Ololera, Koma Odzipereka pa Miyezo ya Mulungu
“ANTHU ololera saali opusa, ndipo anthu opusa saali ololera,” umatero mwambi wachitchaina. Mwambi umenewu ukunena zoona kwambiri, pakuti kukhala wololera nkovuta, kumafuna kudzipereka pa miyezo yoyenera ya khalidwe. Koma kodi ndi miyezo iti imene tiyenera kudziperekapo? Kodi sikungakhale kwanzeru kutsatira miyezo imene Mpangi wa mtundu wa munthu anaika, yofotokozedwa m’Mawu ake, Baibulo Lopatulika? Mulungu iye mwini amapereka chitsanzo chabwino koposa potsatira miyezo yake.
Mlengiyo—Chitsanzo Chathu Choposa
Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse, amakulinganiza mwangwiro kulolera, samakusonyeza mopambanitsa kapena mochepa kwambiri. Kwa zaka zikwi zambiri, iye walekerera aja otonza dzina lake, osokoneza mtundu wa munthu, ndi kuwononga dziko lapansi. Mtumwi Paulo analemba zimene zili pa Aroma 9:22 kuti Mulungu “analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko.” Kodi nchifukwa ninji Mulungu wakhala wololera kwanthaŵi yaitali chonchi? Chifukwa kulolera kwake kuli ndi cholinga.
Mulungu waleza nawo mtima mtundu wa munthu ‘posafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’ (2 Petro 3:9) Mlengi wapatsa mtundu wa munthu Baibulo ndipo watuma atumiki ake kuti adziŵikitse miyezo yake ya khalidwe kulikonse. Akristu oona ngodzipereka pa miyezo imeneyi. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti atumiki a Mulungu ayenera kukhala olimbirira m’mikhalidwe iliyonse?
Olimba, Koma Ololera
Yesu Kristu analimbikitsa awo ofuna moyo wamuyaya ‘kuloŵa pachipata chopapatiza.’ Koma kuloŵa pachipata chopapatiza sikufuna kuumirira maganizo a iwe mwini. Ngati timakonda kuchita umbuye kapena liuma pamene tili ndi ena, tingapeputsire aliyense moyo ngati tithetsa chizoloŵezi chimenechi. Motani?—Mateyu 7:13; 1 Petro 4:15.
Theofano, wophunzira wa ku Greece amene anafotokoza kuti nthaŵi imene anakhala ndi anthu osiyanasiyana inamthandiza kuwamvetsa bwino, anati: “Tifunika kuyesa kudziŵa kalingaliridwe kawo m’malo moŵakakamiza kutenga kalingaliridwe kathu.”
Chotero, mwa kumdziŵa bwino mnzathu, tingapeze kuti zakudya zimene amakonda ngakhalenso kalankhulidwe kake si zachilendo monga momwe tinkaganizira. M’malo molankhula zochuluka nthaŵi zonse kapena kuumirira kuti lingaliro lathu ndilo ligwire ntchito, tingadziŵe zinthu zambiri zothandiza mwa kumvetsera lingaliro lake. Inde, anthu amaganizo otseguka amapeza zambiri m’moyo.
Pamene nkhani ili pa zimene munthu amakonda, tiyenera kukhala olola ndi kuwaleka ena kuti asangalale nazo zosankha zawo. Koma pamene khalidwelo likukhudza kumvera Mlengi wathu, tiyenera kulimba. Mulungu Wamphamvuyonse samalekerera khalidwe lamtundu uliwonse. Iye anasonyeza zimenezo mwa zochita zake kwa atumiki ake akale.
Msampha wa Kulolera Mopambanitsa
Eli, mkulu wa ansembe wa mtundu wakale wa Israyeli, anali mtumiki wa Mulungu amene anakodwa mumsampha wa kulolera mopambanitsa. Aisrayeli analoŵa mu unansi wapangano ndi Mulungu, navomereza kuti adzamvera malamulo ake. Koma ana a Eli aŵiri aamuna, Hofeni ndi Pinehasi, anali aumbombo ndi achisembwere ndipo analibe ulemu mpang’ono pomwe kwa Wamphamvuyonse. Ngakhale kuti Eli anali kuchidziŵa bwino Chilamulo cha Mulungu, anawadzudzula mofeŵa ndipo anawalekerera osawalanga. Analakwa poganiza kuti Mulungu adzalekerera kuipako. Mlengi amasiyanitsa kufooka ndi kuipa. Chifukwa cha kuswa kwawo dala Chilamulo cha Mulungu, ana oipa a Eli analangidwa kowopsa—ndipo moyenera.—1 Samueli 2:12-17, 22-25; 3:11-14; 4:17.
Ha, tsoka lingatigwere ngati tilolera mopambanitsa m’banja lathu mwa kunyalanyaza zolakwa za ana athu zobwerezabwereza! Kuli bwino chotani nanga kuwalera iwo “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye”! Zimenezi zikutanthauza kuti ife enife tiyenera kuumirira miyezo ya Mulungu ya mayendedwe ndi kuikhomereza mwa ana anthu.—Aefeso 6:4.
Momwemonso, mpingo wachikristu sungalekerere kuipa. Ngati munthu ali ndi chizoloŵezi chochita zolakwa zazikulu ndipo akana kulapa, achotsedwe. (1 Akorinto 5:9-13) Komabe, kunja kwa banja ndi mpingo, Akristu oona samayesa kusintha anthu onse.
Unansi Wolimba ndi Yehova
Kusalolera kumabutsa mkhalidwe wa nkhaŵa. Komabe, ngati tili ndi unansi wolimba waumwini ndi Mulungu, timakhala ndi mkhalidwe wachisungiko umene umatithandiza kusapambanitsa. “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka,” timaŵerenga zimenezo pa Miyambo 18:10. Inde kulibe chovulaza chilichonse chimene chingadze pa ife kapena okondedwa athu chimene Mlengi sadzasamalira panthaŵi yake yoyenera.
Wina amene anapindula kwambiri ndi unansi wolimba ndi Mulungu anali mtumwi Paulo. Monga Myuda wotchedwa Saulo, anazunza otsatira a Yesu Kristu ndipo anali ndi liwongo la mwazi. Koma Saulo iye mwini anakhala Mkristu ndipo, atakhala mtumwi Paulo, anayamba ulaliki wanthaŵi zonse pambuyo pake. Paulo anasonyeza maganizo otseguka polalikira kwa anthu onse, ‘kwa Ahelene ndi kwa akunja, kwa anzeru ndi kwa opusa.’—Aroma 1:14, 15; Machitidwe 8:1-3.
Kodi iye anakhoza bwanji kusintha? Mwa kupeza chidziŵitso cholongosoka cha Malemba ndi mwa kukula m’chikondi chake kwa Mlengi, wopanda tsankhu. Paulo anaphunzira kuti Mulungu ngwolungama pakuti Iye amaweruza munthu aliyense malinga ndi umunthu wake ndi zochita zake, osati malinga ndi chikhalidwe chake kapena fuko lake. Inde, ntchito nzimene Mulungu amafuna. Petro anati “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Mulungu Wamphamvuyonse alibe tsankhu. Zimenezi nzosiyana ndi olamulira ena adziko, amene mwadala amagwiritsira ntchito kusalolera kuti apeze zofuna zawo.
Nthaŵi Zikusintha
Malinga ndi John Gray, wa pa Yunivesite ya Oxford ku England, kulolera ndi “mkhalidwe umene wakhala wosoŵa posachedwa.” Koma zimenezi zidzasintha. Kulolera kolinganiza ndi nzeru ya Mulungu kudzafala.
M’dziko latsopano la Mulungu lomwe layandikira, kusalolera sikudzakhalamonso. Kusalolera koipitsitsa, konga tsankhu ndi liuma, sikudzakhalamonso. Kuumirira maganizo a iwe mwini sikudzathetsanso chisangalalo m’moyo. Pamenepo, kudzakhala paradaiso waulemerero woposa aliyense amene akanakhalako m’Chigwa cha Kashmir.—Yesaya 65:17, 21-25.
Kodi mukuyembekeza kudzakhala m’dziko latsopano limenelo? Umenewo udzakhala mwaŵi wanu ndipo zidzakhala zosangalatsa!
[Chithunzi patsamba 26]
Mtumwi Paulo sanapambanitse chifukwa anali paunansi ndi Mulungu