Zamkatimu
August 2013
© 2013 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Ulamuliro wonse pa magazini ino n’ngwathu.
MUNGAPEZE ZAMBIRI PA WEBUSAITI YA
ACHINYAMATA
ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
N’Chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza Mwadala?
Mtsikana wina, dzina lake Jerrine, ananena kuti: “Nthawi zonse ndinkati ndikadzicheka mwadala, ndinkasokonezeka maganizo ndipo ndinkaganiza kuti imeneyi ndi njira yabwino yothanirana ndi mavuto anga.” Vuto limeneli ndi lofala kwambiri kwa achinyamata. Koma n’chifukwa chiyani amadzivulaza? Kodi amachita zimenezi potengera anzawo? Kodi mungatani ngati inunso muli ndi vuto limeneli?
(Fufuzani pa mawu akuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACHINYAMATA)
ANA
Werengani nkhani zomwe zafotokozedwa pogwiritsa ntchito zithunzi. Gwiritsani ntchito nkhanizi kuthandizira ana anu kudziwa zambiri za anthu otchulidwa m’Baibulo komanso kuwathandiza kuti akhale ndi makhalidwe abwino.
(Fufuzani pa mawu akuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANA)