Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 4/14 tsamba 7
  • 1 Zinthu Zimasintha pa Moyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 1 Zinthu Zimasintha pa Moyo
  • Galamukani!—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Bwanji Ndingodzipha?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • 4 | Muziteteza Chiyembekezo Chanu
    Galamukani!—2022
  • Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Zimene Mungachite Zinthu Zikasintha
    Galamukani!—2016
Onani Zambiri
Galamukani!—2014
g 4/14 tsamba 7

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUDZIPHA NDI NJIRA YABWINO YOTHETSERA MAVUTO?

1 Zinthu Zimasintha pa Moyo

“Timapanikizidwa mwamtundu uliwonse, koma osati kupsinjidwa moti n’kulephera kusuntha. Timathedwa nzeru, koma osati mochita kusoweratu pothawira.”—2 AKORINTO 4:8.

Kudzipha kuli ngati kuwotcha nyumba chifukwa choti m’nyumbamo muli makoswe, m’malo mongopha makoswewo. Ngakhale munthu atakumana ndi mavuto aakulu ooneka ngati sangathe, m’kupita kwa nthawi akhoza kutha. Ndipotu zinthu zikhoza kusintha n’kuyamba kuyenda bwino.—Onani bokosi lakuti “Zinthu Zinasintha pa Moyo Wawo.”

Ngakhale zitakhala kuti zinthu sizingasinthe pa moyo wanu, ndi bwino kumathana ndi mavuto amene mukukumana nawo panopa, m’malo momada nkhawa ndi mavuto amene angabwere m’tsogolo. Yesu ananena kuti: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”—Mateyu 6:34.

Nanga kodi mungatani zitakhala kuti vuto lanu ndi loti silingathe? Mwachitsanzo, mwina muli ndi matenda okhalitsa. Kapenanso mukuvutika maganizo chifukwa cha zinthu zoti sizingasinthe, monga kutha kwa ukwati kapena imfa ya munthu amene munkamukonda?

Dziwani kuti ngakhale pa zochitika zoterezi, mungathebe kusintha zinazake. Mungasinthe mmene mukuonera nkhaniyo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muyambe kuona zinthu moyenera. (Miyambo 15:15) Zingakuthandizeninso kuti mupirire vuto lanulo m’malo momaganiza zoti ndi bwino kungofa. Zotsatira zake zingakhale zoti ngakhale kuti simungathetse vutolo, mungayambe kuliona moyenera.—Yobu 2:10.

MFUNDO YOYENERA KUIKUMBUKIRA: Simungathe kukwera phiri mwa kungoyenda sitepe imodzi yokha, koma mutayenda masitepe ambirimbiri mungapezeke muli pamwamba pa phirilo. N’chimodzimodzinso ndi mavuto anu amene mwina mungamawaone kuti ndi aakulu ngati phiri. Muyenera kumathana nawo pang’onopang’ono.

ZIMENE MUYENERA KUCHITA PANOPA: Uzani mnzanu kapena wachibale za vuto lanulo. Munthu ameneyo angakuthandizeni kuti muyambe kuona vutolo moyenera.—Miyambo 11:14.

ZINTHU ZINASINTHA PA MOYO WAWO

Taganizirani za anthu 4 okhulupirika otchulidwa m’Baibulo amene anakumana ndi mavuto pa moyo wawo moti sankafunanso kukhala ndi moyo.

  • Rabeka: “Ngati umu ndi mmene ndivutikire, ndiye ndi bwino ndingofa.”—Genesis 25:22.

  • Mose: “Chonde, ingondiphani kuti tsokali lindichoke.”—Numeri 11:15.

  • Eliya: “Chotsani moyo wanga . . . pakuti sindine woposa makolo anga.”—1 Mafumu 19:4.

  • Yobu: “Bwanji sindinamwalire nditangotuluka m’mimba?”—Yobu 3:11.

Mukawerenga nkhani za anthu amenewa, muona kuti kenako zinthu pa moyo wawo zinasintha n’kuyamba kuyenda bwino, ngakhale kuti izi si zimene iwo ankayembekezera. Zoterezi zikhoza kukuchitikiraninso inuyo. (Mlaliki 11:6) Choncho musataye mtima.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena