Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 2/8 tsamba 21-22
  • Kulolera Kuchita Mopambanitsa Mbali Zonse Ziŵiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulolera Kuchita Mopambanitsa Mbali Zonse Ziŵiri
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchoka pa Kulolera Kukhala Waliuma
  • Kuchoka pa Kulolera Kukhala Wakhalidwe Loipa
  • Kuteteza Ufulu—Motani?
    Galamukani!—1999
  • Kulinganiza Bwino Kungakometse Moyo Wanu
    Galamukani!—1997
  • Ololera, Koma Odzipereka pa Miyezo ya Mulungu
    Galamukani!—1997
  • Kukhala Ololera
    Galamukani!—2015
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 2/8 tsamba 21-22

Kulolera Kuchita Mopambanitsa Mbali Zonse Ziŵiri

KUKONGOLA kwa Chigwa cha Kashmir kunasonkhezera wafilosofi wa m’zaka za zana la 16 kunena kuti: “Ngati paradaiso alikodi, ndi yemweyu!” Kunena zoona, iye sanadziŵe zimene zinali kudzachitika pambuyo pake m’dera limenelo la dziko. Pazaka zisanu zokha zapitazo, anthu osachepera 20,000 aphedwa m’nkhondo ya zigaŵenga ndi Asilikali a India. Tsopano nyuzipepala yachijeremani Süddeutsche Zeitung imatcha dera limenelo “chigwa cha misozi.” Chigwa cha Kashmir chikutiuza phunziro lapafupi koma lofunika kwambiri: Kusalolera kungawononge malo amene angakhale paradaiso.

Kodi kulolera kumatanthauzanji? Malinga ndi Collins Cobuild English Language Dictionary, “ngati uli wololera, umalola anthu ena kukhala ndi maganizo awo kapena zikhulupiriro zawo, kapena kuchita mwanjira ina, ngakhale ngati sugwirizana nayo kapena kuiyanja.” Ndi mkhalidwe wabwino chotani nanga kuusonyeza! Inde mtima umakhala m’malo ngati tili ndi anthu amene amalemekeza zikhulupiriro zathu ndi maganizo athu, ngakhale ngati zimenezo zisiyana ndi zawo.

Kuchoka pa Kulolera Kukhala Waliuma

Liwu lotsutsana ndi kulolera ndilo kusalolera, limene lili ndi matanthauzo angapo osiyana mphamvu zake. Kusalolera kungayambe ndi kusavomereza khalidwe la wina kapena kachitidwe kake ka zinthu chifukwa choumirira maganizo a iwe mwini. Kuumirira maganizo a iwe mwini kumachotsa chisangalalo m’moyo ndi kutseka maganizo ako kuti usadziŵe zatsopano.

Mwachitsanzo, munthu wosafuna maseŵera anganyansidwe ndi chisangalalo chachikulu cha mwana. Wachichepere angaipidwe ndi mkulu pa iye chifukwa iyeyo amayamba waganiza kwambiri asanachite chinthu. Uzani munthu wosamala kuti achite zinthu pamodzi ndi wina wosimbwa, ndipo aŵiriwo adzakwiya. Kodi nchifukwa ninji kunyansidwa, kuipidwa, ndi kukwiya? Chifukwa, m’mikhalidwe yonseyo, aliyense zikumuvuta kulolera maganizo kapena khalidwe la mnzake.

Patakhala kusalolera, kuumirira maganizo a iwe mwini kungakule kukhala tsankhu, limene ndilo kunyansidwa ndi gulu, fuko, kapena chipembedzo. Loipa kuposa tsankhu ndi liuma, limene limasonyezedwa ndi udani wachiwawa. Zotsatira zake ndizo nsautso ndi kukhetsa mwazi. Talingalirani zimene kusalolera kunachititsa m’Nkhondo za Mtanda! Ngakhale lero, kusalolera kwabutsa nkhondo ku Bosnia, Rwanda, ndi ku Middle East.

Kulolera kumafuna kulinganiza, ndipo kulinganiza bwino sikwapafupi ayi. Tili ngati pendulum ya koloko, yolendeŵera uku ndi uko. Nthaŵi zina, timakhala ololera pang’ono kwambiri; nthaŵi zina, mopambanitsa.

Kuchoka pa Kulolera Kukhala Wakhalidwe Loipa

Kodi nkotheka kukhala wololera mopambanitsa? Phungu wa nyumba ya malamulo ya United States, Dan Coats, polankhula mu 1993, anafotokoza za “mkangano ponena za tanthauzo la kulolera ndi mmene angakuchitire.” Kodi anatanthauzanji? Phunguyo anadandaula kuti m’dzina la kulolera, ena “amaleka kukhulupirira choonadi cha makhalidwe—chabwino ndi choipa, choyenera ndi chosayenera.” Anthu amenewo amaganiza kuti kulibe munthu amene ali ndi mphamvu yonena kuti khalidwe labwino ndi ili, loipa ndi ili.

Mu 1990, Mbritishi wandale Lord Hailsham analemba kuti “mdani woipa kwambiri wa makhalidwe abwino saali kukana Mulungu, kukayikira Mulungu, kukonda chuma, umbombo kapena china chilichonse pa zochititsa zake zolandirika. Mdani weniweni wa makhalidwe abwino ndi nihilism, kusakhulupiriratu kalikonse.” Mwachionekere, ngati sitikhulupirira kalikonse, ndiye kuti tilibe miyezo ya khalidwe labwino ndipo tingalole zonse. Koma kodi kuli bwino kulola khalidwe lamtundu uliwonse?

Hedimasitala wa sukulu ya sekondale ku Denmark sanaganize zimenezo. Iye analemba nkhani m’nyuzipepala kuchiyambi kwa ma 1970, kudandaula ndi zilengezo zimene anaulutsa za zionetsero zamaliseche zosonyeza anthu akugonana ndi nyama. Zilengezo zimenezi anazilola chifukwa cha mkhalidwe “wololera” wa Denmark.

Inde, zovuta zimabuka chifukwa chololera pang’ono kwambiri komanso chifukwa chololera mopambanitsa. Kodi nchifukwa ninji kuli kovuta kupeŵa kupambanitsa ndi kuchita molinganiza? Taŵerengani nkhani yotsatira chonde.

[Chithunzi patsamba 21]

Kupambanitsa kukwiya chifukwa cha zolakwa za ana kungawawononge

[Chithunzi patsamba 22]

Kulekerera zonse zimene ana amachita sikudzawathandiza kukonzekera mathayo a moyo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena