Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 10/14 tsamba 12-13
  • Alimi Odziwa Kusamalira Nkhalango

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Alimi Odziwa Kusamalira Nkhalango
  • Galamukani!—2014
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Milemeyi Imafesera Mbewu
  • Mmene Imaswera Komanso Kusamalira Ana
  • Luso la Mleme Loona Zinthu Ndi Makutu
    Kodi Zinangochitika Zokha?
  • Mleme Waung’ono Kwambiri
    Galamukani!—2010
  • Mapiko a Zamoyo Zouluka
    Galamukani!—2009
  • Zochitika Padzikoli
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—2014
g 10/14 tsamba 12-13
Mleme ukudya zipatso mumtengo

Alimi Odziwa Kusamalira Nkhalango

ALIMI ambiri amadziwa zoti, kuti akolole zambiri amayenera kudzala pa nthawi yake komanso pamalo oyenera. Koma n’zochititsa chidwi kuti pali alimi ena amene amadzala mbewu zawo usiku ndipo amadzala akuuluka. Alimi amenewa ndi mileme ya m’nkhalango ndipo chifukwa choti imakhala yaikulu ena anaipatsa dzina loti nkhandwe zouluka.a

Mmene Milemeyi Imafesera Mbewu

Mileme imeneyi imakonda kuuluka usiku m’nkhalango n’kumadya zipatso. Imamwanso timadzi totsekemera tam’maluwa. Zitosi za milemeyi zimakhala ndi nthangala za zipatso ndipo milemeyi imagwetsa zitosizi ili m’malere. Nthangalazo zikagwera pansi, zimamera n’kukhala mitengo. Komanso milemeyi ikamamwa madzi a m’maluwa imatenga mungu, kapena kuti poleni, kuchoka m’mitengo ina kupita m’mitengo ina.

Popeza milemeyi imauluka mtunda wautali pofunafuna chakudya, imatha kufesa mbewu m’dera lalikulu. Ndiponso popeza ikamauluka imamwaza zitosi, zitosizi zimathandiza kuti nthaka ikhale yachonde ndipo mbewu zimakula bwino. Choncho kuti mitengo yambiri m’nkhalango imere, ikule bwino komanso ibale zipatso, imadalira milemeyi.

Milemeyi imaona kwambiri ndipo ili ndi luso lotha kudziwa kumene ikupita. Zimenezi n’zimene zimaithandiza kuti izitha kuuluka mtunda wautali m’nkhalango. Ngakhale pamalo a mdima, milemeyi imaona bwino kuposa anthu ndipo imatha kusiyanitsa mitundu ya zinthu. Imathanso kuuluka usiku komanso masana mosavuta.

Mmene Imaswera Komanso Kusamalira Ana

Mleme

KODI MUKUDZIWA? Mileme ya mitundu ina ikafuna kudziwa ngati pali chakudya pafupi, imakuwa ndipo imamvetsera mmene phokosolo likumvekera. Koma mileme ya m’nkhalangoyi imadziwa kumene kuli zipatso chifukwa choti imaona zipatsozo komanso imamva fungo. Milemeyi ili ndi maso akuluakulu ndipo n’chifukwa chake imatha kuona bwinobwino usiku

Pali mitundu ina, yomwe imapezeka ku Samoa imene imakwatirana ndipo imakhala limodzi kwa moyo wawo wonse. Kafukufuku wina anasonyeza kuti mileme ina yaikazi imasamalira bwino ana ake. Mwachitsanzo, imawanyamula kulikonse kumene ikupita komanso imawayamwitsa mpaka atakula. Mleme waukazi wa mtundu wina umatha kukhala mzamba, mleme unzake ukamaswa.

Koma chomvetsa chisoni n’chakuti mileme yambiri yamtunduwu ikhoza kutheratu chifukwa anthu akuwononga nkhalango. Izi zingabweretse mavuto akulu. Mwachitsanzo, pazilumba zina za ku South Pacific pali mitengo ina yomwe singabale zipatso popanda milemeyi. Mitengoyi imadalira milemeyi kuti itenge poleni pamaluwa a mtengo wina kupita pamtengo wina. Apatu taona kuti milemeyi ndi yofunika kwambiri chifukwa imathandiza kuti nkhalango zisathe.

a Milemeyi imapezeka ku Africa, Asia, Australia ndi madera ena kuzilumba za m’nyanja ya Pacific.

MILEMEYI IMATHANDIZA KUTI NKHALANGO ZISATHE

Mtengo wa mlambe

Maluwa a mtengo wa malambe amakhala kwa maola 24 basi kenako amanyala. Koma pa nthawi yochepa yomweyi, milemeyi imadziwa kuti mitengoyi yachita maluwa ndipo imapita kukamwa madzi otsekemera a maluwawa. Ikamachoka pa maluwawo imatenga poleni ndipo imakamusiya pamaluwa a mtengo wina

Mitengo ya m’nkhalango ikadulidwa, milemeyi imathandiza kuti m’nkhalangomo mumerenso mitengo ina. Kuti izi zitheke, milemeyi imafesanso mbewu za mitengo zomwe zimakula n’kukhala mitengo ikuluikulu. Poganizira zimenezi, buku lina linanena kuti: “Kuti anthufe tikhale ndi thanzi labwino timafunika mitengo, ndipo mileme ya m’nkhalango imathandiza kuti mitengo isathe.”—Bats of the World, lolembedwa ndi Gary L. Graham.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena