“Chokumana Nacho Cholemekezeka Kwenikweni”
MKATI mwachirimwe mu 1984, Gerard, mwamuna wachichepere wochokera ku France, ananyamuka paulendo wa miyezi isanu ndi umodzi—ulendo wa panjinga kuzungulira United States ndi Canada. Mapiri aakulu a Rocky Mountains anamusangalatsa iye, mapaki amtendere anamudekhetsa mtima iye, koma chochitika chomwe anawona pa Montmagny, Quebec, Canada, chinamusangalatsa iye koposa; chinasintha njira yake yonse yamoyo.
Pa Sande, September 16, Gerard anali kutchova njinga kuzunguiira Mongtmagny pamene iye anawona mzera wautali wa magalimoto ataimikidwa m’mphepete mwamsewu. Kenaka, iye anawona mazana a anthu akuimirira mozungulira malo omangapo nyumba. “Kodi nchiyani chimene chikuchitika pano?” lye anafunsa mmodzi wa ogwira ntchito amene anali kutsogolera magalimoto. Ngakhale kuti munthuyo anali wotanganitsidwa, iye anatenga nthawi kumlongosolera Gerard kuti anthu onse amene anali kugwira ntchito anali Mboni za Yehova kugwiritsira ntchito masiku awo akutha kwa mlungu kumanga nyumba kaamba ka misonkhano yawo ya chipembedzo. Mosadziwika kwa Gerard, iye anali atafika mkati mwa maora omalizira ofulumira a projekiti ya masiku awiri a Nyumba ya Ufumu. lye anasangalatsidwa ndi zonse zimene anawona ndi kumva. Usiku umenewo iye analemba mukabukhu kake kolembamo zochitika za pa tsiku: “Madzulo ndinakumana ndi Mboni za Yehova. Izo zamanga nyumba m’masiku awiri. Zinalipo zoposa 1, 000 za izo. Chokumana nacho cholemekezeka kwambiri.”
Pambuyo pake Gerard anabwerera ku France. Zaka ziwiri pambuyo pake, pa July 26, 1986, iye anatumiza kalata ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova mu Montmagny. Iye analemba:
’Kodi mumakumbukirabe kulankhula kwa woyendetsa njinga wochokera ku France mkati mwa tsiku lachiwiri la projekiti yanu yakumanga Nyumba ya Ufumu? Tsiku limene lija wolamulira magalimoto anafesa mbewu. Miyezi ina pambuyo pake Mboni zinandichezera ine mu France, ndipo ndinalandira choperekachawo cha kuphunzira Baibulo ndi iwo. Popeza ndiri wochokera ku banja lokhulupirika la Chikatolika, phunzirolo silinali lokhweka. Koma Yehova anapangitsa mbewuyo kukula. Milungu iwiri yapitayo ndinabatizidwa pa msonkhano mu Nantes. Ndikuyamikira Yehova kaamba ka kundilola ine kupeza chowonadi, ndipo ndili woyamikira kaamba ka zonse zimene mbaleyo anandiphunzitsa ine Sande limenelo, September 16, 1984. Moni waubale kuchokera kwa wofufuza yemwe anatembenukira ku chowonandi.
Ndi chimwemwe chotani nanga chimene mpingo wa Montmagny unamva pambuyo pakumva kalata ya Gerard ikuwerengedwa mu Nyumba yawo ya Ufumu! Awo onse amene anathandiza m’kumanga holoyo anakumana ndi chowonadi cha mawu a Solomo: “Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri. (Mlaliki 11:1) Inde, zotulukapo zabwino za maprojekiti a Nyumba za Ufumu ziri zosatha ndi zofika patali m’njira zambiri.