Kangaude
Analengedwadi Mwaluso
◼ Ulusi wa kangaude ndi wopepuka tikauyerekeza ndi ulusi wa thonje. Komabe, tikatenga ulusiwu ndi chitsulo, zonse zolemera mofanana, ulusiwu ndi umene ungakhale wolimba kwambiri. Kwa zaka zambiri, akatswiri a sayansi aphunzira zambiri zokhudza ulusi wa kangaude. Anthu amachita chidwi ndi ulusi wina womwe kangaude amapanga, wolimba kwambiri kuposa ulusi wamitundu 7 umene akangaude ena amapanga. Ulusiwu ndi wolimba kwambiri ndiponso sunyowa ndi madzi. Umasiyana ndi ulusi wopangidwa ndi mtundu wina wake wa mbozi womwe amawombera nsalu.
Taganizirani izi: Mafakitale opanga ulusi wolimba kwambiri amagwiritsa ntchito mankhwala ndiponso moto wambiri. Mosiyana ndi zimenezi, akangaude amapanga ulusi popanda moto ndiponso amagwiritsa ntchito madzi okha. Koma zingwe zopangidwa ndi kangaude ndi zolimba kwambiri kuposa zingwe zina. Ukonde wopangidwa ndi zingwe za kangaude ataukulitsa ngati bwalo losewerera mpira, ungathe kuimitsa ndege yaikulu yomwe ikuuluka.
N’zosadabwitsa kuti ofufuza amachita chidwi kwambiri ndi kulimba kwa zingwe zopangidwa ndi ulusi umenewu. Munthu wina dzina lake Aimee Cunningham analemba m’magazini (ya Science News ) kuti: “Akatswiri a sayansi akufunitsitsa atapanga zinthu zina mofanana ndi mmene kangaude amapangira ulusiwu. Zinthu zimenezi ndi monga mavesiti amene zipolopolo sizilowa ndiponso zingwe zomangira milatho yolenjekeka.”
Komabe, kupanga zinthu motsanzira ulusiwu n’kovuta. Zimenezi zili choncho chifukwa ulusiwu umapangidwa m’mimba mwa kangaude ndipo zimene zimachitika popanga ulusiwu sizidziwika bwino. Katswiri wina wa sayansi dzina lake Cheryl Y. Hayashi, analemba m’magazini ina kuti: “N’zochititsa manyazi kuti anthu ambiri anzeru zawo, akuyesayesa kupanga zinthu motsanzira zimene akangaude omwe amakhala m’makonde a nyumba zathu amachita mosavutikira.”—Chemical & Engineering News
Kodi mukuganiza bwanji? Kodi akangaude opanga ulusi wolimba kwambiri amenewa anakhalako okha kapena anapangidwa ndi Mlengi waluso?
[Chithunzi patsamba 24]
M’mene ulusi wa kangaude umaonekera ukamapangidwa
[Mawu a Chithunzi]
Copyright Dennis Kunkel Microscopy, Inc.