Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 3 tsamba 15-18
  • Uyo Amene Anapanga Zinthu Zonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Uyo Amene Anapanga Zinthu Zonse
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Amene Anapanga Zinthu Zonse
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Mulungu Ayamba Kupanga Zinthu
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Mulungu Analenga Kumwamba ndi Dziko Lapansi
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Kalata Yochokera kwa Mulungu
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 3 tsamba 15-18

Mutu 3

Uyo Amene Anapanga Zinthu Zonse

INE ndikudziwa kanthu kena kodabwitsa. Kodi mungafune kukamva iko?—ayang’anani m’dzanja lanu. Pindani zala zanuzo. Tsopano tolani kanthu kena. Dzanja lanu lingathe kuchita zinthu zambiri, ndipo ilo lingathe kuzichita izo bwino lomwe. Kodi mukumdziwa amene analipanga’ dzanjalo?—Anali Mulungu.

Tsopano tayang’anani kumaso kwanga. Kodi nchiani chimene inu mukuchiona?—Inu mukuona kamwa yanga, mphuno yanga ndi maso anga awiri. Kodi mungazione izo bwanji?—Ndi maso anu. Ndipo kodi ndani amene anawapanga masowo?—Anali Mulungu. Kodi chimenecho sichiri chodabwitsa?—

Inu mungathe kuona zinthu zambiri ndi maso anu. Inu mungathe kuyang’ana maluwa. Inu mungathe kuona mbalame. Inu mungathe kuyang’ana udzu wobiliwira ndi m’mlengalenga mobiliwira.

Koma kodi ndani amene anazipanga zinthu zimenezi?—Kodi munthu wina anazipanga izo?—Ai. Anthu angathe kumanga nyumba. Koma palibe munthu amene angathe kupanga udzu umene umakula. Anthu sangathe kupanga mbalame, duwa kapena kanthu kena kali konse kamoyo. Kodi inu mukuzidziwa zimenezo?—

Mulungu ndiye Uyo amene anazipanga zinthu zonsezi. Mulungu anapanga miyamba ndi dziko lapansi. Iye anawapanganso anthu. Iye analenga mwamuna woyambayo ndi mkazi woyambayo. Yesu, Mphunzitsi Wamkuruyo, anaphunzitsa chimenechi.—Mateyu 19:4-6.

Kodi Yesu anadziwa bwanji kuti Mulungu anapanga mwamuna ndi mkazi? Kodi Yesu anamuonaMulungu akuchita?—Inde, iye anamuona. Yesu anali limodzi ndi Mulungu pamene Mulungu anampanga mwamuna ndi mkazi. Yesu anali munthu woyamba amene Mulungu anampanga. Iye anali mngelo, ndipo iye anakhala ndi moyo ndi kugwira nchito kumwamba limodzi ndi Atate wache.

Baibulo limatiuza ife kuti Mulungu anati: “Tiyeni tipange munthu.” Kodi mukumdziwa amene Mulungu anali kulankhula naye?—Iye anali kumalankhula ndi Mwana wache, uyo amene pambuyo pache anadza ku dziko lapansi ndi kufikira kukhala Mphunzitsi Wamkuru!—Genesis 1:26, NW.

Chinthu chiri chonse chimene Mulungu wachichita chimasonyeza chikondi chache. Mulungu anapanga dzuwa. Dzuwa limatipatse ife kuunika ndipo limatipangitsa ife kumva kutentha. Chinthu chiri chonse chikadakhala chozizira ndipo sipakadakhala moyo pa dziko lapansi ngati ife tikadapanda dzuwa. Kodi inu simuli okondwa kuti Mulungu anapanga dzuwa?—

Mulungu amabvumbitsanso mvula. Nthawi zina inu simungaikonde mvulayo chifukwa chakuti inu simugathe kuturuka kunja kukasewera pamene mvula ikubvumba. Koma mvula imawathandiza maluwa kukula.

Chotero pamene ife tiwaona maluwa okongola, kodi ife tidzathokoza yani kaamba ka iwo?—Mulungu. Ndipo kodi tiyenera kuthokoza yani pamene ife tidya zipatso ndi ndiwo zamasamba zimene zimakoma?—Ife tiyenera kuthokoza Mulungu, chifukwa chakuti ndizo dzuwa ndi mvula yache zimene zimazipangitsa zinthu kukula. Mulungu ali wabwino kwambiri kuchita zinthu zodabwitsa zonsezi kaamba ka ife.

Kodi mukukudziwa kumene Mulungu ali?—Baibulo limatiuza ife kuti Mulungu amakhala kumwamba.

Kodi inu mungathe kumuona Mulungu?—Ai. Baibulo limati: ‘Palibe munthu angathe kumuona Mulungu.’ Chotero palibe munthu ali yense amene ayenera kuyesayesa kuchipanga chithunzithunzi kapena chifaniziro cha Mulungu. Mulungu amatiuzadi ife kuti tisayese kupanga fano la iye. Chotero ife sitiyenera kukhala ndi zinthu zonga zimenezo m’nyumba mwathu, ati?——Eksodo 33:20, 20:4, 5.

Koma ngati inuyo simungathe kumuona Mulungu, kodi mumadziwa motani kuti kulidi Mulungu?—Ganizirani za ichi. Kodi inu mungathe kuiona mphepho?—Ai. Palibe munthu ali yense angathe kuiona mphepo. Koma inu mungathe kuziona zinthu zimene mphepoyo imazichita. Inu mungathe kuwaona masamba akugwedezeka pamene mphepoyo ikuomba kupyola m’nthambi za mtengo. Chotero inu mumakhulupilira kuti kuli mphepo.

Inu mungathenso kuziona zimene Mulungu wazichita. Pamene inu muliona duwa lamoyo kapena mbalame, inu mumakaona kanthu kena kamene Mulungu wakapanga. Chotero inu mumakhulupilira kuti kulidi Mulungu.

Munthu wina angakufunseni kuti, “Kodi ndani amene anapanga dzuwa ndi dziko lapansi?” Kodi inuyo mukanati chiani?—Inu mungathe kunena kuti Mulungu anazipanga izo. Baibulo limati: “Mulungu adalenga miyamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1, NW.

Bwanji ngati munthu wina akufunsani inu kuti, “Kodi Mulungu anapanganso munthu ndi zinyama?” Kodi mudzanena chiani?—Muuzeni kuti: “Inde, Mulungu anapanga munthu ndi zinyama. Mulungu anapanganso mbalame.” Baibulo limati: ‘Mulungu adalenga zinthu zonse.’—Aefeso 3:9, NW.

Munthu wina angakuuzeni kuti iye samakhulupilira Mulungu. Kodi nchiani chimene inuyo mudzachinena pamenepo? —Bwanji osasonya nyumba? Mfunseni munthuyo kuti: ‘Kodi ndani amene anaimanga nyumba imeneyo?” Munthu wina anaimanga. Nyumbayo sinadzimange yokha, kodi inatero?—

Pamenepo mutengereni munthuyo ku munda wamaluwa ndi kumsonyeza iye duwa. Mfunseni iye kuti: “Kodi ndani amene analipanga ili?” Palibe munthu ali yense amene analipanga. Popeza kuti nyumba sinadzipange yokha, duwa limeneli silinadzipange lokha. Wina wache analipanga ilo. Mulungu analipanga.

Mpempheni munthu kuti aime ndi kumvetsera nyimbo ya mbalame. Pamenepo mfunseni iye kuti: “Kodi ndani amene anazipanga mbalame ndi kuziphunzitsa izo kuyimba?” Mulungu anatero. Mulungu ali Uyo amene anapanga miyamba ndi dziko lapansi ndi zinthu zonse zamoyo! Iye ndiye Uyo amene amapereka moyo.

Ndipo ndi kwabwino chotani nanga kukhala wamoyo! Ife tingathe kuzimva nyimbo zokongola za mbalame. Ife tingathe kuona maluwa ndi zinthu zina zimene Mulungu wazipanga. Ndipo ife tingathe kudya zakudya zimene Mulungu watipatsa.

Ife tiyenera kumthokoza Mulungu kaamba ka zinthu zonse zimenezi. Choposa mwa zonse, ife tiyenera kumthokoza iye kaamba ka kutipatsa ife moyo. Ngati ife tiridi othokoza kwa Mulungu, ife tidzachita kanthu kena. Kodi kameneko nchiani?—Ife tidzamumvetsera Mulungu ndipo ife tidzamlambira iye m’njira imene iye amatiuzira ife kumlambira nayo m’Baibulo. M’njira imeneyo ife tingathe kusonyeza kuti ife timamkonda Uyo amene anapanga zinthu zonse.

(Ife tiyenera kusonyeza chiyamikiro kwa Mulungu kaamba ka zonse zimene iye wazichita. Motani? Werengani chimene chalembedwa pa Salmo 139:14 [138:13, MO], Chibvumbulutso 4:11, Yohane 4:23, 24 ndi 1 Yohane 5:21.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena