Kuphunzira kwa Akangaude
KODI mumachita mantha mutawona kangaude? Ngakhale ife amene timatero mwina tinazizwapo ndi lukanelukane wokongola wa ukonde wa kangaude, mosasamala kanthu kuti kaŵirikaŵiri sitingatero. Ndiponso, ambiri a ife tinamvapo kuti ukondewo ngwopangidwa mozizwitsa. Koma bwanji za zinthu zimene ukondewo umapangidwa nazo—siliki?
Asayansi ndi mainjiniya achita chidwi kwazaka zambiri ndi siliki wopangidwa ndi akangaude ena, zilumphirabere, ndi ntchentche. Christopher Viney, wachiŵiri kwa pulofesa wopanga zinthu mwakutsanzira zamoyo ndi katswiri wofula zitsulo pa Yunivesite ya Washington, U.S.A., wafufuza mwapadera kangaude woluka ukonde wobulungika. Malinga ndi nyuzipepala ya The Globe and Mail, ya ku Toronto, Canada, iye wapeza kuti umodzi wa mitundu isanu ya siliki umene kangaudeyo amapanga ngwolimbirapo kuposa chitsulo—kunena zowona, ngwolimbirapo kuŵirikiza nthaŵi khumi kuposa Kevlar, nkhosi yopangira nsalu za buletipulufu, maferemu a bwato, ndi galimoto zankhondo!
Asayansi a gulu la nkhondo la United States akhoza kuyerekezera msanganizo wa makhemikolo a fibroin, protini yopanga siliki ameneyu. Komabe, asayansiwo apeza kuti suli chabe msanganizo wa makhemikolo a siliki umene umachititsa mpangidwe wake wodabwitsa; komanso njira imene kangaudeyo amalukira khemikoloyo. Mkati mwa perepetu wa kangaude, siliki amakhala mumpangidwe wamadzi wonga krustalo. Mamolekyu ake amapanga mizera ya timaunyolo tatitali totchedwa polymers, timene tiri ndi nyonga yakutamuka. Komabe, Viney ali ndi chidaliro chakuti patapezeka makina apadera opangira nkhosizo, asayansi pomalizira adzaphunzira kujambula luso limenelo.
“Akangaude akutiposabe,” Viney anauza mtola nkhani wa The Globe and Mail, koma anawonjezera kuti, “Adziŵa ndani? Mwinamwake tidzawaposa.” Mwinamwake adzatero; mwina sadzatero. Mulimonse mmene zingakhalire, thamo la mpangidwe woyambirira lidzamka ku Magwero amodzi okha nthaŵi zonse—Amene analenga zinthu zonse, Yehova.—Chivumbulutso 4:11.