Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 2/8 tsamba 23-25
  • Kulinganiza Bwino Kungakometse Moyo Wanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulinganiza Bwino Kungakometse Moyo Wanu
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Omwe Angakhale Odudukira za Eni
  • “Mantha Aakulu”
  • Peŵani Msampha wa Mphwayi
  • Kuteteza Ufulu—Motani?
    Galamukani!—1999
  • Kulolera Kuchita Mopambanitsa Mbali Zonse Ziŵiri
    Galamukani!—1997
  • Ololera, Koma Odzipereka pa Miyezo ya Mulungu
    Galamukani!—1997
  • Kukhala Ololera
    Galamukani!—2015
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 2/8 tsamba 23-25

Kulinganiza Bwino Kungakometse Moyo Wanu

KULOLERA kuli ngati shuga m’kapu ya khofi. Mlingo wabwino ungakondweretse mtima wanu. Koma pamene kuli kwakuti timaoloŵa dzanja pashuga, nthaŵi zambiri timaliumitsa pakulolera. Chifukwa ninji?

“Anthu safuna kulolera,” analemba motero Arthur M. Melzer, wachiŵiri kwa profesa pa Yunivesite ya Michigan State. “Zimene amachita mwachibadwa ndi . . . tsankhu.” Chotero kusalolera sikuli chabe khalidwe losayenera lopezeka mwa anthu oŵerengeka okha; kuumirira maganizo a iwe mwini kumachitika mwachibadwa kwa ife tonse chifukwa mtundu wa munthu wonse ngwopanda ungwiro.—Yerekezerani ndi Aroma 5:12.

Omwe Angakhale Odudukira za Eni

Mu 1991, magazini a Time anasimba za mzimu woumirira maganizo a iwe mwini womwe ukufala ku United States. Nkhaniyo inafotokoza za “odudukira m’moyo wa eni,” anthu amene ayesa kuumiriza miyezo yawoyawo ya khalidwe pa aliyense. Osafuna kutengera za eni avutika. Mwachitsanzo, mkazi wina ku Boston anamchotsa ntchito chifukwa anakana kudzola zodzikometsera nazo. Mwamuna wina ku Los Angeles anamchota ntchito chifukwa anali wonenepa kwambiri. Nkuchitiranji changu pofuna kuti ena agonje?

Anthu oumirira maganizo a iwo eni ali osalolera, adyera, aliuma, ndipo okonda kuchita umbuye. Koma kodi anthu ochuluka saali osalolera, adyera, aliuma, kapena okonda kuchita umbuye pamlingo wina wake? Ngati mikhalidwe imeneyi izika mizu mu umunthu wathu, tidzakhala oumirira maganizo a ife eni.

Nanga bwanji za inu? Kodi mumazunguza mutu mukaona zakudya zimene mnzanu amadya? Pamakambirano, kodi nthaŵi zambiri mumafuna kuti lingaliro lanu ndilo ligwire ntchito? Pogwira ntchito ndi gulu, kodi mumafuna kuti iwo atsatire kalingaliridwe kanu? Ngati mumatero, kungakhale bwino kuwonjeza shuga pang’ono m’khofi wanu!

Koma, monga momwe yatchulira nkhani yapitayo, tsankhu laudani lingakhale mtundu wina wa kusalolera. China chimene chingachititse kuti kusalolera kukule ndi nkhaŵa yaikulu.

“Mantha Aakulu”

Akatswiri a mafuko apenda mbiri ya mtundu wa munthu kuti apeze nthaŵi ndi malo kumene kunaonekera tsankhu. Anapeza kuti kusalolera kwa mtundu umenewu sikumakhalapo nthaŵi zonse, ndipo sikumaonekera pamlingo umodzimodzi m’dziko lililonse. Magazini achijeremani a sayansi yachilengedwe a GEO akusimba kuti kulimbana kwa mafuko kumachitika panthaŵi ya vuto pamene “anthu ali ndi mantha aakulu ndiponso ndi ganizo lakuti fuko lawo lili pangozi.”

Kodi “mantha aakulu” amenewo ngofala lerolino? Inde. Mtundu wa munthu kuposa ndi kale lonse ukukumana ndi vuto lina ndi linzake. Ulova, kukwera kwa mitengo, kuchulukitsa kwa anthu, kuwonongeka kwa muyalo wa ozoni, upandu m’mizinda, kuipitsa madzi akumwa, kutentha kwa dziko—mantha oziziritsa m’nkhongono pa chimodzi cha zimenezi amawonjeza nkhaŵa. Mavuto amadzetsa nkhaŵa, ndipo nkhaŵa yopambanitsa imayambitsa kusalolera.

Kusalolera kotero kumaonekera, mwachitsanzo, pamene mafuko ndi magulu osiyana chikhalidwe akhala pamodzi, monga m’maiko ena ku Ulaya. Malinga ndi lipoti la National Geographic mu 1993, maiko a Kumadzulo kwa Ulaya panthaŵiyo anali ndi anthu odzakhaliratu oposa 22 miliyoni. Azungu ambiri “anathedwa mphamvu ndi mlongo wa alendo” achinenero, chikhalidwe, kapena chipembedzo chosiyana. Ku Austria, Belgium, Britain, France, Germany, Italy, Spain, ndi Sweden kwakhala anthu ambiri osafuna akunja.

Nanga bwanji za olamulira adziko? M’ma 1930 ndi ma 1940, Hitler anapanga kusalolera kukhala kachitidwe ka boma. Mwachisoni, atsogoleri ena andale ndi achipembedzo lerolino amagwiritsira ntchito kusalolera kuti apeze zofuna zawo. Zimenezi zachitika kumalo onga Austria, France, Ireland, Russia, Rwanda, ndi United States.

Peŵani Msampha wa Mphwayi

Ngati khofi wathu ali ndi shuga wochepa kwambiri, timadziŵa kuti kanthu kena kakusoŵa; ngati ali ndi wochulukitsa amazuna m’kamwa mwathu kochititsa nseru. Ndi mmenenso kulolera kulili. Talingalirani zimene zinachitikira mwamuna wina amene amaphunzitsa pakoleji ku United States.

Zaka zingapo zapitazo, David R. Carlin, Jr., anapeza njira yapafupi komanso yabwino yosonkhezera kukambirana m’kalasi. Anali kunena mawu ena ndi cholinga chotokosa malingaliro a ophunzira ake, akudziŵa kuti iwo adzatsutsa. Panali kukhala makambirano osangalatsa. Komabe, mu 1989, Carlin analemba kuti njira imodzimodziyo sinagwirenso bwino ntchito. Chifukwa? Pamene kuli kwakuti ophunzirawo sanali kuvomereza zimene iye ananena, sanasamalenso zokangana. Carlin anafotokoza kuti iwo anatengera “mphwayi ya munthu wokayikira”—mzimu wosasamala, wosafuna kusamala mpang’ono pomwe.

Kodi mzimu wosafuna kusamala mpang’ono pomwe ndiwo kulolera? Ngati palibe amene asamala zimene aliyense aganiza kapena kuchita, sipamakhala miyezo iliyonse. Kusakhalapo kwa miyezo ndiko mphwayi—kusasamala za kalikonse. Kodi mkhalidwe umenewo umachitika bwanji?

Malinga ndi Profesa Melzer, mphwayi imafala pakati pa anthu amene amalandira miyezo yambiri yosiyana ya kakhalidwe. Anthuwo amafika pokhulupirira kuti khalidwe lililonse nlololeka ndi kuti chilichonse ndi nkhani ya munthu mwini. M’malo mophunzira kuganiza ndi kudzifunsa kuti chololeka nchiti ndi chosaloleka nchiti, anthu “nthaŵi zambiri amaphunzira kusaganiza mpang’ono pomwe.” Amasoŵa chikumbumtima chimene chimasonkhezera munthu kutsutsa kusalolera kwa ena.

Nanga bwanji za inu? Kodi nthaŵi ndi nthaŵi mumapeza kuti mukutengera mzimu wosafuna kusamala mpang’ono pomwe? Kodi mumaseka mukamva nthabwala zotukwana kapena zokondera fuko? Kodi mumalola mwana wanu mnyamata kapena mtsikana kupenyerera mavidiyo osonkhezera umbombo ndi chisembwere? Kodi muganiza kuti ana anu ayenera kumachita maseŵero achiwawa apakompyuta?

Patakhala kulolera kopambanitsa, banja kapena anthu amatuta chisoni, pakuti palibe amene adziŵa—kapena kusamala—za chabwino kapena choipa. Phungu wa nyumba ya malamulo ya United States, Dan Coats anachenjeza za “msampha woyesa kuti mphwayi ndiyo kulolera.” Kulolera kungachititse munthu kukhala wotseguka mutu; kulolera mopambanitsa—mphwayi—kungamchititse kukhala wopanda kanthu m’mutu.

Choncho, tiyenera kulola chiyani ndipo tiyenera kukana chiyani? Kodi chinsinsi chake chotheketsa kulinganiza bwino nchiyani? Umenewo udzakhala mutu wa nkhani yotsatira.

[Chithunzi patsamba 23]

Yesetsani kuchita molinganiza ndi mikhalidwe yosiyanasiyana

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena