Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g02 5/8 tsamba 9
  • Si Zongopeka Kuti Dziko Lonse Lidzakhala Pamtendere!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Si Zongopeka Kuti Dziko Lonse Lidzakhala Pamtendere!
  • Galamukani!—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Zidzatheka Bwanji Kuti Padziko Lonse Lapansi Padzakhale Mtendere?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Mtendere Weniweni—Kodi Udzachokera Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Lolani “Mtendere wa Mulungu” Uchinjirize Mtima Wanu
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Adzatsogolera Anthu ku Mtendere Ndani?
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—2002
g02 5/8 tsamba 9

Si Zongopeka Kuti Dziko Lonse Lidzakhala Pamtendere!

ALFRED Nobel akanakhala ndi moyo lero n’kuona zinthu zonse zimene zakhala zikuchitika zaka 100 zapitazi, kodi akanaganiza kuti anthu padziko lonse atsala pang’ono kukhala pamtendere? N’zosakayikitsa kuti akanasangalala kudziŵa kuti anthu ambiri akhala akuyesetsa ndi mtima wonse kuthetsa nkhondo. Komabe sakanamva bwino kudziŵa chilungamo chake cha nkhaniyi. Pulofesa Hugh Thomas anangonena mwachidule za nkhaniyi, pamene anati: “Ngakhale kuti zaka 100 kuyambira chaka cha 1900 zinali zaka zachitukuko ndiponso zaka zimene maboma akhala akuganizira kwambiri anthu osauka, zakazi n’zodziŵika kwambiri ndi kugwiritsa ntchito zinthu monga mfuti zoomba zipolopolo molumikiza, akasinja, ndege zoponya mabomba ndiponso mabomba ouluka okha. Nthaŵi imeneyi yatchuka kwambiri ndi nkhondo zopulula anthu ndiponso zowononga kwambiri kuposa nkhondo za kale lonse.” Pulofesa Thomas ananenanso kuti “motero nkhani yakuti kaya zaka zimenezi zinali zachitukuko kapena ayi ingangodalira pa mmene aliyense angaganizire.”

Kodi tsopano pakuti tayamba zaka 100 zina, zikuoneka kuti zingatheke kuti dziko lonse lidzakhale pamtendere? Ayi ndithu! Pankhani ya zimene zigaŵenga zinachita pa September 11, 2000, ku New York City ndi ku Washington, D.C. magazini ya Newsweek inanena kuti: “Pakuti masiku ano ndege zikuluzikulu angathe kuzisandutsa mabomba ouluka paokha, palibe chinthu chilichonse chimene tingati n’chosatheka n’komwe, kapenanso chimene tinganenedi kuti tingathe kuchipeŵa.”

Anthu ena amanena kuti mtendere wapadziko lonse sungatheke pokhapokha zinthu ziŵiri izi zitachitika: Choyamba, anthu ayenera kusinthiratu kaganizidwe ndi khalidwe lawo; chachiŵiri, mayiko onse ayenera kugwirizana n’kumalamulidwa ndi boma limodzi. Baibulo limalosera za nthaŵi imene mtendere udzathekedi, koma osati chifukwa cha mphamvu za anthu ayi. Ponena za Mlengi wathu, Yehova Mulungu, Salmo 46:9 limati: ‘Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.’ Kodi Mulungu adzachita bwanji zimenezi? Adzagwiritsa ntchito Ufumu wake umene anthu ambiri oona mtima akhala akuupempherera mobwerezabwereza. Sikuti ufumu umenewo uli chabe mtima wa munthu wovuta kuufotokoza ayi, koma ndi boma lenileni limene Mulungu adzagwiritse ntchito pokhazikitsa mtendere padziko lonse lapansi. Mneneri wouziridwa Yesaya analosera kuti anthu amene adzakhale m’boma limenelo “sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:4) Chifukwa cha maphunziro amene adzakhalepo padziko lonse, anthu adzaphunzira kukhala pamtendere ndipo potero “adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape.”

Ngakhale tsopano lino, Mboni za Yehova zikuchita zimenezi. Ngakhale kuti Mbonizi zimachokera m’mitundu yosiyanasiyana ndiponso m’mayiko opitirira 200, zimakana kunyamula zida n’kumapha anthu anzawo. Kusaloŵerera kwawo pankhondo m’dziko lino mmene nkhondo ili pachimake penipeni, kukusonyezeratu poyera kuti mtendere si chinthu chimene sichingatheke koma ndi chinthu chotheka ndithu.

Kodi mungakonde kudziŵa zambiri za chikhulupiriro chochokera m’Baibulo chakuti padzakhala mtendere weniweni? Chonde lemberani kalata kwa ofalitsa a magazini ino, pogwiritsa ntchito adiresi ya kufupi ndi kwanu imene ili patsamba 5, kapena kaonaneni ndi Mboni za Yehova kumene mukukhalako.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena