Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 8/08 tsamba 29
  • “Tikukuthokozani Chifukwa Chokonda Kwambiri Anthu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Tikukuthokozani Chifukwa Chokonda Kwambiri Anthu”
  • Galamukani!—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Russia
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Anthu Okonda Mtendere Akuyesetsa Kuti Anthu Asaipitse Mbiri Yawo
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Mboni za Yehova ku Russia
    Galamukani!—1997
  • Inali Yoyamba Zaka 100 Zapitazo
    Galamukani!—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—2008
g 8/08 tsamba 29

“Tikukuthokozani Chifukwa Chokonda Kwambiri Anthu”

YOLEMBEDWA KU RUSSIA

◼ Mumzinda wa Chita kummawa kwa Siberia, mpingo wina wa Mboni za Yehova usanasamukire m’Nyumba ya Ufumu yatsopano, unkachitira misonkhano yachikhristu m’kalasi pasukulu inayake. Mbonizo zinkayesetsa kwambiri kuyeretsa kalasiyo, kukonza zowonongeka ndiponso zinali zokoma mtima ndi zaulemu. Poona zimenezi, akuluakulu apasukuluyi analemba kalata yoyamikira mpingowo.

M’kalatayo, iwo anati: “Tikukuthokozani chifukwa chokonda kwambiri anthu, ndipo zimenezi zimaonekera kwa munthu aliyense amene mwakumana naye. Tikuthokozanso chifukwa cha ntchito yanu yolalikira ndi yothandiza anthu m’dera lathu. Sitidzaiwala zinthu zabwino zimene taphunzira kwa inu pa zaka zonse zomwe takhalira limodzi. Zatisonyeza kuti anthu amene amakhulupirira Mulungu ndi abwino, akhama ndi okoma mtima, komanso ndi anthu ofunitsitsa kukwaniritsa zolinga zawo, achikhulupiriro ndiponso moyo wawo umakhala ndi cholinga.” Mboni za Yehova zikusangalala kumva mawu amenewa.

◼ Kumadzulo kwa mzinda wa Chita, pamtunda wa makilomita pafupifupi 5,500, woimira nthambi ya Mboni za Yehova ku Russia anaitanidwa ku mwambo wapadera umene akuluakulu a boma la St. Petersburg anakonza. Kodi anaitanidwa chifukwa chiyani? Chaka chilichonse chipale chofewa chikasungunuka, Mboni zakumeneko zimathandiza kuchotsa zinyalala zomwe zimaunjikana mu msewu wa pafupi ndi nthambi, wamakilomita 60. Posonyeza kuyamikira mtima wofuna kuthandiza anthu umenewu, mkulu wa boma anapereka satifiketi kwa woimira nthambiyo. Anthu amene anali pa mwambowu anawombera m’manja mosangalala. Chochititsa chidwi ndi chakuti mmodzi wa akuluakulu amene analankhula pa mwambowu atalephera kutchula bwino dzina la Mulungu lakuti Yehova, mwamsanga anthu ambiri pamwambowu amene si Mboni anamuwongolera, kusonyeza kuti anthuwo amadziwa bwino dzina la Mulungu ndiponso anthu amene amadziwika ndi dzinalo.

Ku Russia, Mboni za Yehova zilipo pafupifupi 150,000, ndipo n’zodziwika bwino chonchi chifukwa cha ntchito yawo yolalikira kwa anthu onse. Cholinga chawo ndi chakuti apitirize ‘kukonda kwambiri anthu,’ mwa kulalikira uthenga wolimbikitsa wa m’Baibulo kwa anthu ofuna kumva.—Mateyo 22:39.

[Chithunzi patsamba 29]

Nthambi ya ku Russia inalandira satifiketi yoyamikira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena