Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 2/10 tsamba 21
  • Mleme Waung’ono Kwambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mleme Waung’ono Kwambiri
  • Galamukani!—2010
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Sipezekapezeka
  • Luso la Mleme Loona Zinthu Ndi Makutu
    Kodi Zinangochitika Zokha?
  • Alimi Odziwa Kusamalira Nkhalango
    Galamukani!—2014
  • Mapiko a Zamoyo Zouluka
    Galamukani!—2009
  • Wamkulu Kwambiri Ndiponso Wamng’ono Kwambiri
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 2/10 tsamba 21

Mleme Waung’ono Kwambiri

● Mu 1973, katswiri wina wa zinthu zamoyo, dzina lake Kitti Thonglongya, ndi anzake anagwira mileme yosiyanasiyana yoposa 50 m’phanga linalake pafupi ndi mathithi otchedwa Sai Yok ku Thailand. Iye anatumiza ina mwa milemeyi kwa Dr J. E. Hill yemwe amagwira ntchito kumalo osungira zinthu zakale mumzinda wa London. N’zomvetsa chisoni kuti Kitti anamwalira asanadziwe kuti pa mileme yomwe anatumizayo, panali mtundu wina watsopano, womwe Hill anaupatsa dzina la katswiriyu n’cholinga choti anthu azimukumbukira.

Mileme imeneyi ndi yaing’ono kwambiri kuposa mileme ina yonse yomwe anthu akuidziwa ndipo ili m’gulu la zinyama zing’onozing’ono kwambiri padziko lonse. Ndi yaitali pafupifupi masentimita atatu ndipo mapiko ake amatalika pafupifupi masentimita 13. Ili ndi mphuno yooneka ngati ya nkhumba komanso ilibe mchira ndipo makutu ake ndi aakulu.

Sipezekapezeka

Mileme imeneyi imangopezeka ku nkhalango yotetezedwa ya Sai Yok ku Thailand ndi ku Myanmar basi. Mofanana ndi mileme ina, milemeyi ikamafufuza chakudya monga tizilombo, imalira ndipo phokosolo limathandiza milemeyi kudziwa mmene iyendere kuti ikapeze chakudyacho. Komanso popeza kuti ili ndi mapiko okulirapo poyerekezera ndi thupi lake, milemeyi imatha kuuluka malo amodzimodzi kwa nthawi yaitali. Zimenezi zimathandiza kuti izitha kugwira chakudya chake m’mitengo popanda kutera. Milemeyi imakonda kukhala m’malo otentha m’mapanga. Imakonda malo amenewa chifukwa chakuti imakhala yotetezeka komanso m’malowa mumatentherako. Zimene mileme yaing’ono imeneyi imachita n’zogometsa ndipo zimasonyeza kuti Mlengi ndi wanzeru.—Chivumbulutso 4:11.

Popeza kuti milemeyi imapezeka m’madera ochepa kwambiri, ngati anthu atapanda kusamala, milemeyi ikhoza kutheratu. Anthu ena akuyesetsa kupeza njira zotetezera milemeyi, koma kudula mitengo mwachisawawa, kulambula misewu komanso kuchuluka kwa alendo odzaona malo, zikusokoneza ntchito yoteteza milemeyi moti sizikudziwika ngati ikhalekobe m’tsogolomu.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 21]

MILEME ILIPO YAMITUNDU YOSIYANASIYANA

Padziko lonse pali mitundu pafupifupi 1,000 ya mileme ndipo pa zinyama zonse ndi mleme wokha umene umauluka. Mileme yaikulu kwambiri imalemera pafupifupi kilogalamu imodzi ndipo mapiko ake amatha kufika mamita 1.5 (1). Pamene mileme yaing’ono kwambiri imalemera magalamu awiri ndipo mapiko ake amatha kufika masentimita atatu (2).

[Mawu a Chithunzi patsamba 21]

Photos: © Merlin D. Tuttle, Bat Conservation International, www.batcon.org

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena