Kulimbana ndi Vuto la CFS
MADOKOTALA paprogramu ya pawailesi yakanema anali kukambitsirana pankhani yosiirana ponena za njira yochiritsira CFS (chronic fatigue syndrome) pamene mmodzi wa iwo anati: “Odwala onseŵa amawonekera kukhala athanzi mofanana ndi aliyense wa ife tikukambitsirana pano.” Chifukwa chakuti odwalawo samawoneka kukhala odwala, kaŵirikaŵiri amachitiridwa mwanjira imene imawonjezera vuto lawo.
Patricia, wodwala CFS mu Texas, anati: “Nthaŵi zina ndimadzilingalira monga Yobu, amene anzake nthaŵi zina sanali othandiza.” Mwachitsanzo, tsiku lina, womzonda anamuuza kuti: “Simukuwoneka wodwala kwa ine! Ndimati mwina ndinu wodwala kwambiri. Inuyo simusiyana ndi apongozi anga. Nawonso amada nkhaŵa pamene alibe matenda enieni.”
Mawu oterowo angakhale okhwethemula, ndipo amakhala vuto lalikulu ponena za CFS. “Kupweteka kwa mtima kochititsidwa ndi kusuliza kwakuti ‘simumadzilimbikitsa’ nkosaneneka,” anatero Betty, wodwala CFS mu Utah, “ndipo ndiko mbali yoipitsitsa yakuvutika kumene CFS imachititsa.”
Kumvetsetsa ndi Chikondi Nzofunika
Betty anasonyeza malingaliro mwina a wodwala CFS aliyense pamene anati: “Sitimafuna chisoni. Sitimafuna chifundo. Koma, kalanga ine, timafuna kutimvetsetsa chotani nanga! Mulungu amadziŵa mavuto ndi chisoni chathu, ndipo ndicho chofunika koposa. Koma nkofunikanso kuti tipeze chichirikizo cha maganizo kwa abale ndi alongo athu Achikristu.”
Komabe, kwa anthu ambiri, CFS yakhalabe yovuta kuimvetsetsa, monga momwe wodwala wina wachichepere wa ku mzinda wa Washington ananenera posachedwapa. “Chinthu chimene ndingakonde kwambiri kuti anthu akhale nacho ndicho kudziyika mu mkhalidwe wa ena,” iye anatero, “osati chifundo, koma kudziyika mu mkhalidwe wa ena. Ndipo zimenezo sizotheka chifukwa chakuti sianthu ambiri amene anadwalapo matendaŵa.”
Komabe, sikuyenera kukhala kosatheka kumvetsetsa odwala CFS. Nzowona, mwina sitingathe kudziŵa mkhalidwe wa thupi lawo. Koma tikhoza kuphunzira ponena za nthenda yawo kufikira pamene timvetsetsa mmene akuvutikira ndi matendawo. Mosiyana ndi AIDS, imene imapha, wodwala wina anafotokoza kuti, CFS “imangokupangitsani kufuna kuti mungofa.” Deborah, amene anadwala mu 1986, anavomereza kuti: “Kwanthaŵi yaitali, ndinapemphera kwa Mulungu usiku uliwonse kuti andilole ndife.”—Yerekezerani ndi Yobu 14:13.
Ndithudi, timafuna kukhala olimbikitsa, kuthandiza odwalawo kulimbana ndi vuto la CFS, koma mwatsoka mawu athu angachite zosiyana. Mwachitsanzo, wozonda wodwala wa cholinga chabwino anapereka lingaliro iri kwa wodwala CFS: “Muyenera kumwa mkaka wofunda usiku. Udzakuthandizani kugona tulo, ndipo mudzakhala bwino pambuyo pa masiku oŵerengeka.” Mawuwo anasonyeza kusamvetsetsa CFS kotheratu. Anapweteka wodwalayo mmalo momthandiza.
Kaŵirikaŵiri odwala angamve kukhala osakhoza kuchita zinthu monga kufika pamisonkhano Yachikristu. Pamene abwera, kuyesayesa kumene amakuchita kungakhale kwakukulu kuposa zimene timalingalira. Chotero mmalo mwakunena zakusapezekapo kwawo pamisonkhano yapita, tingangonena kuti: “Takondwa kwambiri kukuwonani. Ndidziŵa kuti nkovuta nthaŵi zina kuti mubwere, koma ndife okondwa kukuwonani lero.”—Wonani bokosi.
Dongosolo lamitsempha la odwala CFS kaŵirikaŵiri limayambukiridwa, kupangitsa ngakhale zochita ndi anthu za masiku onse kukhala zovuta. “Tiyenera kukhala wotetezera pakati pa iwo ndi ena,” anafotokoza motero Jennifer, amene mwamuna wake ali ndi CFS. “Tiyenera kuwathandiza mwakuwalola kuchita zofuna zawo, mwakusawakwiyira, ndi mwakuwathandiza kupeŵa mkangano uliwonse.”
Jennifer anavomereza kuti nthenda ya odwalawo ingakhale yothodwetsa kwa ziwalo za banja, zimene zingatope ndi kuwachitira chirichonse. Koma monga momwe ananenera, ngati odwalawo samaloledwa kupuma, kudzatenga nthaŵi yaitali kuti achire, ndipo motero aliyense adzavutika. Mokondweretsa, nthendayo mwachiwonekere simayambukira kaŵirikaŵiri ndipo kaya ngati imatero nkomwe, ngakhale kuti pakuwonekera kukhala kuthekera kwa m’majini kochititsa nthendayo.
Tottie, wodwala CFS ndipo mkazi wa woyang’anira woyendayenda wa Mboni za Yehova, ananena kuti kwa zaka zambiri mwamuna wake anamthandiza kulimbana ndi vuto la nthenda yake. Amamuuza ponena za chiyamikiro chake komanso anati: “Mabwenzi kaŵirikaŵiri amafunsa ponena za ine ndi mkhalidwe wanga, koma Ken amafunikira chithandizo nayenso.”
Kudziŵiratu Kwabwino—Koma Kwaupandu
CFS simapha kaŵirikaŵiri ndipo kaya ngati imatero nkomwe. Chidziŵitso choterocho chingakuthandizeni kulimbana ndi vutolo. Ochuluka amapezapo bwino mkupita kwanthaŵi, ndipo ambiri amachira. Dr. Anthony Komaroff ananena kuti: “Pakati pa mazana ambiri amene tapenda odwala nthendayo, palibe ngakhale mmodzi amene nthenda yake inapitirizabe kukula mosalekeza. Palibe amene anadwalapo motero. Chotero mosiyana ndi matenda ena amene amakula mosalekeza, nthendayi njosiyana.”
Povomereza zimenezo, Dr. Andrew Lloyd, wofufuza CFS wotchuka mu Australia, anati: “Pamene munthu achira, ndipo tikhulupirira kuti zimenezo zimachitika kaŵirikaŵiri, kuchirako kumakhala kotheratu. . . . Chotero, izi zimatanthauza kuti uliwonse umene uli mchitidwe umenewu umene umachititsa kutopa kumeneku umawongoleredwa kotheratu.” Mwachiwonekere odwalawo samakhala ndi kuvulala kulikonse kwa ziwalo kowonekera atachira.
Deborah, amene nthaŵi zonse anapempherera kufa chifukwa cha kudwala kwambiri, anapezapo bwino potsirizira pake. Akupeza bwino monga momwe analiri kale ndipo posachedwapa anati akukonzekera kugwirizana ndi mwamuna wake muuminisitala wanthaŵi zonse. Enanso achira mofananamo. Komabe, tifunikira kuchenjera. Chifukwa ninji?
Keith, amene ankangodwaladwala nthendayo, anachenjeza kuti: “Nkofunika kwambiri kusachepetsa kuwopsa kwa nthendayi, osafulumira kuganiza kuti yatha.” Pamene anadzimva kuti anapezanso bwino, Keith analoŵanso uminisitala wanthaŵi zonse ndi kuyambanso maseŵera ake olimbitsa thupi, akumathamanga ndi kunyamula zitsulo zolemera nthaŵi zonse. Koma, mwatsoka, nthendayo inabweranso, ndipo anabwereranso m’kama!
Umenewu ndiwo mkhalidwe wachiphamaso wa nthendayi; imabwerera kaŵirikaŵiri. Komabe, mkhalidwewo ngovuta kuupeŵa. Monga momwe Elizabeth anafotokozera kuti: “Nkovuta kupeŵa kuchita zinthu zimene munaphonya panthaŵi imene inawonongeka pamene muyamba kupeza bwinopo. Mumafuna kwambiri kuiŵala ponena za matendawo—mumafuna kuchita zinthu.”
Motero pamafunikira kudziletsa kwakukulu ndi kuleza mtima kuti mulimbane ndi CFS.
Zimene Odwalawo Angachite
Nkofunika kwambiri kuti odwala akhale odziŵiratu za kusatsimikizirika kwa nthenda yalizunzo. Beverly, wodwala kwa nthaŵi yaitali, anafotokoza kuti: “Pamene ndiyamba kulingalira kuti ndikupeza bwino m’milungu kapena miyezi imene ndimapezako bwino, kaŵirikaŵiri ndimadwalanso kuposa pakale paja. Chotero nthaŵi zonse ndimayesayesa kuvomereza malingaliro anga olakwa.” Keith anati: “Mwinamwake chofunika koposa ndicho kuleza mtima.”
Odwala CFS afunikira kusunga nyonga yawo ndi kulola matupi awo kuchira. Chifukwa chake, awo amene akulimbana mwachipambano ndi CFS amasonyeza phindu la chimene chimatchedwa chithandizo cha kupuma kodzikakamiza. Izi zimatanthauza kukonzekera modzikakamiza kaamba ka zochitika zirinkudza mwakupuma kwambiri pasadakhale. Monga chotulukapo, odwala CFS angathe kufika pamisonkhano yaikulu Yachikristu kapena zochitika zina zapadera popanda kudwala pambuyo pake chifukwa cha kutopa kwambiri.
Chofunikanso, ndicho kukhala ndi maganizo okhazikika ndi abata, popeza kuti kupsinjika mtima kukhoza kubutsanso nthendayo mosavuta monga momwe kudzitopetsa kungachitire. Chotero, uphungu wabwino ngwakuti: “Musataye nyonga yanu mwakudzitchinjiriza kwambiri ndi mawu.” Inde, peŵani kuyesa kufotokoza mkhalidwe wanu kwa anthu okaikira amene samvetsetsa.
Ngati mukudwala CFS, mufunikira kukumbukira kuti sizimene ena amakulingalirani zimene ziri kanthu koma zimene Mlengi wathu, Yehova Mulungu, amalingalira. Ndipo iye amazindikira mkhalidwe wanu ndipo amakukondani kwambiri kaamba ka zirizonse zimene mumachita kumtumikira. Muyenera kukhulupirira kuti Yehova ndi angelo ake akuwona, osati kuchuluka kwa ntchito zanu, koma, monga momwe zinaliri kwa Yobu, kaimidwe kanu ka maganizo, chipiriro, ndi kukhulupirika.
Susan, yemwe wabindikiritsidwa ndi CFS pafupifupi kwa zaka ziŵiri, anawona kuti umodzi wa mikhalidwe yoipitsitsa ya CFS ndiwo wakuti munthu angawone moyo kukhala ulibenso chifuno. Chotero akulangiza kuti: “Pezani zinthu zimene zimakupatsani chisangalalo kapena chikhutiro. Ndiri ndi maluŵa okongola a mu Afirika amitundu itatu, ndipo masiku onse ndimawayang’ana kuwona mphukira zatsopano.” Koma chofunika koposa, iye akutero, ndicho “kudalira Yehova kupyolera m’pemphero ndi kuika patsogolo zinthu zanu zauzimu.”
Odwala ambiri amanena kuti kwakhala kowathandiza kumvetsera Baibulo ndi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zojambulidwa pakaseti. Moyenerera, Priscilla, wotchulidwa m’nkhani yachiŵiri, ananena kuti pamene munthu aleka kulingalira zimene anataikiridwa, “CFS simakhala yodetsa nkhaŵa kwambiri.” Iye anati: “Kuti ndipeŵe kulingalira kuti mkhalidwewu udzapitiriza nthaŵi zonse, ndaika malemba olimbikitsa osiyanasiyana m’malo owonekera bwino m’chipinda changa.”
Bwanji Ponena za Kuchiritsa?
Pakali pano palibe chimene chingachitidwe kwenikweni mwanjira ya mankhwala kusiyapo kusamalira zizindikiro za nthendayo. Panali chiyembekezo chachikulu cha mankhwala oyesedwa a Ampligen. Ambiri amene anagwiritsira ntchito mankhwalawo anawonekera kupezapo bwino, koma ziyambukiro zake zoipa kwa ena zinachititsa bungwe la Food and Drug Administration la ku United States kuyamba laletsa kuwagwiritsira ntchito.
Odwala CFS ambiri amakhala ndi mavuto a kudodometseka kwa tulo, kuphatikizapo vuto la insomnia (kusapeza tulo kapena kubalalika kwa tulo). Mokondweretsa, mankhwala oletsa kuchita tondovi—nthaŵi zina mbali yaing’ono kwambiri ya mankhwalawo—imathandiza ena odwala, koma osati onse, kugona bwinopo ndipo motero amapezapo bwino. Beverly anapeŵa mankhwala oterowo kwa zaka zambiri ndiyeno nkudzawayesa. “Anandithandiza kwambiri,” iye anatero, “bwenzi ndikadayamba msanga.”
“Njira zina zambiri zochiritsira [kuphatikizapo “zoloŵa m’malo” zija zozoloŵereka zimene odwala ena amazipeza kukhala zabwino pamene zozoloŵerekazo zilephera] zayesedwa kuchiritsira CFS,” inatero The Female Patient. “Izi zimaphatikizapo mankhwala osiyanasiyana, chithandizo chakulimbitsa thupi popanda mankhwala, . . . acupuncture, homeopathy, naturopathy, anticandidal therapy, ndi njira za sayansi yamakhwala ya Ahindu, pakati pa zina.”
Magazini amankhwala ameneŵa analimbikitsa kuti: “Mosasamala kanthu ndi zimene dokotalayo amazikhulupirira, ayenera kudziŵa zina ponena za [njira zochiritsirazo] kuti amvetsetse ndi kupereka uphungu wabwino kwa wodwalayo. Odwala ambiri amakondwa kungopeza dokotala amene amawamvetsera ndi amene amalingalira mwamphamvu madandaulo awo. . . . Odwala CFS ambiri angathandizidwe kupeza bwinopo—ngakhale ngati angotsimikiziridwa ndi dokotalayo kuti adzakhala wowathandiza—ndipo ambiri akhoza kuthandizidwa.”
Popeza kuti palibe kuchiritsa kulikonse, ena amakaikira ubwino wa kupita kwa dokotala. Phindu lalikulu lakufuna chithandizo choterocho nlakuti kupima kungapatulepo matenda ena amene angakhale ndi zizindikiro zofanana, monga ngati kansa, kupuwala, zithupsa, ndi matenda oyambukira khungu. Ngati nthendazi zazindikiridwa mwamsanga, zikhoza kuchiritsidwa. Emergency Medicine ikulangiza madokotala kuti: “Mutaipeza CFS, njira yabwino koposa ndiyo kutumiza wodwalayo ku chipatala cha chronic fatigue syndrome [nthenda yakutopa kwalizunzo].”
Kupuma ndiko njira yochiritsira yabwino koposa, koma pafunikira kusamala. Chotero uphungu wabwino koposa ndiwo wakuti: Phunzirani kuchita zinthu mosapambanitsa. Dziŵani malire anu, ndipo chitani zinthu mosaposa malirewo, tsiku ndi tsiku, mlungu ndi mlungu, mwezi ndi mwezi. Maseŵera pang’ono olimbitsa thupi, monga ngati kuyenda kapena kusambira m’dziŵe lofunda, angakhale othandiza malinga ngati sachitidwa kufikira pakutopa kaya mwakuthupi kapena mwamaganizo. Kadyedwe kabwino kamene kamathandiza kulimbitsa dongosolo lotetezera thupi nkofunikanso.
Matendaŵa angachititsenso kutaya chiyembekezo, monga momwe zinachitikira mwachisoni kwa wodwala wina wotchedwa Tracy amene anataya mtima ndi kudzipha. Koma imfa sindiyo yankho. Monga momwe bwenzi lake lochita chisoni linanenera kuti: “Ndidziŵa chimene Tracy anafuna kwenikweni. Sanafune kufa. Anafuna kukhalabe ndi moyo—koma kukhala ndi moyo popanda kuvutika. Ndipo chimenecho chiyenera kukhala chonulirapo chathu.” Inde, ndicho chonulirapo chabwino koposa. Chotero sumikani chiyembekezo chanu, osati pakufa, koma pakukhalabe ndi moyo kuti mufikire chonulirapocho, paliponse pamene chidzafikira.
CFS ndiyo imodzi ya matenda osadziŵika yowonjezera pandandanda ya miliri imene yakantha mtundu wa anthu lerolino. Mosasamala kanthu za kupita patsogolo kumene asayansi yamankhwala angakupange, padzafunikira wina woposa akatswiri amankhwala kuti yonse ichiritsidwe. Dokotala Wamkulu, Yehova Mulungu, akufuna kuchita zimenezo—kuchiritsa matenda onse apadziko—kupyolera mwa ulamuliro wachikondi wa boma la Ufumu wake. Panthaŵiyo “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” Ili ndilo lonjezo la Mulungu lotsimikizirika!—Yesaya 33:24.
[Bokosi pamasamba 12, 13]
Mmene Ena Angathandizire
Zimene Simuyenera Kunena ndi Kuchita
◆ “Mukuwoneka bwino ndithu” kapena, “Simukuwoneka wodwala.” Kunena zimenezo kumapangitsa wodwalayo kulingalira kuti simukhulupirira kuwopsa kwa zizindikiro za matenda ake.
◆ “Nanenso ndikumva kutopa.” Mawuŵa amapeputsa kuvutikako. CFS imaphatikizapo zoposa kutopa kokha. Ndinthenda imene imapweteka, ndi yofooketsa.
◆ “Inetu ndatopa. Mwina nanenso ndidzadwala CFS.” Kumeneku kungakhale kuseka, koma CFS sinthenda yochita nayo nthabwala.
◆ “Koma inenso ndatopa, ndingakonde kukhala patchuthi kwamasiku angapo kuti ndipumeko.” Odwala CFS sali patchuthi.
◆ “Munali kugwira ntchito kwambiri. Nchifukwa chake mwadwala.” Wodwala angalingalire zimenezi kukhala mukumuuza kuti anadzidwalitsa yekha.
◆ “Kodi muli bwanji?” Musafunse pokhapo ngati mufunadi kudziŵa. Kunena zowona, wodwala kaŵirikaŵiri amakhala akuvutika kwambiri koma sangafune chabe kudandaula.
◆ “Ujeni nayenso anali ndi Cfs, koma anadwala kwa chaka chimodzi chokha.” Wodwala CFS aliyense amasiyana pautali wa nyengo ndi ukulu wa nthendayo, ndipo kutchula kuchira msanga kwa munthu wina kungakhale kokhwethemula kwa wodwala kwa nthaŵi yotalikirapo.
◆ Musapereke uphungu wa mankhwala pokhapo ngati mwafunsidwa ndipo ndinu woyeneretsedwa kutero.
◆ Musapangitse odwala CFS kulingalira kuti ngati kudwalako ndikuja kobwerezabwereza, ziyenera kukhala chifukwa cha chinachake chimene anachita.
Zimene Muyenera Kunena ndi Kuchita
◆ Sonyezani kuti mumakhulupirira kuti iwo alidi odwala.
◆ Ayimbireni foni, kapena kukawazonda. Kuthanga mwaimba foni kaŵirikaŵiri kumakhala lingaliro labwino.
◆ Tsatirani ziletso zirizonse za kuwona odwala kapena mafoni.
◆ Ngati sikuloledwa kuzonda munthuyo, tumizani khadi kapena kalata. Odwala kaŵirikawiri amayembekezera kulandira makalata tsiku lirilonse.
◆ Khalani achifundo. Nthaŵi zina kumangofunikira kumvetsetsa mkhalidwe wa wodwalayo.
◆ Atumikireni, kaŵagulireni zakudya zimene amafuna ndi zinthu zina ku masitolo, apititseni kwa dokotala, ndi zina zotero.
◆ Mungangonena kuti: “Tisangalala kwambiri kukuwonani. Yehova amadziŵa bwino lomwe kupirira kwanu mwachikhulupiriro.”