Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 5/15 tsamba 8-9
  • Kuphunzitsa Ana Kuti Azikumverani

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuphunzitsa Ana Kuti Azikumverani
  • Galamukani!—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • VUTO LIMENE LIMAKHALAPO
  • Kodi Malangizo Abwino Olerera Ana Mungawapeze Kuti?
    Galamukani!—2015
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Mmene Mungatetezere Ana Anu
    Galamukani!—2007
  • Zimene Mungachite Mwana Akayamba Kuvuta
    Galamukani!—2013
Onani Zambiri
Galamukani!—2015
g 5/15 tsamba 8-9
Kamnyamata komwe sikakufuna kumvera mayi ake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Mungaphunzitse Bwanji Mwana Wanu Kuti Azikumverani?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Tiyerekezere kuti nthawi zonse inuyo ndi mwana wanu wazaka 4 simugwirizana. Mukamuuza kuti achite zinazake, amakana ndipo nthawi zambiri inuyo mumangochita zofuna za mwanayo.

  • Mukamuuza kuti achite zinthu zina zimene sakufuna, sakuyankhani ndipo amangokhala ngati sanamve.

  • Mukamuletsa kuchita zinazake, amayamba kuvuta.

Mumadabwa ndi zimene amachitazi ndipo mumadzifunsa kuti, ‘Kodi akuchita zimenezi chifukwa choti ndi mwana, akadzakula adzasiya?’

Ngakhale zimaoneka kuti n’zovuta, mungathe kuphunzitsa mwana wanu kuti azikumverani. Koma tisanakambirane zimene mungachite, tiyeni tione zimene zimachititsa kuti mwana wanu asamakumvereni.

ZIMENE ZIMACHITITSA

Mwana wanu atangobadwa, munkafunika kumusamalira pa chilichonse. Akangolira, nthawi yomweyo munkathamanga kuti mukaone kuti akulira chiyani ndipo munkamuchitira chilichonse chimene akufuna. Kuchita zimenezi kulibe vuto lililonse chifukwa ndi udindo wa kholo kusamalira mwana wake.

Popeza mwana akakhala wamng’ono makolo amamuchitira chilichonse, mwanayo amazolowera zimenezi ndipo amayamba kuona kuti ndi wofunika kwambiri kuposa aliyense. Koma akamakwanitsa zaka ziwiri, amaona kuti zinthu zayamba kusintha. Amaona kuti makolo ake sakumuchitiranso zinthu zina zimene akufuna. Amaonanso kuti iyeyo akufunikira kumvera makolo akewo. Ana ambiri zimawavuta kuvomereza zimenezi, choncho amayamba kuvuta. Pomwe ena amakana dala kuchita zimene makolo awo awauza kuti aone zomwe makolowo angachite.

Imeneyi ndi nthawi yomwe muyenera kusintha mmene mumachitira zinthu ndi mwanayo. Mufunika kumuthandiza kuzindikira kuti inuyo ndi amene muyenera kumamuuza zochita. Nanga bwanji ngati mwana wanu safuna kuti muzimuuza zochita ngati mmene zilili m’chitsanzo chili kumanzerechi?

ZIMENE MUNGACHITE

Muzimuuza zochita. Mwana wanuyo sangakhale womvera ngati nthawi zonse mumangochita zimene iyeyo akufuna. Mwanayo ayenera kudziwa kuti monga makolo ake, muli ndi udindo womuuza zochita ndipo iyeyo ayenera kumakumverani. Koma m’zaka zapitazi, akatswiri ena opereka malangizo olerera ana ankapangitsa anthu kuganiza kuti kulera ana m’njira imeneyi ndi nkhanza. Ndipo katswiri wina ananena kuti makolo amene amachita zimenezi, ali ndi “khalidwe loipa” ndipo akuchita “zosemphana ndi chikhalidwe.” Komabe makolo akamangolekerera ana kuti azichita zimene akufuna, anawo sadziwa zoyenera kuchita, amaona ngati akhoza kuchita chilichonse komanso amadziona ngati ndi ofunika kwambiri. Izi zimachititsa kuti anawo akadzakula azidzalephera kuchita zinthu ngati anthu aakulu.—Lemba lothandiza: Miyambo 29:15.

Muzimupatsa chilango. Buku lina lotanthauzira mawu linanena kuti chilango chimathandiza munthu kukhala womvera komanso wodziletsa. Koma zimenezi sizitanthauza kuti muyenera kulanga mwana wanu mwankhanza. Cholinga chanu polanga mwanayo chizikhala kumuthandiza kuti asinthe.—Lemba lothandiza: Miyambo 23:13.

Muzimuuza momveka bwino zimene mukufuna kuti achite. Makolo ena akafuna kuti mwana wawo achite zinazake, amachita kumupempha. Mwachitsanzo anganene kuti: “Kodi ungaseseko pakhondepo?” Angachite zimenezi pofuna kum’phunzitsa mwanayo kulankhula mwaulemu. Koma kuchita zimenezi kungapangitse mwanayo kuganiza kuti ali ndi ufulu wosankha kuchita kapena kusachita zimene makolo ake amupempha. Choncho m’malo momupempha, muyenera kumuuza momveka bwino zimene akuyenera kuchita.—Lemba lothandiza: 1 Akorinto 14:9.

Musamasinthesinthe. Mukamuletsa mwana wanu kuti asachite chinachake, musamasinthe maganizo. Ngati mwamuna kapena mkazi wanu waletsa mwana kuchita zinazake, inuyo muyenera kugwirizana nazo. Ndiponso ngati mwamuuza kuti akapanda kumvera alandira chilango chinachake, muyenera kumupatsadi chilangocho. Mukamuuza kuti achite zinazake, palibe chifukwa choti muyambe mwakambirana naye kapena kumuuza chifukwa chake. Zingakhale zosavuta kuti azikumverani ngati nthawi zonse, ‘mukati Inde amakhaladi Inde ndipo mukati Ayi amakhaladi Ayi.’—Yakobo 5:12.

Muzichita zinthu mwachikondi. Simuyenera kuchitira nkhanza ana anu. Komabe si bwinonso kumangowalekerera. Mulungu amafuna kuti makolo azilera mwachikondi ana awo kuti akule bwino. Kuti zimenezi zitheke, muyenera kumalangiza mwana wanu kapena kum’patsa chilango choyenera. Zimenezi zingathandize mwanayo kuti azikumverani komanso kuti adziwe zoti mumamukonda.

MALEMBA OMWE MUNGAGWIRITSE NTCHITO

  • “Mwana womulekerera adzachititsa manyazi mayi ake.”—Miyambo 29:15.

  • “Usam’mane chilango mwana.”—Miyambo 23:13.

  • “Ngati simukulankhula zomveka ndi lilime lanu, zingatheke bwanji kudziwa zimene mukunena?”—1 Akorinto 14:9.

KUTI MUDZIWE ZAMBIRI

Mfundo zina za m’Baibulo zomwe zingathandize makolo kulera bwino ana awo, mungazipeze pa webusaiti yathu ya jw.org/ny. Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANTHU APABANJA NDIPONSO MAKOLO. Pamenepo mungapezepo nkhani zotsatirazi ndi zina zambiri:

  • “Zimene Mungachite Mwana Akayamba Kuvuta”

  • “Kodi Mungatani Kuti Musamangopatsa Mwana Wanu Chilichonse Chimene Akufuna?”

  • “Zimene Mungachite Ngati Mwana Wanu Amanama”

  • “Zimene Mungachite Kuti Mwana Wanu Azikumverani”

Onaninso nkhani ya pachikuto yakuti, “N’chifukwa Chiyani Ana a Masiku Ano Safuna Kuuzidwa Zochita?” m’magazini ya Galamukani! ya April 2015.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena