Panagona Luso!
Diso la Kadziwotche
● Akadziwotche ndi mtundu wa agulugufe omwe amakonda kuuluka usiku. Maso a zilombo zambiri zoyenda usiku amawala akayandikira moto kapena chinthu china chowala. Koma akadziwotche amatha kubisika chifukwa maso awo sawala ngakhale atayandikira moto kapena magetsi.
Taganizirani izi: Maso a kadziwotche amasiyana ndi maso a zamoyo zina chifukwa ali ndi timabampu ting’onoting’ono kwambiri tosaoneka ndi maso. Timabamputi tinayalidwa m’magulumagulu, ndipo gulu lililonse limakhala ndi timabampu 6. Popeza kuti “timabamputi ndi tating’ono kwambiri, kuwala kukafikapo sikubwerera. Choncho, munthu sangathe kuona kuti masowo akuwala,” anatero Peng Jiang, yemwe ndi mphunzitsi wa sayansi payunivesite inayake ku Florida, United States. Kuyalana kwa timabamputi komanso kuchepa kwake kumachititsa kuti kuwala kochokera ku mbali zosiyanasiyana kukafika m’disolo kusamabwererenso. Timabamputi ndi tating’ono kwambiri moti tikayerekezera kunenepa kwa kabampu kamodzi ndi kunenepa kwa katsitsi ka munthu kamodzi, kabampuko kangalowe m’tsitsimo maulendo pafupifupi 300.
Asayansi akuganiza kuti akadzamvetsetsa bwinobwino mmene diso la kadziwotche limagwirira ntchito, adzatha kupanga ma TV ndi makompyuta osathobwa m’maso. Kapangidwe ka diso la kadziwotche kakhoza kuthandizanso asayansi popanga magetsi oyendera mphamvu ya dzuwa. Malata amene amagwiritsa ntchito masiku ano popanga magetsiwa, amawononga kwambiri mphamvu ya dzuwa chifukwa mphamvu yambiri ikafika pamalatawo imabwerera. Koma potengera kayalidwe ka timabampu ta m’diso la kadziwotche, Jiang ndi anzake anapanga malata abwino kwambiri opangira magetsi oyendera mphamvu ya dzuwa, chifukwa mphamvu ya dzuwa ikafikapo, yambiri siibwerera. Jiang anati: “Tikhoza kuphunzira zambiri kuchokera ku tizilombo timeneti.”
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika mwangozi kuti kuwala kukafika padiso la kadziwotche kusamabwerere, kapena pali winawake amene anapanga disoli mwanjira imeneyi?
[Chithunzi patsamba 30]
Diso la kadziwotche lili ndi timabampu ting’onoting’ono kwambiri. Timabamputi tili m’magulumagulu, ndipo gulu lililonse limakhala la timabampu 6
[Zithunzi patsamba 30]
Malata opangira magetsi ochokera ku mphamvu ya dzuwa amene sawononga mphamvu yambiri ya dzuwa
[Mawu a Chithunzi patsamba 30]
Moth eye close-up: Courtesy of Dartmouth Electron Microscope Facility; silicon close-up: Courtesy Peng Jiang