Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 5/10 tsamba 24-31
  • Zoti Banja Likambirane

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zoti Banja Likambirane
  • Galamukani!—2010
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Anaganiza Bwino?
  • KODI MUKUDZIWA CHIYANI ZOKHUDZA MFUMU YEHOSAFATI?
  • ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE
  • KUCHOKERA M’MAGAZINI INO
  • MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2010
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2008
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2010
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 5/10 tsamba 24-31

Zoti Banja Likambirane

Kodi Anaganiza Bwino?

Werengani Maliko 14:66-72. Kenako yang’anani pa chithunzichi ndipo lembani mayankho anu m’mizere imene ili m’munsimu.

1. Kodi zimene mukuona pachithunzichi zinachitikira kuti?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Maliko 14:53, 54.

․․․․․

2. Kodi Petulo anatani anthu atamudziwa kuti anali wotsatira wa Yesu?

․․․․․

3. Kodi chinachitika n’chiyani tambala atalira kachiwiri?

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Petulo anachita zimenezi? Kodi inuyo mungapewe bwanji kuchita zinthu ngati zimenezi?

KODI MUKUDZIWA CHIYANI ZOKHUDZA MFUMU YEHOSAFATI?

4. Kodi Yehosafati anakhazikitsa dongosolo lotani pankhani yoweruza milandu ku Yuda?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Mbiri 19:5-11.

․․․․․

5. Kodi Yehosafati analakwitsa chiyani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Mbiri 18:1-3; 19:1-3.

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi nkhani ya Yehosafati ikukuphunzitsani chiyani pankhani yosankha anthu ocheza nawo?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Akorinto 15:33.

ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowekapo.

TSAMBA 4 Kodi tiyenera kuchotsa chiyani kuti tidziyeretse? 2 Akorinto 7::․․․

TSAMBA 5 Kodi anthu awiri amatani? Mlaliki 4::․․․

TSAMBA 19 Kodi anthu anzeru amadalira chiyani? 1 Timoteyo 6::․․․

TSAMBA 27 Kodi inuyo nthawi zambiri mumasangalala pochita chiyani? Machitidwe 20::․․․

● Mayankho ali patsamba 24

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Pabwalo la mkati ku nyumba ya mkulu wa ansembe.

2. Petulo anakana zoti akudziwa Yesu.

3. Petulo analira.

4. Yehosafati anaika oweruza oopa Mulungu m’mizinda, komanso Alevi ndi ansembe ku Yerusalemu.

5. Iye anachita mgwirizano ndi Mfumu yoipa Ahabu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena