Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 1/15 tsamba 6
  • Baibulo Lili Ndi Mayankho Ogwira Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Baibulo Lili Ndi Mayankho Ogwira Mtima
  • Galamukani!—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Moyo Unayamba Bwanji?
    Nkhani Zina
  • “Chokumana Nacho Cholemekezeka Kwenikweni”
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Mayankho Mungawapeze Kuti?
    Galamukani!—2004
  • Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Kuti Dziko Linalengedwa M’masiku 6 Enieni?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
Onani Zambiri
Galamukani!—2015
g 1/15 tsamba 6
Baibulo lotsegula

PACHIKUTO | KODI MOYO UNAYAMBA BWANJI?

Baibulo Lili Ndi Mayankho Ogwira Mtima

ANTHU ambiri akaganizira umboni womwe ulipo amaona kuti payenera kukhala winawake wanzeru amene analenga zonse. Pulofesa wina dzina lake Antony Flew, poyamba ankalimbikitsa chikhulupiriro choti kulibe Mulungu. Kenako anaphunzira zinthu zochititsa chidwi zokhudza moyo komanso kuti zinthu zakuthambo zimayenda motsatira malamulo enaake. Zimenezi zinapangitsa kuti asinthe maganizo ake. Flew analemba mfundo yomwe akatswiri akale anzeru za anthu ankaikhulupirira. Iye anati: “Tiyenera kuvomereza zotsatira za kafukufuku ngakhale zitakhala kuti n’zosiyana ndi zomwe timayembekezera.” Pulofesayu anaona kuti kafukufuku amasonyeza kuti pali winawake wanzeru amene analenga zinthu zonse.

Gerard, yemwe tamutchula m’nkhani yoyamba ija, nayenso anayamba kukhulupirira zimenezi. Iye anati: “Ndimaona kuti palibe umboni wokhutiritsa wosonyeza kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Zamoyo zimachita zinthu mwadongosolo komanso mogometsa kwambiri. Payenera kuti pali winawake amene anazilenga chifukwa zimenezi sizingangochitika zokha.”

Munthu akhoza kudziwa zambiri za katswiri wojambula zithunzi poona zimene katswiriyo anajambula. Nayenso Gerard anayamba kudziwa makhalidwe amene Mulungu ali nawo poona zimene Mulunguyo analenga. Anaphunziranso zambiri za Mulungu kudzera m’Mawu ake, Baibulo. (2 Timoteyo 3:16) Zinthu zina zimene anaphunzira m’Baibulo ndi mfundo zomveka bwino zonena za anthu oyambirira komanso zimene munthu angachite ngati akukumana ndi mavuto. Zimenezi zinamupangitsa kutsimikizira kuti Baibulo ndi Mawudi a Mulungu.

M’Baibulo muli mayankho ogwira mtima a mafunso osiyanasiyana. Tikukulimbikitsani kuti inunso muliphunzire ndipo mudzapeza mayankho a mafunso osiyanasiyana omwe muli nawo.

Kodi Mukudziwa?

BAIBULO SILITSUTSANA NDI MFUNDO ZOLONDOLA ZASAYANSI. Baibulo limalimbikitsa anthu kuti aziphunzira zambiri zokhudza Mlengi kudzera m’chilengedwe. (Yesaya 40:26) Ngakhale kuti Baibulo si buku la sayansi, zimene limanena pa nkhani ya sayansi, zimakhala zolondola. Mwachitsanzo, Baibulo silimanena kuti dzikoli linalengedwa masiku 6 enieni a maola 24. Mawu omwe ali m’buku la Genesis omwe anamasuliridwa kuti “tsiku,” angatanthauze nthawi yaitali ndithu.a

a Kuti mudziwe zambiri, werengani kabuku kachingelezi kakuti, Was Life Created? kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Kabukuka kakupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org/ny.

Baibulo Limaphunzitsa Kuti . . .

ZAMOYO ZINACHITA KULENGEDWA. “Pakuti inu [Mulungu] ndinu kasupe wa moyo.”—Salimo 36:9.

MULUNGU ANALENGA ZOMERA KOMANSO NYAMA “MONGA MWA MITUNDU YAKE.” (Genesis 1:11, 12, 21, 24, 25) Zimene Baibulo limanenazi zikusonyeza kuti mitundu ya zomera komanso ya nyama, m’kupita kwa nthawi ingatulutse zinthu zina koma zosasiyana kwenikweni ndi zoyambazo.

MULUNGU ANALENGA ANTHU M’NJIRA YOTI AZITHA KUSONYEZA MAKHALIDWE ABWINO AMENE IYEYO ALI NAWO. Makhalidwe ake ndi monga chikondi, ubwino komanso chilungamo. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti Mulungu analenga anthu ‘m’chifaniziro chake, kuti akhale ofanana naye.’—Genesis 1:26.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena