Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 4/09 tsamba 27
  • Masamba a Kakombo Sanyowa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Masamba a Kakombo Sanyowa
  • Galamukani!—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2009
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2004
Galamukani!—2009
g 4/09 tsamba 27

Panagona Luso!

Masamba a Kakombo Sanyowa

◼ Kodi munaonapo makapu apulasitiki omwe amadzichapa okha? Kapena mawindo omwe sanyowa akavumbidwa ndi mvula? Kapenanso makina omwe sawonongeka ndi madzi? Asayansi akuti zimenezi ndi zinthu zochepa chabe zimene angathe kupanga ngati atadziwa chinsinsi cha tsamba la kakombo.

Taganizirani izi: Tsamba la kakombo lili ndi timatuza ting’onoting’ono tomwe n’tokutidwa ndi mafuta olimbirapo ngati a kandulo. Madontho a madzi akagwera patsambali amaterereka chifukwa limaima mopendekeka. Chifukwa cha zimenezi, tsambali silinyowa komanso limakhala loyera chifukwa madontho a madziwo amachotsa fumbi.

Asayansi akufuna kupanga zinthu zoti zisamanyowe ndi madzi ngati tsamba la kakombo. Nzeru zimenezi zingathandize popanga makina oti asamawonongeke ndi madzi. Magazini ina inati asayansi “angapange zinthu zambiri potengera tsamba la kakombo.”—Science Daily.

Ndiyeno kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi tsamba la kakombo linakhalako lokha, kapena linachita kulengedwa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena