Duwa Lalikulu Padziko Lonse
M’CHAKA cha 1818, munthu wina wa ku Britain, dzina lake Joseph Arnold, anapita pachilumba cha Sumatra chomwe chili ku Indonesia, kuti akafufuze mitundu yosiyanasiyana ya maluwa ndi zomera zina. Tsiku lina ali mkati mofufuza, munthu amene ankamulondolera anamuuza kuti: “Bwana, tiyeni mukaone chiduwa chachikulu komanso chokongola kwambiri.” Arnold atapita ndi munthuyo anapeza kuti duwalo linali la mtundu wa rafflesia ndipo linalidi lokongola kwambiri. Panopa patha zaka 200 kuchokera pamene anapeza duwa la mtunduwu ndipo limadziwikabe kuti ndi duwa lalikulu kwambiri padziko lonse.
Pali maluwa osiyanasiyana a mtunduwu omwe amamera m’nkhalango za m’chigawo cha kum’mwera chakum’mawa kwa Asia. Akatswiri adakatulukirabe mitundu ina ya duwa limeneli. Mtundu wa duwali womwe umakula kwambiri amautchula kuti Rafflesia arnoldii potengera dzina la Joseph Arnold ndi mnzake, Sir Thomas Stamford Raffles, yemwe anali bwanamkubwa wa ku Singapore. Koma ngakhale kuti duwali ndi lokongola kwambiri anthu salikonda.
Chifukwa choyamba n’chakuti duwali limakula kwambiri. Limatha kukula ngati tayala la basi yaikulu ndipo limalemera makilogalamu 11.a Limaoneka la pinki womkera ku bulauni ndipo limakhala ndi timadontho tokhala ngati tiziphuphu. Pakati pake pamakhala chibowo chachikulu chokhala ngati poto choti mukhoza kudzaza madzi okwana malita 6.
Chifukwa china chimene anthu sakondera duwali n’chakuti limanunkha. Anthu ena amanena kuti duwali limanunkha ngati “nyama yakufa yomwe ili mphutsi zokhazokha,” moti ena anafika pomaitchula kuti mtembo.b Ntchentche zimakonda maluwa amenewa chifukwa cha fungo lake.
Chodabwitsa n’chakuti duwali lilibe tsinde, masamba kapena mizu. Limamera komanso limapeza zakudya zake pa zomera zina zoyanga pansi. Duwali limamera pang’onopang’ono moti limatenga miyezi 10 kuti likule bwinobwino ndipo likakhala kuti silinatambasule, nthawi zambiri limaoneka ngati kabichi wamkulu. Koma duwali limangotenga maola ochepa kuti lonse litambasule. Pakati penipeni pachibowo cha duwali pamakhala timingaminga. Ntchito yeniyeni ya timingati siidziwika ngakhale kuti akatswiri ena amanena kuti timathandiza kuti duwalo lizitentha, zomwe zimachititsa kuti lizinunkha kwambiri.
Ngakhale kuti duwali ndilokongola chonchi, silichedwa kufa. Pakangotha masiku ochepa litatambasula, limafa n’kuyamba kuola zomwe zimachititsa kuti pamene panali duwalo patsale zinthu zakuda komanso zoterera.
Duwali silipezeka kawirikawiri ndipo akatswiri amanena kuti maluwa amtunduwu atsala pang’ono kutheratu. Zimenezi zikuchitika chifukwa chakuti anthu amathyola maluwa amenewa asanakule n’komwe kuti akadye kapena kuti akachitire mankhwala. Chinanso chimene chikuchititsa kuti maluwa amenewa atsale pang’ono kutheratu n’chakuti anthu akuwononga nkhalango zimene maluwa amenewa amamera.
Kunena zoona duwali ndilochititsa chidwi chifukwa ndilokongola komanso lalikulu kwambiri, ngakhale kuti limanunkha. Duwa limeneli ndi chimodzi mwa zinthu zambiri zimene Mulungu analenga. N’chifukwa chake lemba la Salimo 104:24 limanena kuti: “Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova! Zonsezo munazipanga mwanzeru zanu. Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.”
[Mawu a M’munsi]
a Mitundu ina ya maluwa amenewa imakhala yaing’ono mwina masentimita 10 okha likatambasuka.
b Palinso duwa lina (Amorphophallus titanum) lomwe limadziwikanso kuti limanunkha kwambiri ndipo nthawi zina anthu amalisokoneza ndi duwa la rafflesia.—Onani Galamukani! yachingelezi ya June 22, 2000, tsamba 31.
[Mapu patsamba 17]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
MALAYSIA
SUMATRA
[Chithunzi patsamba 17]
Duwa la rafflesia latsala pang’ono kutambasula