Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 1/09 tsamba 17
  • Mlomo wa Mbalame Yotchedwa Toucan

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mlomo wa Mbalame Yotchedwa Toucan
  • Galamukani!—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Mlomo Wochititsa Chidwi wa Nyama ya M’madzi
    Galamukani!—2009
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2009
  • Mlomo wa Nankapakapa
    Galamukani!—2010
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—2009
g 1/09 tsamba 17

Panagona Luso!

Mlomo wa Mbalame Yotchedwa Toucan

◼ Mbalame ya toucan, imene imapezeka ku Central ndi ku South America, siikonda kuuluka ndipo imadalira kudumpha. Mbalame zina zamtunduwu zikamalira, mawu ake amafanana ndi a chule, koma ndi aakulu moti amatha kumveka m’nkhalango pamtunda wa pafupifupi kilomita imodzi. Koma mwina chimene asayansi amadabwa nacho kwambiri ndi mbalameyi, ndi mlomo wake.

Taganizirani izi: Mlomo wa mbalame zina zamtunduwu ndi wautali pafupifupi theka la utali wa mbalame yonseyo. Umaoneka ngati wolemera kwambiri, koma si choncho. Katswiri wina wa sayansi, dzina lake Marc André Meyers, anati: “Kunja kwa mlomowu kunapangidwa ndi puloteni yotchedwa keratini imene imapezekanso m’zikhadabo ndi m’tsitsi. Khungu la mlomowu lili ndi tizinthu ting’onoting’ono tamabokosimabokosi toyalana ngati matailosi padenga.”

Mlomo wa mbalameyi umakhala ngati chinkhupule cholimba kwambiri. Mbali zina zili ndi mphako, pamene mbali zina zili ndi khungu komanso zochirikizira. Chifukwa cha zimenezi, mlomowu ndi wopepuka koma wolimba kwambiri. Meyers anati: “Zikukhala ngati mbalame ya toucan ili ndi luso la zopangapanga.”

Kapangidwe ka mlomo wa mbalameyi kamaithandiza kuti isavulale ngakhale itamenyetsa mlomowu pazinthu zolimba. Asayansi amakhulupirira kuti akatswiri opanga ndege ndi galimoto atatengera kapangidwe ka mlomo wa mbalameyi, angamapange zinthu zabwino kwambiri. Meyers anati: “Ngati mbali zina za galimoto atamazipanga motengera kapangidwe ka mlomo wa [mbalameyi] zingateteze kwambiri oyendetsa galimoto patachitika ngozi.”

Ndiyeno kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika kuti mlomo wa mbalame ya toucan ukhale wolimba koma wopepuka? Kapena kodi pali amene anaupanga?

[Chithunzi patsamba  17]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Mphako

Mbali yooneka ngati chinkhupule

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena