N’Chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Akukondwerera Khirisimasi Masiku Ano?
KODI inuyo mumasangalala nyengo ya Khirisimasi ikamayandikira, kapena mumada nkhawa? M’mayiko ambiri, nyengo ya Khirisimasi ikamayandikira anthu amadzifunsa kuti: ‘Kodi ndigulire ndani mphatso? Nanga ndigule mphatso zotani? Kodi ndili ndi ndalama zokwanira kugulira mphatsozo? Ngati nditatenga ngongole, kodi zinditengera nthawi yaitali bwanji kuti ndizibweze?’
Ngakhale kuti anthu amakhala ndi nkhawa zimenezi, ambiri amakondwererabe Khirisimasi. Ndipo ngakhale m’mayiko amene si achikhristu, anthu ambiri ayamba kukondwerera Khirisimasi. Mwachitsanzo, ku Japan mabanja ambiri amakondwerera Khirisimasi, osati ngati mwambo wa chipembedzo koma ngati nthawi yosangalala basi. Nyuzipepala ina inanena kuti “m’mizinda ikuluikulu ku China, anthu ayamba kuika zithunzi za Father Christmas m’mawindo a masitolo. Anthu ambiri m’mizindayi akulemera, ndipo iwo ayamba kukondwerera Khirisimasi pongofuna kupezerapo mwayi wogula zinthu zatsopano ndiponso kuchita maphwando.”—The Wall Street Journal.
M’mayiko ambiri, Khirisimasi yathandizira kuti ntchito zamalonda zipite patsogolo. Izi n’zimene zachitika ku China, ndipo nyuzipepala ija inanena kuti panopa dzikoli “likugulitsa kwambiri ku mayiko ena zinthu monga mitengo ya pulasitiki, timapepala tokongoletsera zinthu, timagetsi ndi zokongoletsera zina za pa Khirisimasi.”
M’mayiko achisilamu anthu ayambanso kuchita maphwando ofanana ndi Khirisimasi ngakhale kuti sachitika pa December 25. Mwachitsanzo, mumzinda wa Ankara m’dziko la Turkey, ndi mumzinda wa Beirut m’dziko la Lebanon, si zachilendo kuona m’mawindo a masitolo ataikamo mitengo yokongoletsedwa ndi timapepala, komanso ataika mphatso zokutidwa ndi mapepala okongola pansi pa mitengoyi. Ku Indonesia, mahotela ndi masitolo akuluakulu amakhala ndi masiku apadera amene ana amatha kudyera limodzi ndi Father Christmas kapena kujambulitsa naye.
Magazini ina ya ku Canada (Royal Bank Letter) inati m’mayiko a azungu, Khirisimasi si mwambonso wa chipembedzo ndipo nyengo ya Khirisimasi imangotengedwa ngati nthawi yochitira malonda. Komanso otsatsa malonda ambiri “cholinga chawo chachikulu chimakhala choti akope ana.” N’zoona kuti anthu ena amapitabe kutchalitchi pa Khirisimasi, koma ambiri m’malo mopita kutchalitchi amapita kumasitolo kukagula zinthu zosiyanasiyana. Pa nthawi imeneyi m’masitolowa mumamveka nyimbo zosiyanasiyana za Khirisimasi. N’chifukwa chiyani anthu asintha chonchi? Mwinatu chiyambi cha Khirisimasi n’chimene chikuchititsa zimenezi. Kodi Khirisimasi inayamba bwanji?
Tisanakambirane mafunso amenewa, ndi bwino kuti tiwerenge kaye nkhani za m’Baibulo zimene zimachititsa anthu ena kuti azikondwerera Khirisimasi.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 4]
ZIMENE OLEMBA UTHENGA WABWINO AMANENA
Mtumwi Mateyu: “Yesu atabadwa ku Betelehemu wa Yudeya m’masiku a mfumu Herode, okhulupirira nyenyezi ochokera kum’mawa anabwera ku Yerusalemu. Iwo ananena kuti: ‘Ili kuti mfumu ya Ayuda imene yabadwa? Chifukwa pamene tinali kum’mawa, tinaona nyenyezi yake ndipo tabwera kudzaigwadira.’ Mfumu Herode itamva zimenezi, inavutika mumtima.” Choncho Herode anafunsa “ansembe onse aakulu . . . za kumene Khristu adzabadwire.” Atamva kuti “adzabadwira ku Betelehemu,” Herode anawauza okhulupirira nyenyeziwo kuti: “Pitani mukam’funefune mwanayo mosamala, ndipo mukakam’peza mudzandidziwitse.”
Iwo “anapitiriza ulendo wawo. Kenako nyenyezi imene anaiona ali kum’mawa ija inawatsogolera, mpaka inakaima m’mwamba pamalo pamene panali mwanayo. . . . Atalowa m’nyumbamo, anaona mwanayo ndi mayi ake Mariya.” Atapatsa Yesu mphatso zosiyanasiyana, iwo “analandira chenjezo la Mulungu m’maloto kuti asapitenso kwa Herode, [choncho] iwo anabwerera kudziko lakwawo kudzera njira ina.”
“Okhulupirira nyenyezi aja atachoka, mngelo wa Yehova anaonekera kwa Yosefe m’maloto n’kumuuza kuti: ‘Nyamuka, tenga mwanayu ndi mayi ake ndipo uthawire ku Iguputo . . . ’ Chotero Yosefe anadzuka usiku n’kutenga mwana uja limodzi ndi mayi ake. Anachoka kumeneko kupita ku Iguputo . . . Herode, poona kuti okhulupirira nyenyezi aja am’pusitsa, anakwiya koopsa. Choncho anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna m’Betelehemu ndi m’zigawo zake zonse, kuyambira azaka ziwiri kutsika m’munsi.”—Mateyu 2:1-16.
Wophunzira Luka: Yosefe “anachoka ku Galileya, mumzinda wa Nazareti, n’kupita ku Yudeya, kumzinda wa Davide wotchedwa Betelehemu . . . Anapita kukalembetsa limodzi ndi Mariya . . . Ali kumeneko, . . . anabereka mwana wake woyamba wamwamuna. Anamukulunga ndi nsalu n’kumugoneka modyeramo ziweto, chifukwa anasowa malo m’nyumba ya alendo.”
“M’dzikomo munalinso abusa amene anali kugonera kubusa akuyang’anira nkhosa zawo usiku wonse mosinthana maulonda. Mwadzidzidzi mngelo wa Yehova anaima chapafupi ndi iwo, . . . mwakuti anachita mantha kwambiri. Koma mngeloyo anawauza kuti: ‘Musaope! Ine ndabwera kudzalengeza kwa inu uthenga wabwino wa chimwemwe chachikulu chimene anthu onse adzakhala nacho. Chifukwa lero wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye, mumzinda wa Davide.’” Kenako abusawo “anapita mwachangu ndipo anakapeza Mariya ndi Yosefe, komanso mwana wakhandayo atagona modyeramo ziweto.”—Luka 2:4-16.