Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 7/13 tsamba 4-5
  • Zimene Mungachite Mwana Akayamba Kuvuta

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mungachite Mwana Akayamba Kuvuta
  • Galamukani!—2013
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • VUTO LIMENE LIMAKHALAPO
  • Kuphunzitsa Ana Kuti Azikumverani
    Galamukani!—2015
  • Ubongo wa Mwana Umaphunzira Zinthu Mogometsa Kwambiri
    Galamukani!—2011
  • Kudziletsa N’kofunika Kwambiri
    Galamukani!—2019
  • Mmene Mungatetezere Ana Anu
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Galamukani!—2013
g 7/13 tsamba 4-5
[Chithunzi patsamba 4]

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Zimene Mungachite Mwana Akayamba Kuvuta

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

[Chithunzi patsamba 4]

Mwana wanu wa zaka ziwiri akakwiya amayamba kulira kwambiri, kudziponya pansi komanso kutaya zinthu. Mwina mumadzifunsa kuti: ‘Koma mwana wangayu ndi wabwinobwino? Kodi akuvuta chifukwa chakuti sindikumulera bwino? Kodi adzasiya kuvuta?’

N’zotheka kuthandiza mwana wanu kusiya kuvuta. Komano choyamba, tiyeni tione chimene chimapangitsa kuti mwana ayambe kuvuta.

CHIMENE CHIMACHITITSA

Ana aang’ono sadziwa zimene angachite akakhumudwa. Zimenezi zingapangitse kuti nthawi zina azivuta. Komanso pali zifukwa zina.

Mwana akafika zaka ziwiri zinthu zina zimasintha pamoyo wake. Atangobadwa munkamuchitira chilichonse. Mwachitsanzo, akangolira munkasiya chilichonse chomwe mumapanga n’kukamusamalira. Mwina munkadzifunsa kuti ‘Kodi akudwala? Ali ndi njala? Akufuna kumunyamula? Kapena ndimusinthe thewera?’ Munkayesetsa kuchita chilichonse kuti asiye kulira ndipo simunkalakwitsa kuchita zimenezi chifukwa mwana wamng’ono amadalira makolo ake nthawi zonse.

Koma akafika zaka ziwiri, mwana amayamba kuzindikira kuti makolo ake sakumusamaliranso kwambiri ngati mmene ankachitira poyamba. Amaona kuti m’malo moti makolo azichita zimene iyeyo akufuna, makolowo amafuna kuti iyeyo azichita zimene iwowo akufuna. Mwanayo sangasangalale ndi kusintha kumeneku choncho angayambe kuvuta posonyeza kukwiya.

N’kupita kwa nthawi, mwanayo amazindikira kuti makolo ake ali ndi udindo womupatsa malangizo osati kungomusamalira. Komanso amazindikira kuti iyeyo monga mwana ayenera ‘kumvera makolo.’ (Akolose 3:20) Komabe nthawi imeneyi isanafike, mwanayo angamavute kwambiri ndipo zimenezi zingamasowetse mtendere makolowo.

ZIMENE MUNGACHITE

Muzimumvetsa. Muzikumbukira kuti mwana ndi mwana. Chifukwa chakuti sadziwa zimene angachite akakhumudwa, nthawi zina amangoyamba kuvuta. Choncho, muziyerekeza kuti zimene zikumuchitikirazo zikukuchitikirani inuyo.—Lemba lothandiza: 1 Akorinto 13:11.

Musamafulumire kupsa mtima. Mwana wanu akayamba kuvuta, musamafulumire kupsa mtima. Muzingoona kuti chamuchititsa kuyamba kuvuta n’chiyani. Kudziwa chifukwa chimene chachititsa mwanayo kuti ayambe kuvuta kungathandize kuti musamupsere mtima.—Lemba lothandiza: Miyambo 19:11.

Musamangomuchitira zimene akufuna. Mukamangopatsa mwana wanu chilichonse chomwe akufuna n’cholinga choti asiye kuvuta, ndiye kuti nthawi zonse azingovuta akafuna chinthu. Muzimuuza modekha kuti simusintha zimene mwanena.—Lemba lothandiza: Mateyu 5:37.

Kudziwa chifukwa chimene chachititsa mwanayo kuti ayambe kuvuta kungathandize kuti musamupsere mtima

Muzileza mtima. Musamaganize kuti mwana wanu angangosiya kuvuta lero ndi lero, makamaka ngati mumamuchitira zimene akufuna akayamba kuvuta. Choncho, mukamapewa kupsa mtima kapena kumangochitira mwana wanu zimene akufuna akayamba kuvuta, pang’ono ndi pang’ono amasiya kuvuta. Baibulo limanena kuti: “Chikondi n’choleza mtima.”—1 Akorinto 13:4.

Mwina mukhoza kuchitanso zotsatirazi:

  • Mwana wanu akayamba kuvuta muzimunyamula kuti asafulukutefulukute, koma musampane. M’malo momukalipira muzingodikira kuti mtima wake ukhale pansi. Pamapeto pake, mwanayo amazindikira kuti kuvuta sikungamuthandize chilichonse.

  • Pezani malo amene mungamuike kapena kumutsekera akayamba kuvuta. Muzimusiya konko ndipo muzimutulutsa akasiya kuvuta.

  • Ngati mwana wanu wayamba kuvuta muli pagulu, pitani naye pambali. Musamupatse zimene akufunazo chifukwa chakuti pali anthu. Ngati mutamupatsa angayambe kuganiza kuti ngati atayamba kuvuta, muzimupatsa chilichonse chomwe akufuna.

MALEMBA OMWE MUNGAGWIRITSE NTCHITO

  • “Pamene ndinali kamwana, ndinali kulankhula ngati kamwana.”—1 Akorinto 13:11.

  • “Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake.”—Miyambo 19:11.

  • “Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.”—Mateyu 5:37.

MUSAMASINTHESINTHE

“Ndimaseka mumtima ndikamva makolo ena akudandaula kuti mwana wawo samva akamuletsa chinachake. Zimandiseketsa chifukwa mawu amenewa amasonyeza kuti makolowo ndi amene ali ndi vuto. Kawirikawiri ngati mwana sakumva, zimakhala kuti makolo ake amalephera kumuletsa bwinobwino zinthu zina. Ngati mwana sakumvera zikhoza kukhala kuti makolowo samachitadi zimene amanena.”—Anatero John Rosemond, yemwe analemba buku lakuti New Parent Power!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena