anadandaula kuti: “Oipa akhaliranji ndi moyo, nakalamba, nalemera kwakukulu? Mbewu zawo zikhazikika pamodzi nawo pankhope pawo, ndi ana awo pamaso pawo. Nyumba zawo sizitekeseka ndi mantha, ngakhale ndodo ya Mulungu siiwakhalira.” (Yobu 21:7-9) Anthu enanso okonda chilungamo, monga mneneri Yeremiya, anadandaulanso chifukwa chakuti Mulungu amakhala ngati akulekerera anthu oipa.—Yeremiya 12:1, 2.
Nanga inu mukuganiza bwanji? Kodi simumvetsa chifukwa chimene Mulungu walolera zinthu zoipa? Kodi nthaŵi zina mumaona kuti Mulungu ayenera kuchita zinthu mwachangu powononga nthaŵi yomweyo anthu onse oipa? Taganizirani zimene Baibulo limanena pankhani ya malire a kulekerera kwa Mulungu ndiponso zifukwa zake.
N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalekerera?
Choyamba, tifunse kuti: Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu, amene ali wolungama kwambiri amalekerera kuipa kulikonse? (Deuteronomo 32:4; Habakuku 1:13) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti iye amakondwera ndi zinthu zoipa? Sizili choncho ayi! Taganizirani chitsanzo ichi: Yerekezerani kuti pali dokotala amene amaswa malamulo aukhondo ndiponso amene amawapweteka kwambiri anthu odwala. Dokotalayo atakhala kuti akugwira ntchito pa chipatala, kodi sangam’chotse ntchito mwamsanga? Komatu pali nthaŵi zina pamene pangafunike kum’lekerera kwambiri. Tiyerekezere kutachitika mavuto adzidzidzi odetsa nkhaŵa, mwachitsanzo kutachitika nkhondo, kodi sikungakhale koyenera kulekerera dokotalayo kugwira ntchito yake m’njira yovutikira ndiponso yoopsa, mwina ngakhale kugwiritsa ntchito zipangizo zochitira opaleshoni zimene sizingagwiritsidwe ntchito panthaŵi yamtendere?
Mofanana ndi zimenezo, masiku ano Mulungu akulekerera moleza mtima zinthu zambiri zimene iye amaona kuti n’zosaloleka m’pang’ono pomwe. Ngakhale kuti amadana ndi zinthu zoipa, iye akuzilola kuchitikabe kwa nthawi yochepa. Pali zifukwa zomveka zimene iye amachitira zimenezi. Chifukwa china n’nchakuti, zimenezi zimapereka mpata wothetseratu kwamuyaya nkhani zofunika kwambiri zimene Satana anayambitsa ataukira Mulungu m’munda wa Edene. Nkhani zake zikukhudza makamaka mmene Mulungu amalamulilira; ngati muli mwachilungamo ndiponso mwabwino kapena ayi. Komanso popirira zinthu zoipa moleza mtima iye akupereka mpata ndiponso mwayi kwa anthu amene amachita zoipa kuti asinthe.
Mulungu Wachifundo Ndiponso Woleza Mtima
Makolo athu oyambawo, Adamu ndi Hava anagwirizana ndi Satana kuukira Mulungu. Mulungu akanatha kuwawononga nthaŵi yomweyo. Koma anasonyeza chifundo ndiponso kuleza mtima kwake powalola mwachikondi kubereka ana. Koma anaŵa ndiponso anthu onse amene anachokera kwa iwowo, anabadwa ali ochimwa.—Aroma 5:12; 8:20-22.
Mulungu analinganiza zoti alanditse anthu ku tsoka lawoli. (Genesis 3:15) Koma panopo, chifukwa chakuti amamvetsa mmene kupanda ungwiro kumene tinatengera kwa Adamu kumatikhudzira, iye amaleza mtima ndiponso amachita chifundo kwambiri. (Salmo 51:5; 103:13) Iye ndi “wochulukira chifundo” ndiponso ndi wokonzeka ndi wofunitsitsa ‘kukhululukira koposa.’—Salmo 86:5, 15; Yesaya 55:6, 7.
Malire a Kulekerera kwa Mulungu
Komabe ngati Mulungu atalola kuti kuchita zoipa kupitirirebe kwamuyaya ndiye kuti sakusonyeza chikondi komanso chilungamo. Palibe tate wachikondi amene nthaŵi zonse angamalekerere zoipa zimene mwana wake wina amachitabe mwadala kuti apweteketse mtima ena a m’banjamo. Motero kuleza mtima kwa Mulungu polekerera uchimo, nthaŵi zonse kudzakhala koyendera limodzi ndi mikhalidwe yake ina monga chikondi, nzeru ndiponso chilungamo. (Eksodo 34:6, 7) Cholinga chake cholezera mtima chikangokwaniritsidwa, sadzalekereranso zinthu zoipa.—Aroma 9:22.
Mtumwi Paulo ananena zimenezi momveka bwino. Panthaŵi ina yake iye ananena kuti, “M’mibadwo yakale [Mulungu] adaleka mitundu yonse iyende m’njira mwawo.” (Machitidwe 14:16) Panthaŵi inanso Paulo ananena za ‘nthaŵi zimenezi za kusadziŵa pamene Mulungu analekerera’ anthu amene sanamvere malamulo ake ndi mfundo zake. Iye anapitiriza kuti, “Tsopanotu [Mulungu] alinkulamulira anthu onse ponse ponse atembenuke mtima.” Chifukwa chiyani? “Chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo.”—Machitidwe 17:30, 31.
Pindulani Tsopano ndi Kulekerera kwa Mulungu
Ndiyetu kunena zoona, palibe amene ayenera kuganiza kuti angaphwanye dala malamulo a Mulungu, kenaka pofuna kuthaŵa chilango pa zomwe wachitazo n’kumam’pempha Mulunguyo kuti am’khululukire, koma mtima uli zii. (Yoswa 24:19) Anthu ambiri mu Israyeli wakale ankaganiza kuti akhoza kutero. Sankafuna kusintha. Sanamvetsetse cholinga cha kulekerera ndi kuleza mtima kwa Mulungu. Mulungu sanalekerere kwa muyaya kuipa kwawoku.—Yesaya 1:16-20.
Baibulo limasonyeza kuti, kuti munthu asaweruzidwe ndi Mulungu ayenera ‘kulapa,’ kutanthauza kuti kuzindikira mopwetekedwa mtima kuti ndi wopanda ungwiro ndiponso wochimwa ndi kupepesa pamaso pa Mulungu, kenaka n’kulekeratu kuchita zoipa. (Machitidwe 3:19-21) Kenaka chifukwa cha nsembe yadipo ya Kristu, Yehova Mulungu angadzam’khululukire. (Machitidwe 2:38; Aefeso 1:6, 7) Panthaŵi yake yoyenera, Mulungu adzachotsa zinthu zonse zopweteka zimene zinabwera chifukwa cha kuchimwa kwa Adamu. Padzakhala “m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano” mmene sadzalekereranso kuti “zinthu zofuna kuwonongedwa . . . zikhaleko.” (Chivumbulutso 21:1-5; Aroma 9:22, Phillips) N’zotsatira zabwinotu kwambiri zopezeka chifukwa cha kulekerera kosasimbika, koma kokhala ndi malire kwa Mulungu!
[Chithunzi patsamba 29]
Mulungu analola Adamu ndi Hava kuti akhale ndi ana