Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 10/13 tsamba 3
  • Zochitika Padzikoli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zochitika Padzikoli
  • Galamukani!—2013
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Italy
  • Armenia
  • Japan
  • China
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2012
  • Lipoti la Milandu
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova 2014
  • Mmene Mungachitire ndi Mavuto a Kuchuluka kwa Magalimoto Pamsewu
    Galamukani!—2007
  • Lipoti la Milandu
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
Onani Zambiri
Galamukani!—2013
g 10/13 tsamba 3

ZOCHITIKA PADZIKOLI

Italy

[Chithunzi patsamba 3]

Mu 2011, njinga zinkagulitsidwa kwambiri kuposa magalimoto ku Italy. Anthu ambiri akumagula njinga chifukwa cha mavuto azachuma, kukwera mtengo kwa mafuta komanso chifukwa chakuti kukonzetsa galimoto n’kodula. Koma njinga siimafuna ndalama zambiri pokonzetsa, siivuta kugwiritsa ntchito ndiponso ungapite nayo kulikonse.

Armenia

[Chithunzi patsamba 3]

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya lagamula kuti boma la Armenia linaphwanya ufulu wa anyamata 17 a Mboni za Yehova chifukwa chowamanga atakana kulowa ntchito zokhudzana ndi usilikali. Bomali likuyenera kuwalipira ndalama chifukwa chowawonongera mbiri komanso liyenera kulipira ndalama zonse zimene anyamatawo anawononga pa mlanduwu.

Japan

[Chithunzi patsamba 3]

Pa ana 100 alionse amene anachitidwa chipongwe pogwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti, ana 63 anali asanachenjezedwepo ndi makolo awo kuti malowa ndi oopsa. Kuti apeze zimenezi anaunika milandu yokwana 599. Anthu 74 pa 100 alionse amene ankaimbidwa mlanduwu anavomereza kuti cholinga chawo pogwiritsa ntchito malowa chinali choti azigona ana.

China

[Chithunzi patsamba 3]

Pofuna kuchepetsa kuchuluka kwa magalimoto m’misewu, maofesi a boma a m’mizinda ikuluikulu achepetsa nambala ya ziphaso zatsopano za magalimoto. Mwachitsanzo, ku Beijing azipereka ziphaso zatsopano zosapitirira 240,000 pa chaka. Mu August 2012, anthu pafupifupi 1,050,000 anachita maere kuti apatsidwe ziphaso ndipo anthu 19,926 ndi amene anapatsidwa ziphasozo. Zimenezi zikutanthauza kuti munthu mmodzi yekha pa anthu 53 ndi amene anapatsidwa chiphaso.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena